Pular para o conteúdo
Publicidade

Amigo

Por Bíblia Online

O amigo verdadeiro é dádiva rara de Deus. Ele ama em todo tempo, fala a verdade em amor, aconselha com sabedoria e permanece fiel nas adversidades da vida.

Amizade verdadeira

Há amigo mais chegado que um irmão. Em todo tempo ama o amigo. O perfume e o incenso alegram o coração — assim o conselho doce do amigo.

Pali abwenzi amene chibwenzi chawo nʼchapamaso,

koma pali bwenzi limene limakukangamira kuposa mʼbale wako.

Bwenzi lako limakukonda nthawi zonse,

ndipo mʼbale wako anabadwa kuti azikuthandiza pamavuto.

Mafuta ndi zonunkhira zimasangalatsa mtima,

ndipo kukoma mtima kwa bwenzi kwagona pa malangizo ake.

Chitsulo chimanoledwa ndi chitsulo chinzake,

chomwechonso munthu amanoledwa ndi munthu mnzake.

Kudzudzula munthu poyera nʼkwabwino

kuposa chikondi chobisika.

Munthu amene amakukonda ngakhale akupweteke zili bwino,

koma mdani wako amakupsompsona mwachinyengo.

Usasiye bwenzi lako ndiponso bwenzi la abambo ako,

ndipo usapite ku nyumba ya mʼbale wako pamene wakumana ndi mavuto;

mnzako wokhala naye pafupi amaposa mʼbale wako wokhala kutali.

Woyenda ndi anthu anzeru nayenso adzakhala wanzeru;

koma woyenda ndi zitsiru adzapwetekeka.

Usapalane naye ubwenzi munthu wosachedwa kupsa mtima

ndipo usayanjane ndi munthu amene sachedwa kukwiya

kuopa kuti iwe ungadzaphunzire njira zake

ndi kukodwa mu msampha.

Anthu ambiri amayankhula za kukhulupirika kwawo,

koma munthu wokhulupirika angamupeze ndani?

Chuma chimachulukitsa abwenzi;

koma munthu wosauka bwenzi lake limamuthawa.

Jesus, o amigo

Já não vos chamo servos, mas amigos. O maior amor é dar a vida pelo amigo. Jesus é o amigo que nunca falha.

Palibe munthu ali ndi chikondi choposa ichi, choti munthu nʼkutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake. Inu ndinu abwenzi anga ngati muchita zimene Ine ndikulamulani. Ine sindikutchulaninso antchito, chifukwa wantchito sadziwa zimene bwana wake akuchita. Mʼmalo mwake Ine ndakutchani abwenzi pakuti zilizonse zimene ndinaphunzira kwa Atate, Ine ndakudziwitsani.

Lamulo langa ndi ili: Kondanani wina ndi mnzake monga Ine ndakonda inu. Palibe munthu ali ndi chikondi choposa ichi, choti munthu nʼkutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.

Anzanga okondedwa, popeza Mulungu anatikonda chotere, ifenso tiyenera kukondana wina ndi mnzake. Palibe amene anaonapo Mulungu, koma tikakondana wina ndi mnzake, ndiye kuti Mulungu amakhala mwa ife ndipo chikondi chake chafika pachimake penipeni mwa ife.

Mmene timadziwira chikondi chenicheni ndi umu: Yesu anapereka moyo wake chifukwa cha ife. Ndipo nafenso tiyenera kupereka miyoyo yathu chifukwa cha abale athu. Ngati wina ali ndi chuma ndipo nʼkuona mʼbale wake akusowa, koma wosamvera chisoni, kodi mwa iyeyo muli chikondi cha Mulungu? Ana okondedwa, chikondi chathu chisakhale cha pakamwa pokha koma cha ntchito zathu ndi mʼchoonadi.

Ndipo Malemba akunena kuti, "Abrahamu anakhulupirira Mulungu ndipo anatengedwa kukhala wolungama," ndipo anatchedwa bwenzi la Mulungu.

Mukondane kwathunthu monga abale. Lemekezanani wina ndi mnzake kuposa inu eni.

Companheiros de fé

Dois são melhores do que um. Os companheiros de fé se fortalecem mutuamente e caminham juntos com o Senhor.

Kukhala awiri nʼkwabwino kuposa kukhala wekha,

chifukwa ntchito ya anthu awiri ili ndi phindu:

Ngati winayo agwa,

mnzakeyo adzamudzutsa.

Koma tsoka kwa munthu amene agwa

ndipo alibe wina woti amudzutse!

Onani, nʼkokoma ndi kokondweretsa ndithu

pamene abale akhala pamodzi mwachiyanjano!

Zili ngati mafuta amtengowapatali othiridwa pa mutu,

otsikira ku ndevu,

ku ndevu za Aaroni,

oyenderera mpaka mʼkhosi mwa mkanjo wake.

Zili ngati mame a ku Heremoni

otsikira pa Phiri la Ziyoni.

Pakuti pamenepo Yehova amaperekapo dalitso,

ndiwo moyo wamuyaya.

Ine ndine bwenzi la onse amene amakukondani,

kwa onse amene amatsatira malangizo anu.

Ndipo Yonatani anapanga pangano ndi Davide chifukwa ankamukonda monga momwe ankadzikondera.

Musasocheretsedwe, "Kukhala mʼmagulu oyipa kumawononga makhalidwe abwino."

Seja o primeiro