Publicidade

Aprender

Por Bíblia Online

Aprender é vocação do discípulo. Jesus disse: aprendei de mim. A Bíblia convida a aprender com humildade, perseverança e disposição — sentados aos pés do Mestre.

Aprender de Jesus

Tomai sobre vós o meu jugo e aprendei de mim. O Espírito Santo nos ensinará todas as coisas e nos recordará tudo.

Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wodzichepetsa. Ndipo inu mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti goli langa ndi losavuta ndipo katundu wanga ndi wopepuka."

Chifukwa chake, pitani kaphunzitseni anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza mʼdzina la Atate ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera, ndi kuwaphunzitsa amvere zonse zimene ndinakulamulirani. Ndipo onani, Ine ndidzakhala pamodzi ndi inu kufikira kutha kwa dziko lapansi pano."

Koma Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamutumiza mʼdzina langa adzakuphunzitsani zinthu zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndinakuwuzani.

Yesu anayankha kuti, "Chiphunzitso changa si cha Ine ndekha. Chimachokera kwa Iye amene anandituma.

Koma za inu, kudzoza kumene munalandira kwa Khristu kuli mwa inu, ndipo sipafunika wina aliyense kuti akuphunzitseni. Koma kudzozako kumakuphunzitsani zinthu zonse, ndipo popeza kudzoza kwakeko nʼkoona osati konama, monga munaphunzira, khalani mwa Iyeyo.

Ensino e sabedoria

O temor do Senhor é o princípio do saber. A disciplina do Senhor forma o caráter e abre caminhos de entendimento.

Kuopa Yehova ndiye chiyambi cha nzeru.

Zitsiru zimanyoza nzeru ndi malangizo.

Mwana wanga usanyoze malangizo a Yehova,

ndipo usayipidwe ndi chidzudzulo chake.

Paja Yehova amadzudzula amene amamukonda,

monga abambo achitira mwana amene amakondwera naye.

Ndakuphunzitsa njira yake ya nzeru.

Ndakutsogolera mʼnjira zolungama.

Munthu amene amakonda mwambo amakonda kudziwa zinthu,

koma amene amadana ndi chidzudzulo ndi wopusa.

Tsono dziwani mu mtima mwanu kuti monga abambo amalanga mwana wawo, momwemonso Yehova Mulungu wanu amakulangani.

Comunidade de aprendizado

Ensinem e aconselhem-se mutuamente. A igreja é escola de Cristo — onde todos ensinam e todos aprendem juntos.

Mawu a Khristu akhazikike kwathunthu mʼmitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana wina ndi mnzake ndi nzeru zonse pamene mukuyimba Masalimo, nyimbo zotamanda ndi nyimbo zauzimu, kuyimbira Mulungu ndi mitima yoyamika.

Choncho limbikitsanani wina ndi mnzake ndi kuthandizana kukula mu mzimu, monga momwe mukuchitira.

Ndipo tsiku ndi tsiku, sanaleke kuphunzitsa ndi kulalikira mʼNyumba ya Mulungu komanso nyumba ndi nyumba, Uthenga Wabwino wa kuti Yesu ndi Khristu.

Inu mukudziwa kuti, sindinakubisireni kanthu kalikonse kopindulitsa koma ndinakuphunzitsani poyera komanso nyumba ndi nyumba.

Muzichita chilichonse chimene mwaphunzira kapena kulandira kapena kumva kuchokera kwa ine kapena mwaona mwa ine. Ndipo Mulungu wamtendere adzakhala nanu.

Malangizo Osiyanasiyana

Koma iwe uziphunzitsa zogwirizana ndi chiphunzitso choona.

Ouvir e praticar

Ensina-me a fazer a tua vontade. Guia-me pela tua verdade. O verdadeiro aprendiz pratica o que ouviu do Mestre.

Phunzitseni kuchita chifuniro chanu,

popeza ndinu Mulungu wanga;

Mzimu wanu wabwino unditsogolere

pa njira yanu yosalala.

Ndidziwitseni njira zanu Inu Yehova,

phunzitseni mayendedwe anu;

tsogolereni mʼchoonadi chanu ndi kundiphunzitsa,

pakuti Inu ndinu Mulungu mpulumutsi wanga,

ndipo chiyembekezo changa chili mwa Inu tsiku lonse.

Yehova ndi wabwino ndi wolungama;

choncho Iye akulangiza ochimwa mʼnjira yake.

Amatsogolera odzichepetsa kuti achite zolungama

ndipo amawaphunzitsa njira zake.

Ndidzakulangiza ndi kukuphunzitsa njira imene udzayendamo;

ndidzakupatsa uphungu ndi kukuyangʼanira.

Moyo wanga umalakalaka Inu usiku wonse;

nthawi yammawa ndimafunafuna Inu.

Pamene muweruza dziko lapansi

anthu amaphunzira kuchita chilungamo.

Seja o primeiro
Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-29_22-07-56-