Publicidade

Bom ânimo

Por Bíblia Online

Tende bom ânimo! Jesus repetiu estas palavras aos seus discípulos em meio às tempestades. No mundo tereis aflições, mas Ele já venceu o mundo — e nos dá coragem para enfrentar tudo.

"Ine ndakuwuzani izi kuti mwa Ine mukhale nawo mtendere. Mʼdziko lapansi mudzakhala nawo mavuto. Koma limbikani mtima! Ine ndaligonjetsa dziko lapansi."

Paja ndinakulamula kuti ukhale wamphamvu ndi wolimba mtima. Choncho usamachite mantha kapena kutaya mtima popeza Ine Yehova Mulungu wako ndidzakhala nawe kulikonse kumene udzapite."

Yoswa anawawuza kuti, "Musaope kapena kutaya mtima. Khalani amphamvu ndi olimba mtima popeza umo ndi mmene Yehova adzachitire ndi adani anu onse amene mudzamenyana nawo."

Tsono usaope, pakuti Ine ndili nawe;

usataye mtima chifukwa Ine ndine Mulungu wako.

Ndidzakupatsa mphamvu ndipo ndidzakuthandiza,

ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.

Pakuti Mzimu amene Mulungu anatipatsa, si Mzimu wotipatsa manyazi, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzisunga.

Ndikhoza kuchita zonse kudzera mwa Iye amene amandipatsa mphamvu.

Khalani ndi nyonga ndipo limbani mtima,

inu nonse amene mumayembekezera Yehova.

Pamene ndinayitana, munandiyankha;

munandisandutsa wamphamvu ndi wolimba mtima.

Yehova ndiye kuwunika kwanga ndi chipulumutso changa;

ndidzaopa yani?

Yehova ndi linga la moyo wanga;

ndidzachita mantha ndi yani?

Koma Yesu nthawi yomweyo anawawuza kuti, "Limbani mtima! Ndine, musaope."

pakuti onse anamuona ndipo anachita mantha.

Nthawi yomweyo Iye anawayankhula nati, "Limbani mtima! Ndine. Musachite mantha."

Kenaka anati kwa iye, "Mwana wamkazi, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Pita mu mtendere."

Nʼchifukwa chake nthawi zonse timalimba mtima, ndipo timadziwa kuti pamene tikukhala mʼthupi, ndiye kuti tili kutali ndi Ambuye.

Pa tsiku la 23 la mwezi wachisanu ndi chiwiri, Solomoni anawuza anthu aja kuti apite kwawo. Anthu anali achimwemwe ndi okondwa mʼmitima mwawo chifukwa cha zinthu zabwino zimene Yehova anachitira Davide ndi Solomoni ndiponso anthu ake Aisraeli.

"Khalani amphamvu ndi olimba mtima. Musachite mantha kapena kutaya mtima chifukwa cha mfumu ya ku Asiriya ndi gulu lalikulu lankhondo limene ali nalo, pakuti ife tili ndi mphamvu yayikulu kuposa imene ili ndi iye.

Ngati utaya mtima nthawi ya mavuto ndiye kuti

mphamvu yako ndi yochepadi!

Tsono limbani mtima, anthu inu, pakuti ine ndili ndi chikhulupiriro mwa Mulungu kuti zichitika monga momwe wandiwuzira.

Sindikukayika konse kuti Iye amene anayamba ntchito yabwino mwa inu adzayipitiriza ndi kuyimaliza mpaka pa tsiku la kubweranso kwa Khristu Yesu.

Zimenezi zikukondweretseni kwambiri, ngakhale tsopano, kwa kanthawi kochepa, mukumva zowawa mʼmayesero osiyanasiyana.

Chipulumutso cha olungama chimachokera kwa Yehova;

Iye ndiye linga lawo pa nthawi ya masautso.

Ine ndikulakalaka kukuonani kuti ndikugawireni mphatso zina zauzimu kuti zikulimbikitseni ndiponso kuti tonsefe tilimbikitsane mʼchikhulupiriro wina ndi mnzake.

Nʼchifukwa chake ife sititaya mtima. Ngakhale thupi lathu likunka lifowokerafowokera, koma mʼkatimu tikulimbikitsidwa mwatsopano tsiku ndi tsiku.

Choncho limbikitsanani wina ndi mnzake ndi kuthandizana kukula mu mzimu, monga momwe mukuchitira.

Motero abale, mʼmasautso ndi mʼmazunzo athu onse, chikhulupiriro chanu chatilimbikitsa.

Ndipo anthu anayankha, "Sizingatheke kuti timusiye Yehova ndi kutumikira milungu ina! Yehova Mulungu wathu ndiye amene anatitulutsa ife ndi makolo athu mu ukapolo, mʼdziko la Igupto. Tinaona ndi maso athu zizindikiro zozizwitsa zimene anachita. Iye anatiteteza pa ulendo wathu wonse ndi pakati pa mitundu yonse imene tinkakumana nayo.

Pakuti Ine ndikudziwa zimene ndinakukonzerani," akutero Yehova, "ndimalingalira zabwino zokhazokha za inu osati zoyipa, ayi. Ndimalingalira zinthu zokupatsani chiyembekezo chenicheni pa za mʼtsogolo.

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-22_10-02-25-