Bem
Fazer o bem é mandamento de Deus e expressão prática do amor cristão. A Bíblia convida a praticar o bem a todos, com alegria, sem se cansar — porque colheremos no tempo próprio.
Tembenuka kuchoka ku zoyipa ndipo chita zabwino;
funafuna mtendere ndi kuwulondola.
Khulupirira Yehova ndipo uzichita zabwino;
khazikika mʼdziko ndi kutsata zokhulupirika.
Ine ndikutsimikiza mtima za zimenezi;
ndidzaona ubwino wa Yehova
mʼdziko la anthu amoyo.
Kumbukirani Inu Yehova chifundo ndi chikondi chanu chachikulu,
pakuti ndi zakalekale.
Musakumbukire machimo a ubwana wanga
ndi makhalidwe anga owukira;
molingana ndi chikondi chanu ndikumbukireni ine,
pakuti Inu Yehova ndinu wabwino.
Yehova ndi wolungama mʼnjira zake zonse,
ndi wokonda zonse zimene anazipanga.
Choncho udzamvetsa tanthauzo la ungwiro, chilungamo,
kusakondera ndi njira iliyonse yabwino.
Chimene munthu amafuna ndi chikondi chosatha;
nʼkwabwino kukhala wosauka kusiyana ndi kukhala wabodza.
Koma chipatso cha Mzimu Woyera ndi chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndi kudziretsa. Palibe lamulo loletsa zimenezi.
Nʼchifukwa chake ngati tapeza mpata, tiyenera kuchitira zabwino anthu onse, makamaka amene ndi a banja la okhulupirira.
Mʼkamwa mwanu musatuluke mawu aliwonse onyansa, koma okhawo amene ndi othandiza kulimbikitsa ena molingana ndi zosowa zawo, kuti athandize amene akawamve.
Mukomerane mtima ndi kuchitirana chifundo wina ndi mnzake. Khululukiranani wina ndi mnzake, monga momwe Mulungu anakukhululukirani mwa Khristu.
Chikondi chikhale chopanda chinyengo. Dana nacho choyipa; gwiritsitsa chabwino.
Musagonjetsedwe ndi choyipa, koma gonjetsani choyipa pochita chabwino.
Mutha kunena kuti, "Zinthu zonse nʼzololedwa," komatu si zonse zili za phindu. "Zinthu zonse nʼzololedwa," komatu si zonse zimathandiza.
Musasocheretsedwe, "Kukhala mʼmagulu oyipa kumawononga makhalidwe abwino."
Ndipo Mulungu akhoza kukudalitsani kwambiri, kuti inuyo nthawi zonse mukhale ndi zinthu zokukwanirani, ndiponso ndi zina zochuluka kuti muthandize pa ntchito zonse zabwino.
Ndikufunanso kuti amayi azivala mwaulemu, modzilemekeza ndi moyenera. Adzikongoletse koma osati ndi tsitsi loluka mowonjeza muyeso kapena zokongoletsa zagolide kapena mikanda yamtengowapatali kapena ndi zovala zamtengowapatali. Koma adzikongoletse ndi ntchito zabwino zoyenera mayi wopembedza Mulungu.
amene anadzipereka yekha chifukwa cha ife kutiwombola ku zoyipa zonse ndi kudziyeretsera yekha anthu amene ndi akeake, achangu pa ntchito yabwino.
Choncho, chitani khama kuwonjezera moyo wabwino pa chikhulupiriro chanu, ndipo pa moyo wabwino muwonjezerepo nzeru. Pa nzeru muwonjezerepo kudziretsa, pa kudziretsa muwonjezerepo chipiriro, ndipo pa chipiriro muwonjezerepo khalidwe lolemekeza Mulungu. Pa khalidwe lolemekeza Mulungu muwonjezerepo chifundo cha ubale, pa chifundo cha ubale muwonjezerepo chikondi.
Ndani angakuchitireni zoyipa ngati muchita changu kuchita zabwino?
Yehova akuti,
"Imani pa mphambano ndipo mupenye;
kumeneko ndiye kuli njira zakale,
funsani kumene kuli njira yabwino. Yendani mʼmenemo,
ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.
Koma inu munati, ‘Ife sitidzayenda njira imeneyo.’
Yehova ndi wabwino,
ndiye kothawirako nthawi ya masautso.
Amasamalira amene amamudalira,
Anthu sayatsa nyale ndikuyivundikira ndi mbiya, mʼmalo mwake amayika poonekera ndipo imawunikira onse mʼnyumbamo. Momwemonso kuwunika kwanu kuwale pamaso pa anthu kuti aone ntchito zanu zabwino ndi kulemekeza Atate anu akumwamba.
Khalani achifundo, monga momwe Atate anu ali achifundo."