Publicidade

Consolo

Por Bíblia Online

O consolo de Deus é bálsamo para a alma ferida. Ele nos conforta em todas as tribulações para que possamos consolar outros com o mesmo consolo divino.

Deus consola

Ainda que eu ande pelo vale da sombra da morte, não temerei mal algum. O Senhor consola, guia e está sempre presente.

Ngakhale ndiyende

mʼchigwa cha mdima wakuda bii,

sindidzaopa choyipa,

pakuti Inu muli ndi ine;

chibonga chanu ndi ndodo yanu

zimanditonthoza.

Salimo la Davide.

Yehova ndiye kuwunika kwanga ndi chipulumutso changa;

ndidzaopa yani?

Yehova ndi linga la moyo wanga;

ndidzachita mantha ndi yani?

Chitonthozo changa pa masautso anga ndi ichi:

lonjezo lanu limasunga moyo wanga.

Chikondi chanu chosasinthika chikhale chitonthozo changa,

molingana ndi lonjezo lanu kwa mtumiki wanu.

Yehova ndi wabwino kwa amene amayembekezera Iye,

kwa munthu amene amafunafuna Iyeyo;

Confiança na aflição

Eu sei que o meu Redentor vive. Deus é força e escudo — mesmo na tribulação, Ele nos sustenta e consola.

Koma ndikudziwa kuti mpulumutsi wanga ali ndi moyo,

ndipo pa nthawi yomaliza adzabwera kudzanditeteza.

Ndipo khungu langa litatha nʼkuwonongeka,

mʼthupi langa lomweli ndidzamuona Mulungu.

Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga;

ndidzamudalira ndipo sindidzachita mantha.

Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga;

Iye wakhala chipulumutso changa."

Yehova mwini ndiye akukutsogolerani ndipo adzakhala nanu. Sadzakusiyani kapena kukutayani. Usachite mantha ndiponso usataye mtima."

Paja ndinakulamula kuti ukhale wamphamvu ndi wolimba mtima. Choncho usamachite mantha kapena kutaya mtima popeza Ine Yehova Mulungu wako ndidzakhala nawe kulikonse kumene udzapite."

Kotero ife tikunena molimba mtima kuti,

"Ambuye ndiye mthandizi wanga;

sindidzachita mantha. Munthu angandichitenji ine?"

Odala ndi amene ali achisoni,

chifukwa adzatonthozedwa.

Koma ine ndikudikira Yehova mwachiyembekezo,

ndikudikira Mulungu Mpulumutsi wanga;

Mulungu wanga adzamvetsera.

Ine sindikusiyani nokha kuti mukhale ana amasiye. Ine ndidzabweranso kwa inu.

Seja o primeiro
Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-28_14-13-17-