Publicidade

O que é bom

Por Bíblia Online

O que é bom vem de Deus. A Bíblia celebra a bondade divina e nos convida a discernir, praticar e desfrutar tudo o que é bom — porque toda boa dádiva vem do Pai das luzes.

Mulungu anaona zonse zimene anazilenga kuti zinali zabwino kwambiri. Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa, tsiku lachisanu ndi chimodzi.

Yehova ndi wabwino ndi wolungama;

choncho Iye akulangiza ochimwa mʼnjira yake.

Koma kunena za Ine ndi kwabwino kukhala pafupi ndi Mulungu.

Ndatsimikiza kuti Ambuye Yehova ndiwo pothawirapo panga

ndipo ndidzalalika ntchito zanu zonse.

Salimo. Nyimbo ya pa tsiku la Sabata.

Nʼkwabwino kutamanda Yehova

ndi kuyimbira nyimbo dzina lanu, Inu Wammwambamwamba,

Kulengeza chikondi chanu mmawa,

ndi kukhulupirika kwanu nthawi ya usiku,

kuyimbira nyimbo choyimbira cha zingwe khumi

ndi mayimbidwe abwino a zeze.

Pakuti Yehova ndi wabwino ndipo chikondi chake ndi chamuyaya;

kukhulupirika kwake nʼkokhazikika pa mibado ndi mibado.

Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

Onani, nʼkokoma ndi kokondweretsa ndithu

pamene abale akhala pamodzi mwachiyanjano!

Zimene ndikukuphunzitsani ndi zabwino.

Choncho musasiye malangizo anga.

Munthu amakondwera ndi kuyankha koyenera,

ndipo mawu onena pa nthawi yake ndi okoma.

Mwana wanga, uzidya uchi popeza ndi wabwino;

uchi wochokera mʼchisa cha njuchi ndi wokoma ukawulawa.

Udziwe kuti nzeru ndi yoteronso pa moyo wako;

ngati uyipeza nzeruyo, zinthu zidzakuyendera bwino mʼtsogolo,

ndipo chiyembekezo chako sichidzapita pachabe.

Nzeru ngati cholowa, ndi chinthu chabwino

ndipo imapindulitsa wamoyo aliyense pansi pano.

Yehova ndi wabwino kwa amene amayembekezera Iye,

kwa munthu amene amafunafuna Iyeyo;

nʼkwabwino kudikira chipulumutso cha

Yehova modekha.

Munthu iwe, Yehova wakuonetsa kale chimene chili chabwino.

Tsono kodi Yehova akuyembekezera chiyani kwa iwe?

Uzichita zolungama ndi kukonda chifundo

ndiponso kuyenda modzichepetsa pamaso pa Mulungu wako.

Choncho lamulo ndi loyera, lolungama ndi labwino.

Musafanizidwenso ndi makhalidwe a dziko lino koma musandulike pokonzanso maganizo anu. Ndipo mudzadziwa ndi kuzindikira chifuniro chabwino cha Mulungu chomwe ndi chokondweretsa ndi changwiro.

Musalole kuti chimene muchiyesa chabwino achinene ngati choyipa.

Malangizo Achipembedzo

Tsono choyamba ndikukupemphani kuti mupempherere anthu onse. Mapemphero anu akhale opemba, opempha, opempherera ena ndi oyamika. Mupempherere mafumu ndi onse aulamuliro, kuti tikhale moyo wamtendere ndi bata, woopa Mulungu ndi oyera mtima. Izi ndi zabwino ndipo zimakondweretsa Mulungu Mpulumutsi wathu,

Pakuti chilichonse chimene Mulungu analenga ndi chabwino, ndipo chilichonse chisasalidwe, akamachilandira moyamika, pakuti chimayeretsedwa ndi mawu a Mulungu ndi pemphero.

Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera kumwamba, kwa Atate mwini kuwala, amene sasintha ngati mthunzi woyendayenda.

"Mchere ndi wabwino, koma ngati utasukuluka, mungawukoleretsenso bwanji? Mukhale nawo mchere mwa inu nokha, ndipo mukhale pa mtendere wina ndi mnzake."

Seja o primeiro
Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-29_22-07-56-