Pular para o conteúdo
Publicidade

Adoração

Por Bíblia Online

A adoração é a resposta do coração humano à majestade de Deus. Deus é Espírito e importa que os que o adoram o adorem em espírito e em verdade — com todo o ser.

Adorar em espírito

Deus é Espírito e importa que os adoradores o adorem em espírito e em verdade. A adoração verdadeira brota do coração.

Mulungu ndi Mzimu, ndipo omupembedza Iye ayenera kumupembedza mu mzimu ndi mʼchoonadi."

Koma nthawi ikubwera ndipo yafika kale tsopano pamene opembedza woona adzapembedza Atate mu mzimu ndi mʼchoonadi, pakuti opembedza otere ndiwo amene Atate akuwafuna. Mulungu ndi Mzimu, ndipo omupembedza Iye ayenera kumupembedza mu mzimu ndi mʼchoonadi."

Yesu anati, "Mayi inu khulupirira Ine. Nthawi ikubwera pamene inu simudzapembedza Atate mʼphiri ili kapena mu Yerusalemu. Inu Asamariya mumapembedza chimene simukuchidziwa. Ife timapembedza chimene tikuchidziwa, pakuti chipulumutso nʼchochokera kwa Ayuda. Koma nthawi ikubwera ndipo yafika kale tsopano pamene opembedza woona adzapembedza Atate mu mzimu ndi mʼchoonadi, pakuti opembedza otere ndiwo amene Atate akuwafuna.

Pamenepo munthuyo anati, "Ambuye, ndikukhulupirira," ndipo anamulambira Iye.

Yesu anati kwa iye, "Choka Satana! Zalembedwa, Pembedza Yehova Mulungu wako ndi kumutumikira Iye yekha.’ "

Yesu anayankha kuti, "Zalembedwa: Pembedza Yehova Mulungu wako ndi kumutumikira Iye yekha.’ "

Nsembe za Moyo

Nʼchifukwa chake ine ndikukupemphani abale, mwa chifundo cha Mulungu, kuti mupereke matupi anu monga nsembe yamoyo, yopatulika ndi yokondweretsa Mulungu. Nsembeyi ndiye kupembedza kwanu kwa uzimu.

Nsembe za Moyo

Nʼchifukwa chake ine ndikukupemphani abale, mwa chifundo cha Mulungu, kuti mupereke matupi anu monga nsembe yamoyo, yopatulika ndi yokondweretsa Mulungu. Nsembeyi ndiye kupembedza kwanu kwa uzimu. Musafanizidwenso ndi makhalidwe a dziko lino koma musandulike pokonzanso maganizo anu. Ndipo mudzadziwa ndi kuzindikira chifuniro chabwino cha Mulungu chomwe ndi chokondweretsa ndi changwiro.

Pakuti zinthu zonse nʼzochokera kwa Iye, nʼzolengedwa ndi Iye ndipo zimabweretsa ulemerero kwa Iye.

Kwa Iye kukhale ulemerero mpaka muyaya! Ameni.

Kwalembedwa, akutero Ambuye,

"Pamene Ine ndili ndi moyo,

aliyense adzandigwadira

ndipo lilime lililonse lidzavomereza Mulungu."

Louvor e reverência

Vinde, adoremos e prostremo-nos. Louvai ao Senhor! Todo ser que respira louve o nome glorioso do Senhor.

Bwerani, tiyeni tiwerame pomulambira,

tiyeni tigwade pamaso pa Yehova Mlengi wathu;

Bwerani, tiyeni tiwerame pomulambira,

tiyeni tigwade pamaso pa Yehova Mlengi wathu;

Tamandani Yehova.

Tamandani Mulungu mʼmalo ake opatulika;

mutamandeni ku thambo lake lamphamvu.

Mutamandeni chifukwa cha machitidwe ake amphamvu;

mutamandeni chifukwa cha ukulu wake wopambana.

Mutamandeni poyimba malipenga,

mutamandeni ndi pangwe ndi zeze.

Mutamandeni ndi matambolini ndi kuvina,

mutamandeni ndi zingwe ndi zitoliro.

Mutamandeni ndi ziwaya zolira za malipenga,

mutamandeni ndi ziwaya zolira kwambiri.

Chamoyo chilichonse chopuma chitamande Yehova.

Tamandani Yehova.

Chamoyo chilichonse chopuma chitamande Yehova.

Tamandani Yehova.

Lowani ku zipata zake ndi chiyamiko

ndi ku mabwalo ake ndi matamando;

muyamikeni ndi kutamanda dzina lake.

Perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake,

pembedzani Yehova mwa kukongola kwa chiyero chake.

Fuwulani kwa Mulungu ndi chimwemwe, dziko lonse lapansi!

Imbani ulemerero wa dzina lake;

kumutamanda kwake kukhale kwaulemerero.

Nenani kwa Mulungu, "Ntchito zanu ndi zoopsa ndithu!

Mphamvu yanu ndi yayikulu kwambiri

kotero kuti adani anu amawerama pamaso panu.

Dziko lonse lapansi limaweramira inu;

limayimba matamando kwa Inu;

limayimba matamando pa dzina lanu."

Sela.

Ndinafuwula kwa Iye ndi pakamwa panga,

matamando ake anali pa lilime panga.

Mitundu yonse ya anthu imene munayipanga

idzabwera ndi kudzalambira pamaso panu Ambuye;

iwo adzabweretsa ulemerero pa dzina lanu.

Pakuti ndinu wamkulu ndipo mumachita zodabwitsa;

Inu nokha ndiye Mulungu.

Tamanda Yehova, iwe moyo wanga;

ndi zonse zamʼkati mwanga zitamande dzina lake loyera.

Yamikani Yehova, itanani dzina lake;

lalikirani pakati pa anthu a mitundu ina zimene Iye wachita.

Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga,

moona mtima ine ndimakufunafunani;

moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Inu,

thupi langa likulakalaka inu,

mʼdziko lowuma ndi lotopetsa

kumene kulibe madzi.

Chifukwa chikondi chanu

ndi choposa moyo, milomo yanga idzakulemekezani.

Ndidzakutamandani masiku onse a moyo wanga,

ndipo mʼdzina lanu ndidzakweza manja anga.

Declarações de adoração

Tu és digno, Senhor, de receber glória e honra! Ao Senhor pertence a grandeza, o poder, a glória e a majestade.

"Ndinu woyeneradi kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu,

Ambuye ndi Mulungu wathu,

pakuti munalenga zinthu zonse,

ndipo mwakufuna kwanu

zinalengedwa monga zilili."

Mngeloyo anayankhula mokweza mawu kuti, "Wopani Mulungu ndi kumutamanda, chifukwa nthawi yoweruza anthu yafika. Mumupembedze Iye amene analenga thambo, dziko lapansi, nyanja ndi akasupe amadzi."

Inu Ambuye, ndani angapande kukuopani,

ndi kulemekeza dzina lanu?

Pakuti Inu nokha ndiye woyera.

Anthu a mitundu yonse adzabwera

kudzapembedza pamaso panu,

pakuti ntchito zanu zolungama zaonekera poyera."

Ine Yohane, ndine amene ndinamva ndi kuona zinthu izi. Ndipo pamene ndinamva ndi kuona izi ndinagwa pansi kuti ndipembedze mngelo amene amandionetsa zimenezi. Koma mngeloyo anandiwuza kuti, "Usatero ayi! Ine ndine wotumikira monga iwe pamodzi ndi abale ako aneneri ndi onse amene amasunga mawu a mʼbuku pembedzani Mulungu."

Wanu, Inu Yehova ndi ukulu ndi mphamvu,

ulemerero ndiponso ufumu ndi kukongola.

Pakuti zinthu zonse zakumwamba ndi pa dziko lapansi ndi zanu.

Wanu, Inu Yehova ndi ufumu;

Inu ndinu wokwezeka ndipo ndinu mtsogoleri wa zonse.

Yamikani Yehova, pakuti Iye ndi wabwino;

chikondi chake chikhala mpaka muyaya.

Fuwulani kuti, "Tipulumutseni, Inu Mulungu wa chipulumutso chathu,

mutisonkhanitse ndipo mutipulumutse kwa anthu a mitundu ina,

kuti tiyamike dzina lanu loyera,

kuti tikutamandeni."

Atamandike Yehova Mulungu wa Israeli,

kuyambira muyaya mpaka muyaya.

Ndipo anthu onse anati, "Ameni" ndipo "Tikutamandani Yehova."

Yamikani Yehova, pakuti Iye ndi wabwino;

chikondi chake chikhala mpaka muyaya.

Imbirani Iye, muyimbireni nyimbo zamatamando;

nenani za ntchito zake zonse zodabwitsa.

Choncho Mulungu anamukweza Iye kukhala wapamwamba kwambiri,

ndipo anamupatsa dzina loposa dzina lina lililonse

kuti pakumva dzina la Yesu, bondo lililonse limugwadire,

kumwamba ndi pa dziko lapansi ndi pansi pa dziko,

ndipo lilime lililonse livomereze kuti Yesu Khristu ndi Ambuye

kuchitira ulemu Mulungu Atate.

Sacrifício de louvor

Por meio de Jesus ofereçamos sempre sacrifício de louvor. Cantai ao Senhor, celebrai em salmos — enchei-vos do Espírito.

Tsono, tiyeni kudzera mwa Yesu tipereke nsembe zachiyamiko kwa Mulungu osalekeza, chipatso cha milomo imene imavomereza dzina lake.

Popeza tikulandira ufumu umene sungagwedezeke, tiyeni tikhale oyamika ndi kupembedza Mulungu movomerezeka ndi mwaulemu ndi mantha. Pakuti Mulungu wathu ndi moto wonyeketsa.

Muziyankhulana wina ndi mnzake mawu a Masalimo, nyimbo za Mulungu ndi nyimbo za uzimu. Muziyimbira Ambuye movomerezana ndi mitima yanu.

Mawu a Khristu akhazikike kwathunthu mʼmitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana wina ndi mnzake ndi nzeru zonse pamene mukuyimba Masalimo, nyimbo zotamanda ndi nyimbo zauzimu, kuyimbira Mulungu ndi mitima yoyamika.

Koma pakati pa usiku Paulo ndi Sila ankapemphera ndi kuyimba nyimbo zolemekeza Mulungu, ndipo akayidi ena ankamvetsera.

Mulungu Mwini Chitonthozo

Alemekezeke Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu, Atate achifundo chonse, Mulungu wachitonthozo chonse. Iye amatitonthoza ife mʼmavuto athu onse, kuti ifenso tithe kutonthoza amene ali pavuto lililonse ndi chitonthozo chimene ife tilandira kwa Mulungu.

Tikukulalikirani chimene tinachiona ndi kumva, kuti inuyo muyanjane nafe. Kuyanjana kwathu, tikuyanjana ndi Atate ndiponso ndi Mwana wawo, Yesu Khristu.

Adoração como vida

Exaltai ao Senhor, prostrai-vos ante o escabelo dos seus pés. A adoração genuína transforma o adorador e agrada o Criador.

Kwezani Yehova Mulungu wathu

ndipo mulambireni pa mapazi ake;

Iye ndi woyera.

Pakamwa panga padzaza ndi matamando anu,

kulengeza ulemerero wanu tsiku lonse.

Imbirani Mulungu imbirani dzina lake matamando,

mukwezeni Iye amene amakwera pa mitambo;

dzina lake ndi Yehova ndipo sangalalani pamaso pake.

Atate wa ana amasiye, mtetezi wa akazi amasiye,

ndiye Mulungu amene amakhala mʼmalo oyera.

Ine ndidzayamika Yehova chifukwa cha chilungamo chake;

ndipo ndidzayimba nyimbo zamatamando pa dzina la Yehova Wammwambamwamba.

Ine ndidzalengeza dzina lanu kwa abale anga;

ndidzakutamandani mu msonkhano.

Inu amene mumaopa Yehova mutamandeni!

Inu zidzukulu zonse za Yakobo, mulemekezeni!

Muopeni mwaulemu, inu zidzukulu zonse za Israeli!

Ndatambalitsa manja anga kwa Inu;

moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Inu monga nthaka yowuma.

Sela

Bwanji ukumva chisoni,

iwe mtima wanga?

Chifukwa chiyani ukuvutika chonchi mʼkati mwanga?

Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamutamandanso,

Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga.

Ndinati kwa Yehova, "Inu ndinu Ambuye anga;

popanda Inu, ine ndilibe chinthu chinanso chabwino."

Tumikirani Yehova mwa mantha

ndi kukondwerera ulamuliro wake monjenjemera.

Ndidzakondwa ndi kusangalala mwa inu;

Ndidzayimba nyimbo zamatamando pa dzina lanu, Inu Wammwambamwamba.

Falsa adoração

Não terás outros deuses diante de mim. Não adorarás ídolos. A adoração exclusiva ao Senhor é mandamento inegociável.

Usazigwadire kapena kuzipembedza, pakuti Ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wansanje, wolanga ana chifukwa cha tchimo la makolo awo mpaka mʼbado wachitatu ndi wachinayi wa iwo amene amadana nane.

Musapembedze mulungu wina, pakuti Yehova amene dzina lake ndi Nsanje, ndi Mulungu wa nsanje.

Mose akamalowa mu tenti, chipilala cha mtambo chimatsika ndi kukhala pa khomo pamene Yehova amayankhula ndi Mose. Nthawi zonse anthu akaona chipilala cha mtambo chitayima pa khomo la tentiyo amayimirira ndi kupembedza, aliyense ali pa khomo la tenti yake.

Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga;

ndiye chipulumutso changa.

Iye ndiye Mulungu wanga, ndipo ndidzamutamanda,

Mulungu wa makolo anga, ine ndidzamukweza.

Ndithu Yehova, pakati pa milungu,

ndani afanana nanu? Inu amene muli woyera,

ndiponso wotamandika wolemekezeka,

chifukwa cha ntchito zanu,

zazikulu ndi zodabwitsa?

Muzipembedza Yehova Mulungu wanu ndipo adzakudalitsani ndi chakudya ndi madzi ndiponso ndidzachotsa nthenda pakati panu.

Iye ndiye matamando anu, Mulungu wanu amene anakuchitirani zodabwitsa zazikulu ndi zoopsa zimene munaona ndi maso anu zija.

Kumeneko, pamaso pa Yehova Mulungu wanu, inu ndi mabanja anu mudzadya ndi kusangalalako pa china chilichonse chimene mudzakhudza, chifukwa Yehova Mulungu wanu wakudalitsani.

Anamuchititsa nsanje ndi milungu yawo yachilendo

ndiponso anamukwiyitsa ndi mafano awo onyansa.

Anapereka nsembe kwa ziwanda zimene si Mulungu,

milungu imene sankayidziwa nʼkale lomwe,

milungu yongobwera kumene,

milungu imene makolo anu sankayiopa.

Inu munasiya Thanthwe limene linakulerani;

munayiwala Mulungu amene anakubalani.

Dzisamalireni nokha, kuopa kuti mungakopeke mtima ndi kubwerera mʼmbuyo kuyamba kutumikira milungu ina ndi kumayigwadira.

Ambuye akuti,

"Anthu awa amandipembedza Ine ndi pakamwa pawo,

ndi kundilemekeza Ine ndi milomo yawo,

koma mitima yawo ili kutali ndi Ine.

Kundipembedza kwawo ndi kwa chiphamaso.

Amandipembedza motsata malamulo a anthu amene anaphunzitsidwa.

Nyimbo Yotamanda Yehova

Yehova ndinu Mulungu wanga;

ine ndidzakukwezani ndi kutamanda dzina lanu,

pakuti mwachita zodabwitsa

zimene munakonzekeratu kalekale

mokhulupirika kwambiri.

Koma Mulungu anawafulatira, nawapereka kuti apembedze zolengedwa zakumwamba. Zimenezi zikugwirizana ndi zimene zinalembedwa mʼbuku la aneneri kuti,

" Kodi pa zaka makumi anayi zimene munakhala mʼchipululu muja

munkandibweretsera nsembe ndi zopereka, inu nyumba ya Israeli?

Ayi, inu mwanyamula tenti ya Moloki

ndi nyenyezi ya mulungu wanu Refani,

mafano amene munapanga kuti muziwapembedza.

Chifukwa chake, Ine ndidzakutumizani kutali, kupitirira dziko la Babuloni.

Musalole kuti wina aliyense amene amakonda kudzichepetsa mwachiphamaso ndi kumapembedza angelo akulepheretseni kukalandira mphotho. Munthu woteroyu amayankhulanso mwatsatanetsatane zinthu zimene akuti anaziona mʼmasomphenya. Anthuwa ndi odzitukumula ndi fundo zopanda pake zochokera mʼmaganizo mwawo amene si auzimu. Iwo sakulumikizananso ndi mutu, kumene kumachokera thupi lonse, logwirizidwa ndi kumangiriridwa pamodzi ndi mʼmitsempha yake ndi mnofu, limene limakula monga mmene Mulungu afunira kuti likulire.

Musalole kuti wina aliyense akunamizeni mwa njira ina iliyonse. Pakuti tsikulo lisanafike, kudzakhala mpatuko waukulu kwambiri, ndipo kudzaoneka munthu woyipitsitsa uja, munthu woyenera kuwonongedwayo. Iyeyo adzatsutsa ndi kudziyika pamwamba pa chilichonse chimene anthu amachitcha mulungu kapena amachipembedza. Iyeyo adzadzikhazika mʼNyumba ya Mulungu ndi kudzitcha Mulungu.

Exemplos de adoração

Jó adorou em meio ao sofrimento. Esdras adorou na restauração. Paulo e Silas adoraram na prisão — e Deus respondeu.

Atamva zimenezi, Yobu anayimirira nangʼamba mkanjo wake, ndi kumeta tsitsi lake. Kenaka anadzigwetsa pansi napembedza Mulungu, nati,

"Ndinatuluka maliseche mʼmimba mwa amayi anga,

namonso mʼmanda ndidzalowa wamaliseche.

Yehova ndiye anapereka ndipo Yehova watenga;

litamandike dzina la Yehova."

Iwo ankayimba motamanda ndi mothokoza Yehova nyimbo iyi:

"Yehova ndi wabwino;

chikondi chake pa Israeli ndi chamuyaya."

Ndipo anthu onse ankafuwula kwambiri kumutamanda Yehova, chifukwa maziko a Nyumba ya Yehova anali kumangidwa.

Tsopano ine Nebukadinezara, ndikutamanda, kukweza ndi kulemekeza Mfumu yakumwamba chifukwa zonse zimene amachita ndi zoyenera ndipo njira zake zonse ndi zachilungamo. Ndipo onse amene amayenda modzikuza adzawatsitsa.

Inu ndinu wamkulu, Yehova Wamphamvuzonse! Palibe wina wofanana nanu, ndipo palibe Mulungu wina koma Inu nokha, monga tamvera ndi makutu athu.

"Palibe wina woyera ngati Yehova,

palibe wina koma inu nokha,

palibe thanthwe lofanana ndi Mulungu wathu.

Ndipo Alevi awa: Yesuwa, Kadimieli, Bani, Hasabaneya, Serebiya, Hodiya, Sebaniya ndi Petahiya anati: "Imirirani ndipo mutamande Yehova Mulungu wanu, amene ndi wamuyaya."

"Litamandike dzina lake laulemerero limene liposa madalitso ndi matamando onse.

Ngakhale mtengo wa mkuyu usachite maluwa,

ndipo mipesa ikhale yopanda mphesa.

Ngakhale mitengo ya olivi isabereke zipatso,

ndipo mʼminda musatuluke kanthu.

Ngakhale nkhosa

ndi ngʼombe zithe mʼkhola,

komabe ine ndidzakondwera mwa Yehova,

ndidzasangalala mwa Mulungu Mpulumutsi wanga.

Nthawi imeneyo mudzandiyitana, ndi kunditama mopemba ndipo ndidzakumverani.

Sendezani kufupi ndi Mulungu ndipo Iye adzasendeza kwa inu. Sambani mʼmanja mwanu, inu anthu ochimwa. Yeretsani mitima yanu, inu anthu okayikira.

Seja o primeiro