Publicidade

O adultério

Por Bíblia Online

O adultério é pecado grave que destrói alianças, famílias e vidas. A Bíblia condena firmemente a infidelidade conjugal e chama à pureza, fidelidade e santidade no casamento.

A lei de Deus

Não adulterarás. Quem comete adultério destrói a própria alma. A Palavra de Deus é clara e direta sobre este pecado.

"Usachite chigololo.

" Ngati munthu wachita chigololo ndi mkazi wa mnzake, mwamunayo pamodzi ndi mkaziyo ayenera kuphedwa.

" Usagonane ndi mkazi wa mnzako ndi kudziyipitsa naye.

Munthu wochita chigololo ndi wopanda nzeru.

Wochita zimenezi amangodziwononga yekha.

Munthu wochita chigololo ndi wopanda nzeru.

Wochita zimenezi amangodziwononga yekha.

Adzalandira mabala ndi mʼnyozo,

ndipo manyazi ake sadzamuchokera.

Paja nsanje imachititsa mwini mkaziyo kukalipa,

ndipo sadzachita chifundo pobwezera.

Iye savomera dipo lililonse;

sangapepeseke ngakhale umupatse mphatso zochuluka motani.

Kodi munthu angathe kutenga moto

zovala zake osapsa?

Kodi munthu angathe kuyenda pa makala amoto

mapazi ake osapserera?

Ndizo zimachitikira munthu amene amagonana ndi mkazi wa munthu wina.

Aliyense wokhudza mkazi wotere adzalangidwa.

Jesus ensina

Quem olhar para uma mulher com intenção impura já adulterou no coração. Jesus elevou o padrão da pureza.

Zokhudza Chigololo

"Munamva kuti kunanenedwa kuti, Usachite chigololo. Koma Ine ndikuwuzani kuti aliyense woyangʼana mkazi momusirira wachita naye kale chigololo mu mtima mwake.

Koma Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene asudzula mkazi wake pa chifukwa china chilichonse osati chifukwa cha chiwerewere, akumuchititsa mkaziyo chigololo ndipo aliyense wokwatira mkaziyo, akuchitanso chigololo.

Pakuti mu mtima mumatuluka maganizo oyipa, zakupha, zachigololo, zadama, zakuba, zaumboni wonama ndi zachipongwe.

Iye anayankha kuti, "Aliyense amene aleka mkazi wake ndi kukakwatira wina achita chigololo kulakwira mkaziyo. Ndipo akasiya mwamuna wake ndi kukakwatiwa ndi wina, achita chigololo."

"Aliyense amene asiya mkazi wake ndi kukakwatira mkazi wina akuchita chigololo, ndipo mwamuna amene akwatira mkazi wosiyidwayo akuchitanso chigololo."

anati kwa Yesu, "Aphunzitsi, mkazi uyu tinamugwira akuchita chigololo. Mʼmalamulo a Mose anatilamulira kuti akazi otere tiwagende ndi miyala. Tsopano Inu mukuti chiyani?" Iwo anagwiritsa ntchito funsoli ngati msampha, ndi cholinga choti apeze chifukwa cha kumuneneza Iye.

Koma Yesu anawerama pansi ndi kuyamba kulemba pa dothi ndi chala chake. Pamene iwo anapitirira kumufunsa, Iye anaweramuka ndipo anawawuza kuti, "Ngati wina wa inu alipo wopanda tchimo, ayambe iyeyo kumugenda ndi miyala mkaziyu." Iye anaweramanso pansi ndi kulemba pa dothi.

Iwo atamva izi anayamba kuchoka mmodzimmodzi, akuluakulu poyamba, mpaka Yesu anatsala yekha ndi mkaziyo atayimirira pomwepo. Yesu anaweramuka ndipo anamufunsa iye kuti, "Akuluakulu aja ali kuti? Kodi palibe amene wakutsutsa?"

Iye anati, "Ambuye, palibe ndi mmodzi yemwe."

"Inenso sindikukutsutsa iwe. Pita kuyambira tsopano usakachimwenso."

Armadilhas e consequências

Os lábios da mulher estranha destilam mel, mas o seu fim é amargo. Fuja da imoralidade — o adultério escraviza.

Pakuti mkazi wachigololo ali ndi mawu okoma ngati uchi.

Zoyankhula zake ndi zosalala ngati mafuta,

koma kotsirizira kwake ngowawa ngati ndulu;

ngakuthwa ngati lupanga lakuthwa konsekonse.

Mapazi ake amatsikira ku imfa;

akamayenda ndiye kuti akupita ku manda.

Iye saganizirapo za njira ya moyo;

njira zake ndi zokhotakhota koma iye sadziwa izi.

Pakuti mkazi wachigololo ali ndi mawu okoma ngati uchi.

Zoyankhula zake ndi zosalala ngati mafuta,

koma kotsirizira kwake ngowawa ngati ndulu;

ngakuthwa ngati lupanga lakuthwa konsekonse.

Mapazi ake amatsikira ku imfa;

akamayenda ndiye kuti akupita ku manda.

Iye saganizirapo za njira ya moyo;

njira zake ndi zokhotakhota koma iye sadziwa izi.

Tsopano ana inu, mundimvere;

musawasiye mawu anga.

Uziyenda kutali ndi mkazi wotereyo,

usayandikire khomo la nyumba yake,

kuopa kuti ungadzalanditse ulemerero wako kwa anthu ena;

ndi zaka zako kwa anthu ankhanza,

Uziyenda kutali ndi mkazi wotereyo,

usayandikire khomo la nyumba yake,

kuopa kuti ungadzalanditse ulemerero wako kwa anthu ena;

ndi zaka zako kwa anthu ankhanza,

kapenanso alendo angadyerere chuma chako

ndi phindu la ntchito yako kulemeretsa anthu ena.

Potsiriza pa moyo wako udzabuwula,

thupi lako lonse litatheratu.

Ndipo udzati, "Mayo ine, ndinkadana ndi kusunga mwambo!

Mtima wanga unkanyoza chidzudzulo!

Sindinamvere aphunzitsi anga

kapena alangizi anga.

Ine ndatsala pangʼono kuti ndiwonongeke

pakati pa msonkhano wonse."

Iye uja ali ngati mbalale yayikazi yokongola ndiponso ngati gwape wa maonekedwe abwino.

Ukhutitsidwe ndi mawere ake nthawi zonse,

ndipo utengeke ndi chikondi chake nthawi zonse.

Mwana wanga, nʼchifukwa chiyani ukukopeka ndi mkazi wachigololo?

Bwanji ukukumbatira mkazi wachilendo?

Pakuti nyumba yake imatsetserekera ku imfa;

njira zake zimamufikitsa ku manda.

Opita kwa iye palibe ndi mmodzi yemwe amabwerera

kapena kupezanso njira zamoyo.

Pakamwa pa mkazi wachigololo pali ngati dzenje lozama;

amene Yehova wamukwiyira adzagwamo.

Thawani dama. Machimo onse amene munthu amachita amakhala kunja kwa thupi lake, koma amene amachita machimo okhudza chigololo, amachimwira thupi lake lomwe.

Choncho ine ndikuti, mulole kuti Mzimu akutsogolereni ndipo simudzachita zofuna za thupi lanu la uchimo. Pakuti thupi lanu la uchimo limalakalaka zimene ndi zotsutsana ndi Mzimu, ndi Mzimu zimene ndi zotsutsana ndi thupi lanu la uchimo. Ziwirizi zimadana, kotero kuti simungachite zimene mukufuna.

Ntchito za thupi lanu la uchimo zimaonekera poyera ndi izi: dama, zodetsa ndi kuchita zonyansa; kupembedza mafano ndi ufiti; kudana, kukangana, kupsa mtima, kudzikonda, kugawikana, mipatuko ndi nsanje, kuledzera, mchezo ndi zina zotere. Ine ndikukuchenjezani monga ndinachita poyamba paja kuti amene amachita zimenezi sadzalandira ufumu wa Mulungu.

Ukwati muziwulemekeza nonse, ndipo mwamuna ndi mkazi azikhala wokhulupirika, pakuti anthu adama ndi achigololo Mulungu adzawalanga.

Ndi chifuniro cha Mulungu kuti muyeretsedwe: kuti mupewe dama; aliyense wa inu aphunzire kulamulira thupi lake mʼnjira yoyera ndi yaulemu, osati yotsata chilakolako chonyansa monga amachitira akunja, amene sadziwa Mulungu.

Inu anthu achigololo, kodi simukudziwa kuti kuchita ubwenzi ndi dziko lapansi ndi kudana ndi Mulungu? Choncho, aliyense wosankha kukhala bwenzi la dziko lapansi amasanduka mdani wa Mulungu.

Ndamupatsa nthawi kuti aleke zachigololo zake koma sakufuna. Tsono ndidzamugwetsa mʼmasautso ndipo amene amachita naye zadama zakezo ndidzawasautsa kwambiri akapanda kulapa ndi kuleka njira za mkaziyo.

Seja o primeiro
Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-29_22-07-56-