Aniversário de idoso
O aniversário de um idoso é celebração de uma vida longa e cheia de experiências com Deus. A Bíblia honra os cabelos brancos como coroa de glória e prova da fidelidade divina.
Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino;
pakuti chikondi chake ndi chosatha.
Lero ndiye tsiku limene Yehova walipanga;
tiyeni tikondwere ndi kusangalala nalo.
Ndidzayamika Yehova nthawi zonse;
matamando ake adzakhala pa milomo yanga nthawi zonse.
Yehova ndiye mphamvu yanga ndi chishango changa;
mtima wanga umadalira Iye, ndipo Ine ndathandizidwa.
Mtima wanga umalumphalumpha chifukwa cha chimwemwe
ndipo ndidzayamika Iye mʼnyimbo.
Inu mwadzaza mtima wanga ndi chimwemwe chachikulu
kuposa kuchuluka kwa tirigu wawo ndi vinyo watsopano.
Inu mwandidziwitsa njira ya moyo;
mudzandidzaza ndi chimwemwe pamaso panu,
ndidzasangalala mpaka muyaya pa dzanja lanu lamanja.
Chinthu chimodzi chokha chimene ndipempha kwa Yehova,
ichi ndi chimene ndidzachifunafuna:
kuti ndikhale mʼNyumba ya Yehova
masiku onse a moyo wanga,
ndi kuyangʼana kukongola kwa Yehova,
ndi kumufunafuna Iye mʼNyumba yake.
Tiphunzitseni kuwerenga masiku athu molondola,
kuti tikhale ndi mtima wanzeru.
Imvi zili ngati chipewa chaufumu chaulemerero;
munthu amazipeza akakhala moyo wolungama.
Ulemerero wa achinyamata uli mu mphamvu zawo,
imvi ndi ulemerero wa anthu okalamba.
koma iwo amene amakhulupirira Yehova
adzalandira mphamvu zatsopano.
Adzawuluka ngati chiwombankhanga;
adzathamanga koma sadzalefuka,
adzayenda koma sadzatopa konse.
"Tsono papita zaka 45 chiyankhulire Yehova zimenezi kwa Mose. Nthawi imeneyo nʼkuti Aisraeli akuyendayenda mʼchipululu. Yehova wandisunga ndipo tsopano ndili ndi zaka 85. Komabe ndikanali ndi mphamvu lero, monga ndinalili tsiku lija Mose anandituma. Ndili ndi mphamvu moti ndikhoza kupita ku nkhondo kapena kuchita kanthu kena kalikonse.
" ‘Yehova akudalitse
ndi kukusunga;
Yehova awalitse nkhope yake pa iwe,
nakuchitira chisomo;
Yehova akweze nkhope yake pa iwe,
nakupatse mtendere.’ "
Wokondedwa, ndimakupempherera kuti zako zonse zikuyendere bwino, ndikuti ukhale bwino mʼthupi mwako, monga momwe ulili moyo wako wauzimu.