Pular para o conteúdo
Publicidade

Agradecimento pela família

Por Bíblia Online

Agradecer pela família é reconhecer a bênção mais preciosa que Deus nos concede. Os filhos são herança do Senhor — cada membro da família é presente divino a ser celebrado.

Ana ndiye cholowa chochokera kwa Yehova,

ana ndi mphotho yochokera kwa Iye.

Ana a pa unyamata ali ngati mivi mʼmanja

mwa munthu wankhondo.

Wodala munthu

amene motengera mivi mwake mwadzaza.

Iwo sadzachititsidwa manyazi

pamene alimbana ndi adani awo pa zipata.

Tamanda Yehova, iwe moyo wanga;

ndi zonse zamʼkati mwanga zitamande dzina lake loyera.

Tamanda Yehova, iwe moyo wanga,

ndipo usayiwale zabwino zake zonse.

Sitidzabisira ana awo,

tidzafotokozera mʼbado wotsatira

ntchito zotamandika za Yehova,

mphamvu zake, ndi zozizwitsa zimene Iye wachita.

Zidzukulu ndiye ulemu wa anthu okalamba,

ndipo makolo ndiye ulemerero wa ana.

Ndinapempha mwana uyu, ndipo Yehova wandipatsa chimene ndinamupempha.

Kuyamika ndi Pemphero

Ndimayamika Mulungu wanga nthawi zonse ndikakumbukira inu.

Tingathe bwanji kuyamika Mulungu mokwanira poona chimwemwe chonse chimene tili nacho pamaso pa Mulungu wathu chifukwa cha inu?

Perekani kwa Yehova, Inu mabanja a anthu a mitundu ina,

perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu,

Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera kumwamba, kwa Atate mwini kuwala, amene sasintha ngati mthunzi woyendayenda.

Kuchokera mʼkuchuluka kwa chisomo chake ife tonse talandira madalitso pamwamba pa madalitso.

Ndipo amayi osiyanasiyana anati kwa Naomi. "Alemekezeke Yehova, amene lero lino sanakusiyeni nokha wopanda wachibale. Mwanayu dzina lake likhale lotchuka mu Israeli. Mwanayo adzakupatseni moyo watsopano ndi kukuthandizani pa ukalamba wanu. Inde, mpongozi wanu amene amakukondani, amenenso waonetsa kuti ali wopambana kwa inu kuposa ana aamuna asanu ndi awiri, ndiye wakubalirani mwanayu."

Amoyo, amoyo okha ndiwo amakutamandani,

monga mmene ndikuchitira ine lero lino;

abambo amawuza ana awo za

kukhulupirika kwanu.

Seja o primeiro