Compaixão
A compaixão é o coração de Deus em ação. Ele é compassivo e misericordioso, tardio em irar-se e grande em amor. Somos chamados a refletir essa compaixão no mundo.
Monga bambo amachitira chifundo ana ake,
choncho Yehova ali ndi chifundo ndi iwo amene amamuopa;
Koma Ambuye ndinu Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima,
wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi ndi wokhulupirika.
Chifukwa chikondi chanu
ndi choposa moyo, milomo yanga idzakulemekezani.
Ife sitinawonongekeretu chifukwa chikondi cha Yehova ndi chachikulu,
ndi chifundo chake ndi chosatha.
Zimaoneka zatsopano mmawa uliwonse;
kukhulupirika kwanu nʼkwakukulu.
"Kodi amayi angathe kuyiwala mwana wawo wakubere
ndi kusachitira chifundo mwana amene anabereka iwo eni?
Ngakhale iye angathe kuyiwala,
Ine sindidzakuyiwala iwe!
Taona, ndakulemba iwe mʼzikhantho zanga;
makoma ako ndimawaona nthawi zonse.
Komatu Yehova akufunitsitsa kuti akukomereni mtima,
iye ali wokonzeka kuti akuchitireni chifundo.
Pakuti Yehova ndi Mulungu wachilungamo.
Ndi odala onse amene amakhulupirira Iye!
Kodi alipo Mulungu wofanana nanu,
amene amakhululukira tchimo ndi kuyiwala zolakwa
za anthu otsala amene ndi cholowa chake?
Inu simusunga mkwiyo mpaka muyaya
koma kwanu nʼkuonetsa chikondi chosasinthika.
"Ndidzalimbitsa nyumba ya Yuda
ndi kupulumutsa nyumba ya Yosefe.
Ndidzawabwezeretsa
chifukwa ndawamvera chisoni.
Adzakhala ngati kuti
sindinawakane,
chifukwa ndine Yehova Mulungu wawo
ndipo ndidzawayankha.
"Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Muziweruza molungama; muzichitirana chifundo ndi kumverana chisoni. Musamazunze akazi amasiye kapena ana amasiye, alendo kapena osauka. Musamaganizirane zoyipa mʼmitima mwanu.’
Choncho, ngati anthu osankhidwa ndi Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa kwambiri, muvale chifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa ndi kupirira.
Mukomerane mtima ndi kuchitirana chifundo wina ndi mnzake. Khululukiranani wina ndi mnzake, monga momwe Mulungu anakukhululukirani mwa Khristu.
Potsiriza, nonse khalani a mtima umodzi, omverana chisoni. Kondanani monga abale, muchitirane chifundo ndi kudzichepetsa.
Ngati wina ali ndi chuma ndipo nʼkuona mʼbale wake akusowa, koma wosamvera chisoni, kodi mwa iyeyo muli chikondi cha Mulungu?
Alemekezeke Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu, Atate achifundo chonse, Mulungu wachitonthozo chonse. Iye amatitonthoza ife mʼmavuto athu onse, kuti ifenso tithe kutonthoza amene ali pavuto lililonse ndi chitonthozo chimene ife tilandira kwa Mulungu.
Pakuti sitili ndi Mkulu wa ansembe amene sangathe kutimvera chifundo chifukwa cha zofowoka zathu. Koma tili naye amene anayesedwa mʼnjira zonse monga ife, koma sanachimwe.
Kondwani pamodzi ndi amene akukondwa ndipo lirani ndi amene akulira.
Potsiriza abale, ndikuti tsalani bwino. Yesetsani kukhala angwiro, mvetsetsani pempho langa, khalani a mtima umodzi, khalani mwamtendere. Ndipo Mulungu wachikondi ndi mtendere adzakhala nanu.