Bíblia
A Bíblia é a Palavra de Deus — viva, eficaz e mais cortante que espada de dois gumes. Toda Escritura é inspirada por Deus e útil para ensinar, repreender, corrigir e instruir em justiça.
Inspiração divina
Toda Escritura é inspirada por Deus. Homens santos falaram da parte de Deus movidos pelo Espírito Santo.
Malemba onse anawalembetsa ndi Mulungu, ndipo othandiza pophunzitsa, podzudzula, pokonza cholakwika ndi polangiza za chilungamo kuti munthu wa Mulungu akonzekere bwino lomwe kugwira ntchito iliyonse yabwino.
Kuyambira uli wamngʼono wakhala ukudziwa Malemba Oyera, amene akhoza kukupatsa nzeru zokupulumutsa kudzera mʼchikhulupiriro cha mwa Yesu Khristu. Malemba onse anawalembetsa ndi Mulungu, ndipo othandiza pophunzitsa, podzudzula, pokonza cholakwika ndi polangiza za chilungamo kuti munthu wa Mulungu akonzekere bwino lomwe kugwira ntchito iliyonse yabwino.
Kuposa zonse, inu muyenera kuzindikira kuti palibe mawu a uneneri amene amatanthauzidwa pa okha. Pakuti mawu a uneneri sanadze mwa kufuna kwa anthu, koma anthu anayankhula zochokera kwa Mulungu, Mzimu Woyera atawayankhulitsa.
Uyesetse kukhala wovomerezeka pamaso pa Mulungu monga wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi amene amalalikira mawu achoonadi molondola.
Lalikira Mawu; khala wokonzeka pa nthawi yake, ngakhale pamene si pa nthawi yake. Konza zolakwa zawo, dzudzula ndipo limbikitsa moleza mtima kwambiri ndi malangizo osamalitsa.
Mpaka nditabwera, udzipereke powerenga mawu a Mulungu kwa anthu, kulalikira ndi kuphunzitsa.
Poder da Palavra
A Palavra de Deus é viva e eficaz. O céu e a terra passarão, mas as minhas palavras jamais passarão.
Paja Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu. Ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse. Amalowa mpaka molumikizirana moyo ndi mzimu, ndiponso molumikizirana fundo ndi mafuta a mʼmafupa. Amaweruza malingaliro ndi zokhumba za mʼmitima.
Kumwamba ndi dziko lapansi zidzatha, koma mawu anga sadzatha."
Yesu anayankha kuti, "Zalembedwa, ‘Munthu sadzakhala ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu aliwonse ochokera mʼkamwa mwa Mulungu.’ "
Monga mvula ndi chisanu chowundana
zimatsika kuchokera kumwamba,
ndipo sizibwerera komweko
koma zimathirira dziko lapansi.
Ndipo zimameretsa ndi kukulitsa zomera
kenaka nʼkupatsa mlimi mbewu ndi chakudya.
Ndi mmenenso amachitira mawu ochokera mʼkamwa mwanga.
Sadzabwerera kwa Ine kopanda phindu lake,
koma adzachita zonse zimene ndifuna,
ndipo adzakwaniritsa cholinga chimene ndinawatumira.
Ayeretseni ndi choonadi chanu. Mawu anu ndiye choonadi.
Inu mumasanthula malemba chifukwa mumaganiza kuti mʼmalembamo muli moyo wosatha. Awa ndi malemba amene akundichitira umboni.
koma mawu a Ambuye adzakhala mpaka muyaya."
Ndipo awa ndi mawu amene tinalalikira kwa inu.
Kodi mnyamata angathe bwanji kuyeretsa mayendedwe ake?
Akawasamala potsata mawu anu.
Mawu anu onse ndi owona;
malamulo anu onse olungama ndi amuyaya.
Sini ndi Shini
Estudar e pregar
Os bereanos examinavam as Escrituras diariamente. Procura apresentar-te a Deus aprovado como obreiro que maneja bem a Palavra.
Tsopano anthu a ku Bereya anali akhalidwe labwino kusiyana ndi Atesalonika, pakuti iwo analandira mawu ndi chidwi chachikulu ndipo ankasanthula Malemba tsiku ndi tsiku kuti aone ngati zimene ankanena Paulozo zinali zoona.
Paulo, monga mwachizolowezi chake, analowa mʼsunagoge, ndipo anakambirana nawo Mawu a Mulungu kwa masabata atatu, kuwafotokozera ndi kuwatsimikizira kuti Khristu anayenera kufa ndi kuuka. Iye anati, "Yesu amene ndikukulalikirani ndiye Khristu."
Pamenepo Filipo anathamangira ku galeta ndipo anamva munthuyo akuwerenga buku la mneneri Yesaya. Filipo anamufunsa kuti, "Kodi mukumvetsa zimene mukuwerengazi?"
Iye anayankha kuti, "Ndingamvetse bwanji popanda wina wondimasulira?" Ndipo iye anayitana Filipo kuti abwere ndikukhala naye mʼgaleta.
Mawu amene ndunayo imawerenga anali awa:
"Monga mwana wankhosa wopita naye kokamupha amachitira,
kapena monga nkhosa imakhalira duu poyimeta,
momwemonso iye sanatsekule pakamwa pake.
Pamenepo Filipo anayambira pa malemba omwewo kumuwuza za Uthenga Wabwino wa Yesu.
Popeza Ezara anadzipereka kuwerenga ndi kusunga malamulo a Yehova, iye anafunitsitsa kuphunzitsa Aisraeli malamulo ndi malangizo a Mulungu.
Iye anawawuza kuti, "Inu ndinu anthu opusa, osafuna kukhulupirira msanga zonse zimene aneneri ananena! Kodi Khristu sanayenera kumva zowawa izi ndipo kenaka ndi kulowa mu ulemerero wake?" Ndipo kuyambira ndi Mose ndi aneneri onse Iye anawafotokozera zimene zinalembedwa mʼmalemba wonse zokhudzana ndi Iye mwini.
Kenaka Yesu anabwera kwa iwo nati, "Ulamuliro wonse kumwamba ndi dziko lapansi wapatsidwa kwa Ine. Chifukwa chake, pitani kaphunzitseni anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza mʼdzina la Atate ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera, ndi kuwaphunzitsa amvere zonse zimene ndinakulamulirani. Ndipo onani, Ine ndidzakhala pamodzi ndi inu kufikira kutha kwa dziko lapansi pano."
Pamene mukupita, muzikalalikira uthenga uwu: ‘Ufumu wakumwamba wayandikira.’
Revelação e fidelidade
A Palavra do Senhor veio aos profetas. A graça de Deus se manifestou na Escritura para a salvação de todos.
Yehova anayankhula naye kuti,
Yehova anayankhula ndi Yoweli mwana wa Petueli.
Yehova anawuza Yeremiya kuti:
Uthenga: Mawu a Yehova kwa Israeli kudzera mwa Malaki.
Ndipo Yehova anayankhulanso ndi Zekariya kuti,
Ndipo Yehova analamula Yesaya kuti:
Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine,
chifukwa Yehova wandidzoza
kuti ndilalikire uthenga wabwino kwa anthu osauka.
Wandituma kuti ndikatonthoze anthu osweka mtima,
ndikalengeze kwa akapolo kuti alandire ufulu
ndiponso kuti ndikamasule a mʼndende.
Wandituma kuti ndikalengeze nthawi imene Yehova adzapulumutsa anthu ake;
za tsiku limene Yehova adzalanga adani a anthu ake.
Wandituma kuti ndikatonthoze olira.
Wandituma kuti ndiwakonzere olira a ku Ziyoni,
nkhata ya maluwa yokongola
mʼmalo mwa phulusa,
ndiwapatse mafuta achikondwerero
mʼmalo mwa kulira.
Ndiwapatse chovala cha matamando
mʼmalo mwa mtima wopsinjika.
Ndipo iwo adzatchedwa mitengo ya thundu yamphamvu yachilungamo,
yoyidzala Yehova
kuti Iye mwini apezemo ulemerero wake.
Viver pela Palavra
Não só de pão vive o homem. Nada acrescentes nem diminuas. A Palavra é alimento, guia e espada do cristão.
"Mawu ali wonse a Mulungu ndi opanda cholakwika;
Iye ndi chishango kwa amene amathawira kwa Iye.
Usawonjezepo kanthu pa mawu ake,
kuopa kuti Iye angadzakudzudzule ndi kukupeza kuti ndiwe wabodza."
Ndikuchenjeza aliyense amene akumva mawu onena zamʼtsogolo a mʼbukuli kuti, "Ngati wina awonjezerapo kalikonse, Mulungu adzamuwonjezera miliri imene yalembedwa mʼbuku ili. Ndipo wina akachotsapo mawu onena zamʼtsogolo a mʼbuku ili, Mulungu adzachotsa gawo lake pa mtengo wamoyo ndi la mu mzinda woyera zimene zanenedwa mʼbuku ili."
Ine ndikudabwa kuti mukusiya mwamsangamsanga chotere Mulungu amene anakuyitanani mwachisomo cha Khristu ndipo mwatembenuka ndi kutsatira uthenga wina wosiyana, umene si Uthenga Wabwino konse. Pali anthu ena amene akukusokonezani komanso akufuna kupotoza Uthenga Wabwino wa Khristu. Ngakhale ife kapena mngelo wochokera kumwamba, akalalikira Uthenga Wabwino wosiyana ndi umene tinakulalikirani uja, iyeyo akhale wotembereredwa! Monga tanena kale, tsopano ndikubwereza kunenanso kuti, "Ngati wina aliyense akulalikirani Uthenga Wabwino wosiyana ndi umene munawulandira, iyeyo akhale wotembereredwa."
Zindikirani kuti kuleza mtima kwa Ambuye kukutanthauza chipulumutso, monga momwe mʼbale wathu wokondedwa Paulo anakulemberaninso ndi nzeru zimene Mulungu anamupatsa. Iye walemba chimodzimodzi makalata ake onse, kuyankhula za zinthu izi. Mʼmakalata ake mumakhala zinthu zina zovuta kuzimvetsa, zimene anthu osadziwa ndi osakhazikika amazipotoza, monga amachita ndi malemba ena onse, potero akudziwononga okha.
Pakuti zilizonse zimene zinalembedwa kale zinalembedwa kuti zitiphunzitse ife. Malembawo amatilimbikitsa kupirira kuti tikhale ndi chiyembekezo.
Kodi adzayitana bwanji amene sanamukhulupirire? Ndipo adzakhulupirira bwanji asanamve za Iye? Ndipo adzamva bwanji popanda wina kulalikira kwa iwo? Ndipo iwo adzalalikira bwanji osatumidwa? Kwalembedwa kuti, "Akongoladi mapazi a iwo amene amabweretsa Uthenga Wabwino!"
Koma si onse amene anavomereza Uthenga Wabwino. Pakuti Yesaya akuti, "Ambuye, ndani amene wakhulupirira uthenga wathu?" Motero, chikhulupiriro chimabwera pamene timva uthenga ndipo uthenga umamveka kuchokera ku mawu a Khristu.
Ine sindichita manyazi ndi Uthenga Wabwino chifukwa ndiwo mphamvu za Mulungu zopulumutsa aliyense amene akhulupirira, poyamba Myuda, kenaka Mhelene. Pakuti mu Uthenga Wabwino anawulula kuti chilungamo chimachokera kwa Mulungu. Kuyambira pachiyambi mpaka potsiriza ndi chilungamo chobwera mwachikhulupiriro, monga kwalembedwera kuti, "Wolungama adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro."
Mzimu amene tinalandira ife si wa dziko lapansi koma Mzimu wochokera kwa Mulungu wotipatsa ife mwaulere. Izi ndi zimene timayankhula osati mʼmawu wophunzitsidwa ndi nzeru za munthu koma mʼmawu wophunzitsidwa ndi Mzimu, kufotokozera zoonadi zauzimu mʼmawu auzimu. Munthu wopanda Mzimu savomereza zinthu zimene zichokera kwa Mzimu wa Mulungu, popeza ndi zopusa kwa iyeyo, ndipo sangazimvetsetse chifukwa zimazindikirika mwa Mzimu.
Tsono poti mwa nzeru za Mulungu dziko lapansi mu nzeru zake silinamudziwe Iye, Mulungu amakondweretsedwa kuti kudzera mu chopusa cha zomwe zinalalikidwa apulumutse iwo amene akhulupirira.
Ayuda amafuna zizindikiro zodabwitsa ndipo Agriki amafunafuna nzeru, koma ife timalalikira Khristu wopachikidwa. Chitsa chokhumudwitsa kwa Ayuda ndi chopusa kwa a mitundu ina. Koma kwa iwo amene Mulungu anawayitana, Ayuda ndi Agriki omwe, Khristu ndi mphamvu ya Mulungu ndi nzeru za Mulungu.
Pakuti Khristu sananditume ine kudzabatiza, koma kudzalalikira Uthenga Wabwino, osati ndi mawu anzeru za umunthu, kuopa kuti mtanda wa Khristu ungakhale wopanda mphamvu.
Koma inu ndinu anthu osankhidwa ndi Mulungu, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu ake enieni a Mulungu, munasankhidwa kuti mulalikire za ntchito zamphamvu za Iye amene anakuyitanani kuti mutuluke mu mdima ndi kulowa mʼkuwunika kwake kodabwitsa.