Amor próprio
O amor próprio saudável reconhece o valor que Deus nos deu. Fomos criados à imagem de Deus, maravilhosamente formados. Aceitar-se é honrar o Criador.
Ndimakuyamikani chifukwa ndinapangidwa mochititsa mantha ndi modabwitsa;
ntchito zanu ndi zodabwitsa,
zimenezi ndimazidziwa bwino lomwe.
Zolingalira zanu pa ine ndi zamtengowapatali, Inu Mulungu,
ndi zosawerengeka ndithu!
Ndikanaziwerenga,
zikanakhala zochuluka kuposa mchenga;
pamene ndadzuka, ndili nanube.
Pamene ndilingalira za mayiko anu akumwamba,
ntchito ya zala zanu,
mwezi ndi nyenyezi,
zimene mwaziyika pa malo ake,
munthu ndani kuti Inu mumamukumbukira,
ndi mwana wa munthu kuti inu mumacheza naye?
Inu munamupanga kukhala wocheperapo kusiyana ndi zolengedwa zakumwamba
ndipo mwamuveka ulemerero ndi ulemu.
Iye amakweza munthu wosauka kuchoka pa fumbi
ndi kutukula munthu wosowa kuchoka pa dzala;
amawakhazika pamodzi ndi mafumu,
pamodzi ndi mafumu a anthu ake.
Koma Yehova anati kwa Samueli, "Usaone maonekedwe ake kapena msinkhu wake, pakuti ndamukana iyeyu. Yehova sapenya zimene munthu amapenya. Anthu amapenya zakunja, koma Mulungu amapenya za mu mtima."
Koma inu ndinu anthu osankhidwa ndi Mulungu, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu ake enieni a Mulungu, munasankhidwa kuti mulalikire za ntchito zamphamvu za Iye amene anakuyitanani kuti mutuluke mu mdima ndi kulowa mʼkuwunika kwake kodabwitsa.
Kodi atimba asanu samagulidwa ndi ndalama ziwiri? Ngakhale zili chomwecho palibe imodzi ya izo imene imayiwalika ndi Mulungu. Ndithudi, tsitsi lonse la mʼmutu mwanu ndi lowerengedwa. Musachite mantha; inu ndi oposa kwambiri mpheta zambiri.
Chifukwa cha chisomo chopatsidwa kwa ine, ndinena kwa aliyense wa inu kuti musadziyenereze nokha kuposa mmene mulili. Koma mudziganizire nokha modzichepetsa, molingana ndi muyeso wa chikhulupiriro chimene Mulungu wakupatsani.