Admiração
O temor do Senhor é o princípio da sabedoria. A admiração reverente por Deus é a postura que produz conhecimento, obediência e bênção na vida do crente.
Kuopa Yehova ndiye chiyambi cha nzeru.
Zitsiru zimanyoza nzeru ndi malangizo.
Kuopa Yehova ndiye chiyambi cha nzeru;
kudziwa Woyerayo ndiko kukhala womvetsa bwino zinthu.
Kuopa Yehova kumaphunzitsa munthu nzeru,
ndipo kudzichepetsa ndi ulemu chili patsogolo ndi kudzichepetsa.
Kuli bwino kukhala ndi zinthu pangʼono nʼkumaopa Yehova,
kusiyana ndi kukhala ndi chuma chambiri uli pamavuto.
Kuopa Yehova ndiko kudana ndi zoyipa.
Ine ndimadana ndi kunyada, kudzitama,
kuchita zoyipa, ndiponso kuyankhula zonyenga.
Mphotho ya munthu wodzichepetsa
ndi woopa Yehova ndi chuma, ulemu ndi moyo.
Usamadzione ngati wa nzeru.
Uziopa Yehova ndi kupewa zoyipa.
Ukatero thupi lako lidzakhala la moyo wabwino
ndi mafupa ako adzakhala olimba.
Nkhope yachikoka ndi yonyenga, ndipo kukongola nʼkosakhalitsa;
koma mkazi amene amaopa Yehova ayenera kutamandidwa.
Basi zonse zamveka; mathero a nkhaniyi ndi awa:
uziopa Mulungu ndi kusunga malamulo ake,
pakuti umenewu ndiwo udindo
wa anthu onse.
Kuopa Yehova ndicho chiyambi cha nzeru;
onse amene amatsatira malangizo ake amamvetsa bwino zinthu.
Iye ndi wotamandika mpaka muyaya.
Tamandani Yehova.
Wodala munthu amene amaopa Yehova,
amene amakondwera kwambiri ndi malamulo ake.
Odala ndi onse amene amaopa Yehova,
amene amayenda mʼnjira zake.
Koma maso a Yehova ali pa iwo amene amaopa Iye;
amene chiyembekezo chawo chili mʼchikondi chake chosatha,
Mulungu atidalitse
kuti pamenepo malekezero onse a dziko lapansi apembedze Iyeyo.
Koma inu amene mumaopa dzina langa, dzuwa lachilungamo lidzakutulukirani lili ndi kuwala kokuchiritsani. Ndipo inu mudzatuluka ndi kulumphalumpha ngati ana angʼombe amene atulutsidwa mʼkhola.
Tsopano inu Aisraeli, nʼchiyani chimene Yehova afuna kwa inu? Iye akufuna kuti muzimuopa poyenda mʼnjira zake zonse ndi kumamukonda Iye, kumutumikira Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, ndi kusunga malamulo ndi malangizo amene ndikukupatsani lero kuti zizikuyenderani bwino.
Muyenera kutsatira Yehova Mulungu wanu, ndipo ndi Iyeyo amene muyenera kumuopa. Muzisunga malamulo ake ndi kumamumvera, muzimutumikira ndipo kumukangamira Iyeyo.
Pakuti azambawo ankaopa Mulungu, Iye anawapatsa mabanja awoawo.
Abwenzi okondedwa, popeza tili ndi malonjezo amenewa, tiyeni tidziyeretse, kusiyana nazo zilizonse zimene zikhoza kudetsa thupi ndi mzimu, ndipo tiyesetse kukhala oyera mtima poopa Mulungu.
Mubwezereni aliyense amene munamukongola. Ngati inu muli ndi ngongole yamsonkho, perekani msonkho kwa oyenera kuwalipira. Ngati ndi kuopa perekeni kwa oyenera kuwaopa ndipo ngati ndi ulemu kwa oyenera ulemu.
"Munthu amene ali kakasi ayenera kukhala ndi abwenzi odzipereka,
ngakhale kuti iyeyo wasiya kuopa Wamphamvuzonse.