Publicidade

Aceitar Jesus

Por Bíblia Online

Aceitar Jesus é a decisão mais importante da vida. Quem o recebe como Senhor e Salvador recebe vida eterna, perdão completo e a presença permanente do Espírito Santo.

Koma kwa onse amene anamulandira Iye, kwa amene anakhulupirira mʼdzina lake, Iye anawapatsa mphamvu yokhala ana a Mulungu;

"Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi, kotero anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira Iye asatayike koma akhale ndi moyo wosatha.

Yesu anayankha kuti, "Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate popanda kudzera mwa Ine.

kuti ngati udzavomereza ndi pakamwa pako kuti, "Yesu ndiye Ambuye," ndi kukhulupirira mu mtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka.

Pakuti malipiro a tchimo ndi imfa, koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.

Ndipo aliyense amene adzayitana

pa dzina la Ambuye adzapulumuka.

Petro anawayankha kuti, "Lapani ndipo mubatizidwe aliyense wa inu, mʼdzina la Yesu Khristu kuti machimo anu akhululukidwe. Ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.

Chipulumutso sichipezeka mwa wina aliyense; pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo limene lapatsidwa kwa anthu limene tiyenera kupulumutsidwa nalo."

Iwo anayankha kuti, "Khulupirira Ambuye Yesu ndipo udzapulumuka, iwe ndi a mʼbanja lako."

Koma tikavomereza machimo athu, Iye ndi wokhulupirika ndi wolungama ndipo adzatikhululukira machimo athu, nadzatiyeretsa ndi kutichotsera chosalungama chilichonse.

Taonani ndayima pa khomo ndikugogoda. Ngati wina amva mawu anga natsekula chitseko, Ine ndidzalowamo ndi kudya naye, Ine ndi iyeyo.

Seja o primeiro
Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-29_22-07-56-