Publicidade

Consolador

Por Bíblia Online

O Espírito Santo é o Consolador prometido por Jesus. Ele consola os aflitos, fortalece os fracos e nos assegura que nunca estaremos sós.

O Consolador prometido

Jesus prometeu: Eu rogarei ao Pai e Ele vos dará outro Consolador para que fique convosco para sempre.

Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani Nkhoswe ina kuti izikhala nanu nthawi zonse.

Ine sindikusiyani nokha kuti mukhale ana amasiye. Ine ndidzabweranso kwa inu.

Koma Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamutumiza mʼdzina langa adzakuphunzitsani zinthu zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndinakuwuzani.

Ntchito ya Mzimu Woyera

"Nkhoswe ikadzabwera imene Ine ndidzakutumizireni kuchokera kwa Atate, ndiye Mzimu Woyera wachoonadi amene achokera kwa Atate, Iyeyo adzandichitira umboni Ine.

Komatu ndakuwuzani zoona. Ine ndikuti kuli bwino kwa inu kuti ndichoke. Ngati sindichoka, Nkhosweyo sidzabwera kwa inu, koma ngati Ine ndipita, ndidzamutumiza kwa inu.

Consolo divino

Bendito seja o Deus de toda consolação. Ele nos consola em toda tribulação e enxuga toda lágrima de nossos olhos.

Mulungu Mwini Chitonthozo

Alemekezeke Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu, Atate achifundo chonse, Mulungu wachitonthozo chonse. Iye amatitonthoza ife mʼmavuto athu onse, kuti ifenso tithe kutonthoza amene ali pavuto lililonse ndi chitonthozo chimene ife tilandira kwa Mulungu.

Pakuti monga momwe tili mʼmasautso pamodzi ndi Khristu, momwemonso Khristu amatitonthoza kwambiri.

Mulungu amene amapereka kupirira ndi chilimbikitso akupatseni maganizo amodzi pakati panu monga inu mukutsatira Khristu Yesu,

Pamene nkhawa inakula mʼkati mwanga,

chitonthozo chanu chinabweretsa chimwemwe mʼmoyo mwanga.

Ndili mʼmasautso anga ndinalirira Yehova,

ndipo Iye anayankha pondichotsa mʼmasautsowo.

Iwowa sadzamvanso njala,

sadzamvanso ludzu,

dzuwa kapena kutentha kulikonse

sikudzawawotcha.

Pakuti Mwana Wankhosa amene ali pakati pa mpando waufumu

adzakhala mʼbusa wawo.

Iye adzawatsogolera ku akasupe a madzi amoyo.

Ndipo Mulungu adzawapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo.’ "

Yehova akuti, "Ndinetu amene ndimakutonthozani mtima.

Chifukwa chiyani mukuopa munthu woti adzafa?

Mukuopa munthu woti monga udzu sadzakhalitsa.

Odala ndi amene ali achisoni,

chifukwa adzatonthozedwa.

Seja o primeiro
Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-28_14-13-17-