Ânimo
O ânimo vem de Deus. Ele nos fortalece, nos encoraja e renova nossas forças. Quando o desânimo chega, as promessas de Deus nos levantam e nos impulsionam a seguir em frente.
Yehova ndiye kuwunika kwanga ndi chipulumutso changa;
ndidzaopa yani?
Yehova ndi linga la moyo wanga;
ndidzachita mantha ndi yani?
Chipulumutso cha olungama chimachokera kwa Yehova;
Iye ndiye linga lawo pa nthawi ya masautso.
Pamene ndinayitana, munandiyankha;
munandisandutsa wamphamvu ndi wolimba mtima.
Ndikhoza kuchita zonse kudzera mwa Iye amene amandipatsa mphamvu.
Sindikukayika konse kuti Iye amene anayamba ntchito yabwino mwa inu adzayipitiriza ndi kuyimaliza mpaka pa tsiku la kubweranso kwa Khristu Yesu.
Pakuti Mzimu amene Mulungu anatipatsa, si Mzimu wotipatsa manyazi, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzisunga.
Pakuti Ine ndikudziwa zimene ndinakukonzerani," akutero Yehova, "ndimalingalira zabwino zokhazokha za inu osati zoyipa, ayi. Ndimalingalira zinthu zokupatsani chiyembekezo chenicheni pa za mʼtsogolo.
Ndipo anthu anayankha, "Sizingatheke kuti timusiye Yehova ndi kutumikira milungu ina! Yehova Mulungu wathu ndiye amene anatitulutsa ife ndi makolo athu mu ukapolo, mʼdziko la Igupto. Tinaona ndi maso athu zizindikiro zozizwitsa zimene anachita. Iye anatiteteza pa ulendo wathu wonse ndi pakati pa mitundu yonse imene tinkakumana nayo.
Zimenezi zikukondweretseni kwambiri, ngakhale tsopano, kwa kanthawi kochepa, mukumva zowawa mʼmayesero osiyanasiyana.
Ine ndikulakalaka kukuonani kuti ndikugawireni mphatso zina zauzimu kuti zikulimbikitseni ndiponso kuti tonsefe tilimbikitsane mʼchikhulupiriro wina ndi mnzake.
Nʼchifukwa chake ife sititaya mtima. Ngakhale thupi lathu likunka lifowokerafowokera, koma mʼkatimu tikulimbikitsidwa mwatsopano tsiku ndi tsiku.
Choncho limbikitsanani wina ndi mnzake ndi kuthandizana kukula mu mzimu, monga momwe mukuchitira.
Motero abale, mʼmasautso ndi mʼmazunzo athu onse, chikhulupiriro chanu chatilimbikitsa.