Casa de Deus
A casa de Deus é lugar de adoração, refúgio e encontro com o Sagrado. A Bíblia exalta o tabernáculo, o templo e a igreja como morada do Altíssimo entre seu povo.
A presença de Deus
Quão amáveis são os teus tabernáculos! Uma coisa pedi ao Senhor: habitar na casa do Senhor todos os dias da minha vida.
Nʼkwabwino kukhala mʼmabwalo anu tsiku limodzi
kuposa kukhala kwina kwake kwa zaka 1,000;
Ine ndingakonde kukhala mlonda wa pa khomo la Nyumba ya Mulungu wanga
kuposa kukhala mʼmatenti a anthu oyipa.
Chinthu chimodzi chokha chimene ndipempha kwa Yehova,
ichi ndi chimene ndidzachifunafuna:
kuti ndikhale mʼNyumba ya Yehova
masiku onse a moyo wanga,
ndi kuyangʼana kukongola kwa Yehova,
ndi kumufunafuna Iye mʼNyumba yake.
Odala iwo amene inu muwasankha
ndi kuwabweretsa pafupi kukhala mʼmabwalo anu!
Ife tadzazidwa ndi zinthu zabwino za mʼNyumba mwanu,
za mʼNyumba yanu yoyera.
Ndinakondwera atandiwuza kuti,
"Tiyeni ku nyumba ya Yehova."
Zoonadi, zokoma ndi chikondi chosasinthika zidzanditsata
masiku onse a moyo wanga,
ndipo ndidzakhala mʼNyumba ya Yehova
kwamuyaya.
Koma ine ndili ngati mtengo wa olivi
wobiriwira bwino mʼnyumba ya Mulungu;
ndimadalira chikondi chosatha cha Mulungu
kwa nthawi za nthawi.
pakuti changu chochitira nyumba yanu chandiphetsa
ndipo chipongwe cha iwo amene amanyoza Inu chandigwera.
O templo
Minha casa será chamada casa de oração. O zelo da tua casa me consumiu. O verdadeiro templo é o corpo do cristão.
Yesu analowa mʼdera lina la Nyumba ya Mulungu ndipo anatulutsa kunja anthu onse amene ankachita malonda. Anagubuduza matebulo a osinthira ndalama ndi mipando ya ogulitsa nkhunda. Iye anawawuza kuti, "Zinalembedwa kuti Nyumba yanga idzatchedwa Nyumba ya mapemphero koma inu mwayisandutsa phanga la anthu achifwamba."
Nthawi ya Paska ya Ayuda itayandikira, Yesu anapita ku Yerusalemu. Mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu Iye anapeza anthu akugulitsa ngʼombe, nkhosa ndi nkhunda ndipo ena akusintha ndalama pa matebulo. Chifukwa cha zimenezi Iye anapanga chikwapu cha zingwe ndipo anatulutsa onse mʼbwalo la Nyumbayo, pamodzi ndi nkhosa ndi ngʼombe; Iye anamwaza ndalama zawo ndi kugudubuza matebulo. Kwa amene amagulitsa nkhunda, Iye anati, "Tulutsani izi muno! Osasandutsa Nyumba ya Atate anga msika!"
Ophunzira ake anakumbukira kuti zinalembedwa kuti, "Kudzipereka kwanga ku nyumba yanu kudzandiphetsa."
Kodi simukudziwa kuti thupi lanu ndi Nyumba ya Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene mwalandira kuchokera kwa Mulungu? Inu simuli panokha ayi.
Ine zina zikandichedwetsa kubwera, mudziwe za mmene anthu ayenera kukhalira mʼNyumba ya Mulungu, imene ndi mpingo wa Mulungu wamoyo, mzati ndi maziko achoonadi.
Koma Khristu ndi wokhulupirika monga mwana pa nyumba ya Mulungu. Ndipo ndife nyumba yake ngati tipitirire kulimbika mtima ndi kunyadira zomwe tikuyembekerazo.
"Makolo athu anali ndi tenti ya msonkhano pakati pawo mʼchipululu. Anayipanga monga momwe Mulungu anawuzira Mose, molingana ndi chithunzi chimene Mose anachiona. Makolo athu, atayilandira Tentiyo, anabwera nayo motsogozedwa ndi Yoswa pamene analanda dziko la mitundu imene Mulungu anayipirikitsa pamaso pawo. Tentiyo inakhala mʼdzikomo mpaka nthawi ya Davide, amene anapeza chisomo pamaso pa Mulungu ndipo anapempha kuti amʼmangire nyumba Mulungu wa Yakobo. Koma anali Solomoni amene anamanga nyumbayo.
"Komatu, Wammwambamwambayo sakhala mʼnyumba zomangidwa ndi anthu. Monga mneneri akunena kuti,
" ‘Kumwamba ndi mpando wanga waufumu,
ndipo dziko lapansi ndi chopondapo mapazi anga.
Kodi mudzandimangira nyumba yotani?
Akutero Ambuye.
Kapena malo opumuliramo Ine ali kuti?
Kodi si dzanja langa linapanga zonsezi?’
Yehova akuti,
"Kumwamba ndi mpando wanga waufumu
ndipo dziko lapansi ndilo chopondapo mapazi anga.
Tsono nyumba ili kuti yomwe mundimangire,
ndipo malo ali kuti amene inu mungandikonzere kuti ndizipumuliramo?
Kodi si manja anga amene anapanga zinthu zonsezi,
motero zonsezi ndi zanga?"
Akutero Yehova.
"Koma munthu amene ndimakondwera naye ndi uyu:
amene ali wodzichepetsa ndi wosweka mtima,
ndipo amamvera mawu anga.
Yakobo atadzidzimuka, anati, "Zoonadi Yehova ali pa malo ano, ndipo ine sindinadziwe." Tsono anachita mantha ndipo anati, "Malo ano ndi woopsa ndithu. Zoonadi pano ndi pa nyumba ya Mulungu ndi khomo la kumwamba."