Pular para o conteúdo
Publicidade

Colheita

Por Bíblia Online

A colheita é princípio bíblico universal: colhemos o que semeamos. Quem semeia na fé e obediência colherá bênçãos abundantes do Senhor.

Semear e colher

Quem semeia no Espírito, do Espírito colherá vida eterna. Não nos cansemos de fazer o bem — ao tempo certo colheremos.

Pakuti amene amafesa zokondweretsa thupi lake la uchimo, kuchokera ku khalidwe limenelo adzakolola chiwonongeko; amene amafesa zokondweretsa Mzimu, kuchokera kwa Mzimu adzakolola moyo wosatha.

Musanamizidwe: nʼkosatheka kupusitsa Mulungu. Munthu amakolola zimene wafesa.

Tisatope nʼkuchita zabwino, pakuti pa nthawi yoyenera tidzakolola ngati sititopa.

Tsono Mulungu amene amapereka mbewu kwa wofesa, ndiponso chakudya kuti adye, adzaperekanso mbewu mʼnkhokwe zanu ndi kuzichulukitsa. Iye adzachulukitsanso zipatso za chilungamo chanu.

Anthu amtendere amene amadzala mtendere amakolola chilungamo.

Palibe chilango chimene chimaoneka kuti ndi chabwino pa nthawiyo, komatu chowawa. Koma pambuyo pake, chimabweretsa chipatso chachilungamo ndi mtendere kwa iwo amene aleredwa mwa njira imeneyi.

Fidelidade na semeadura

Honra ao Senhor com as tuas primícias. O Senhor abrirá as janelas do céu e derramará bênção sem medida.

Uzilemekeza Yehova ndi chuma chako chonse;

zokolola zonse zoyamba kucha uzilemekeza nazonso Yehova.

Bweretsani chakhumi chathunthu ku nyumba yosungira, kuti mukhale chakudya mʼnyumba mwanga." Akutero Yehova Wamphamvuzonse, "Tandiyesani, ndipo muone ngati sindidzatsekula zipata zakumwamba, ndi kukugwetserani madalitso ochuluka amene mudzasowe malo owayikamo.

" Mukamayenda motsata malangizo anga ndi kumvera mosamalitsa malamulo anga, ndidzakupatsani mvula pa nyengo yake. Nthaka yanu idzabala zokolola zake, ndipo mitengo ya mʼmunda idzabala zipatso zake.

Onani mbalame zamlengalenga sizifesa kapena kukolola kapena kusunga mʼnkhokwe komabe Atate anu akumwamba amazidyetsa. Kodi inu simuziposa kwambiri?

Mpesa wauma

ndipo mtengo wamkuyu wafota;

makangadza, kanjedza ndi mitengo ya apulosi,

mitengo yonse ya mʼmunda yauma.

Ndithudi chimwemwe cha anthu

chatheratu.

Ngakhale mtengo wa mkuyu usachite maluwa,

ndipo mipesa ikhale yopanda mphesa.

Ngakhale mitengo ya olivi isabereke zipatso,

ndipo mʼminda musatuluke kanthu.

Ngakhale nkhosa

ndi ngʼombe zithe mʼkhola,

komabe ine ndidzakondwera mwa Yehova,

ndidzasangalala mwa Mulungu Mpulumutsi wanga.

Seja o primeiro