A comunhão
A comunhão cristã é dom e mandamento. Juntos somos mais fortes. A Bíblia celebra a unidade dos crentes em Cristo como antecipação do céu na terra.
Ine ndikhale mwa iwo ndipo Inu mwa Ine kuti umodzi wawo ukhale wangwiro. Choncho dziko lapansi lidzadziwa kuti Inu munandituma Ine ndipo Inu mwawakonda iwowa monga momwe Inu munandikondera Ine.
"Lamulo latsopano limene ndikukupatsani ndi lakuti: Kondanani wina ndi mnzake, monga momwe Ine ndinakonda inu. Nanunso mukondane wina ndi mnzake. Mukamakondana aliyense adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga."
Okhulupirira onse anali pamodzi ndipo aliyense ankapereka zinthu zake kuti zikhale za onse. Ankagulitsa minda yawo ndi katundu wawo, ndi kugawira kwa aliyense molingana ndi zosowa zake. Tsiku ndi tsiku ankasonkhana pamodzi pa bwalo la pa Nyumba ya Mulungu. Ankadya pamodzi mʼnyumba zawo mwasangala ndi mtima woona. Ankayamika Mulungu ndipo anthu onse ankawakomera mtima. Ndipo tsiku ndi tsiku Ambuye ankawonjezera ena pa chiwerengero cha olandira chipulumutso.
Tikukulalikirani chimene tinachiona ndi kumva, kuti inuyo muyanjane nafe. Kuyanjana kwathu, tikuyanjana ndi Atate ndiponso ndi Mwana wawo, Yesu Khristu.
Mmene timadziwira chikondi chenicheni ndi umu: Yesu anapereka moyo wake chifukwa cha ife. Ndipo nafenso tiyenera kupereka miyoyo yathu chifukwa cha abale athu.
Choncho limbikitsanani wina ndi mnzake ndi kuthandizana kukula mu mzimu, monga momwe mukuchitira.
ndiponso kuti tonsefe tilimbikitsane mʼchikhulupiriro wina ndi mnzake.
Tiyeni tisaleke kusonkhana kwathu pamodzi monga mmene ena amachitira, koma tizilimbikitsana makamaka poona kuti tsiku la Ambuye layandikira.
Chitsulo chimanoledwa ndi chitsulo chinzake,
chomwechonso munthu amanoledwa ndi munthu mnzake.
Thandizanani kusenza zolemetsa zanu, ndipo mʼnjira imeneyi mudzakwanitsa lamulo la Khristu.
Nʼchifukwa chake ngati tapeza mpata, tiyenera kuchitira zabwino anthu onse, makamaka amene ndi a banja la okhulupirira.
Kukhala awiri nʼkwabwino kuposa kukhala wekha,
chifukwa ntchito ya anthu awiri ili ndi phindu:
Ngati winayo agwa,
mnzakeyo adzamudzutsa.
Koma tsoka kwa munthu amene agwa
ndipo alibe wina woti amudzutse!
Komanso ngati anthu awiri agona malo amodzi, adzafunditsana.
Koma nanga mmodzi angadzifunditse yekha?
Munthu mmodzi angathe kugonjetsedwa,
koma anthu awiri akhoza kudziteteza.
Chingwe cha maulusi atatu sichidukirapo.