Publicidade

Conversão

Por Bíblia Online

A conversão é o ato de se voltar para Deus — arrependendo-se do pecado e abraçando a graça. É o início de uma vida nova, transformada pelo amor de Cristo.

Arrependei-vos

Arrependei-vos e convertei-vos para que os vossos pecados sejam apagados. A conversão começa com a mudança de mente e coração.

Chifukwa chake, lapani, bwererani kwa Mulungu, kuti machimo anu afafanizidwe, kuti nthawi ya kutsitsimuka ibwere kuchokera kwa Ambuye,

Petro anawayankha kuti, "Lapani ndipo mubatizidwe aliyense wa inu, mʼdzina la Yesu Khristu kuti machimo anu akhululukidwe. Ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.

Nthawi imene anthu sankadziwa, Mulungu anawalekerera koma tsopano akulamulira kuti anthu onse, kulikonse atembenuke mtima.

Kuyambira nthawi imeneyo, Yesu anayamba kulalikira nati, "Tembenukani mtima ufumu wakumwamba wayandikira."

Onetsani chipatso cha kutembenuka mtima.

"Nthawi yafika, ufumu wa Mulungu wayandikira. Tembenukani mtima ndi kukhulupirira Uthenga Wabwino!"

O amor de Deus converte

Céu se alegra por um pecador que se arrepende. Deus não deseja a morte do ímpio, mas que se converta e viva.

Ine ndikukuwuzani kuti momwemonso kudzakhala chikondwerero chachikulu kumwamba chifukwa cha wochimwa mmodzi amene watembenuka mtima kusiyana ndi anthu olungama 99 amene ali otembenuka mtima kale."

Momwemonso, Ine ndikukuwuzani kuti angelo a Mulungu amakondwera kwambiri chifukwa cha wochimwa mmodzi amene watembenuka mtima."

Ine sindinabwere kudzayitana olungama, koma ochimwa kuti atembenuke mtima."

Ine sindikondwera ndi imfa ya munthu aliyense, akutero Ambuye Yehova. Chifukwa chake, lapani kuti mukhale ndi moyo."

" Munthu woyipa akatembenuka mtima ndi kusiya machimo amene ankachita ndi kuyamba kumvera malamulo anga ndi kumachita zolungama ndi zokhulupirika, ndiye kuti adzakhala ndi moyo. Sadzafa ayi.

Munthu Wochimwa Adzafa

Yehova anandiyankhula nati: "Kodi anthu inu mumatanthauza chiyani mukamabwerezabwereza kunena mwambi uwu wokhudza dziko la Israeli kuti:

" Nkhuyu zodya akulu zimapota

ndi ana omwe?’ "

"Ndithu pali Ine wamoyo, akutero Ambuye Yehova, simudzanenanso mwambi umenewu mu Israeli. Pakuti moyo uliwonse ndi wanga. Moyo wa abambo ndi wanga, wamwananso ndi wanga. Munthu wochimwa ndi amene adzafe.

"Tiyerekeze kuti pali munthu wolungama

amene amachita zolungama ndi zolondola.

Iye sadyera nawo pa mapiri a chipembedzo

kapena kupembedza mafano a Aisraeli.

Iye sayipitsa mkazi wa mnzake

kapena kugonana ndi mkazi pamene akusamba.

Iye sapondereza munthu wina aliyense,

koma amabwezera wangongole nʼchigwiriro chake.

Iye salanda zinthu za osauka,

koma amapereka chakudya kwa anthu anjala,

ndipo amapereka zovala kwa anthu ausiwa.

Iye sakongoletsa ndalama mwa katapira,

kapena kulandira chiwongoladzanja chachikulu.

Amadziletsa kuchita zoyipa

ndipo sakondera poweruza milandu.

Iye amatsatira malangizo anga,

ndipo amasunga malamulo anga mokhulupirika.

Munthu ameneyo ndi wolungama;

iye adzakhala ndithu ndi moyo,

akutero Ambuye Yehova.

"Tiyerekeze kuti munthu wolungama chotere wabala mwana chimbalangondo amene amakhalira kupha anthu ndi kuchita zinthu zina zotere. Iye nʼkumachita zinthu zimene ngakhale abambo ake sanachitepo.

"Amadyera nawo ku mapiri achipembedzo.

Amayipitsa mkazi wa mnzake.

Iye amapondereza munthu wosauka ndi wosowa.

Amalanda zinthu za osauka.

Sabweza chikole cha munthu wa ngongole.

Iye amatembenukira ku mafano

nachita zonyansa.

Iye amakongoletsa mwa katapira ndipo amalandira chiwongoladzanja chachikulu.

Kodi munthu wotereyu nʼkukhala ndi moyo? Ayi ndithu! Chifukwa wachita zinthu zonyansa zonsezi, adzaphedwa ndipo adzalandira chilango chomuyenera.

"Tsono tiyerekeze kuti munthu woyipa uyu wabala mwana amene amaona machimo onse amene abambo ake ankachita. Ngakhale amaona koma osatsanzira ntchito zake zoyipazo.

"Sadyera nawo pa mapiri achipembedzo.

Sapembedza mafano a ku Israeli.

Sayipitsa mkazi wa mnzake.

Sapondereza munthu wina aliyense.

Satenga chikole akabwereketsa chinthu. Salanda zinthu za osauka.

Salanda zinthu za munthu.

Amapereka chakudya kwa anthu anjala.

Amapereka zovala kwa anthu aumphawi.

Amadziletsa kuchita zoyipa.

Sakongoletsa kuti apezepo phindu. Salandira chiwongoladzanja.

Amasunga malangizo anga ndi kumvera malamulo anga.

Munthu wotereyo sadzafa chifukwa cha machimo a abambo ake. Adzakhala ndi moyo ndithu. Koma abambo ake, popeza kuti anazunza anthu ena ndi kubera mʼbale wawo ndiponso popeza kuti sanachitire zabwino anansi ake, adzafera machimo ake omwe.

"Mwina inu mukhoza kufunsa kuti, Nʼchifukwa chiyani mwana salangidwa chifukwa cha kulakwa kwa abambo ake? Ayi, mwanayo adzakhala ndi moyo chifukwa ankachita zolungama ndi zolondola ndipo ankasamala kumvera malamulo anga onse. Munthu wochimwa ndiye amene adzafe. Mwana sadzapezeka wolakwa chifukwa cha abambo ake, kapena abambo kupezeka wolakwa chifukwa cha mwana wawo. Chilungamo cha munthu wolungama ndicho chidzamupulutse, ndipo kuyipa kwa munthu wochimwa ndiko kudzamuwonongetse.

" Munthu woyipa akatembenuka mtima ndi kusiya machimo amene ankachita ndi kuyamba kumvera malamulo anga ndi kumachita zolungama ndi zokhulupirika, ndiye kuti adzakhala ndi moyo. Sadzafa ayi. Zoyipa zake zonse zidzakhululukidwa. Chifukwa cha zinthu zolungama zimene anazichita adzakhala ndi moyo. Kodi Ine ndimakondwera ndi imfa ya munthu woyipa? Ayi, ndimakondwera pamene woyipa watembenuka mtima kuti akhale ndi moyo. Akutero Ambuye Yehova.

" Koma ngati munthu wolungama apatuka kusiya zachilungamo ndi kuyamba kuchita tchimo ndi zonyansa za mtundu uliwonse zimene amachita anthu oyipa, kodi munthu wotereyu nʼkukhala ndi moyo? Ayi ndithu, zolungama zake zonse sizidzakumbukiridwa. Iye adzayenera kufa chifukwa cha machimo amene anachita.

"Komabe inu mukunena kuti, Zimene Ambuye amachita ndi zopanda chilungamo.Tamvani tsono inu Aisraeli: Kodi zochita zanga ndizo zosalungama? Kodi si zochita zanu zimene ndi zosalungama? Ngati munthu wolungama atembenuka kusiya chilungamo chake ndi kuchita tchimo, iye adzafa chifukwa cha tchimolo. Koma ngati munthu woyipa aleka zoyipa zake zimene anazichita ndi kuyamba kuchita zimene ndi zolungama ndi zolondola, iye adzapulumutsa moyo wake. Popeza waganizira za zolakwa zonse ankachita ndipo wazileka, iye adzakhala ndi moyo ndithu; sadzafa. Komabe Aisraeli akunena kuti, Zimene Ambuye amachita ndi zopanda chilungamo.Kodi zochita zanga ndizo zopanda chilungamo, inu Aisraeli? Kodi si zochita zanu zimene ndi zopanda chilungamo?

"Chifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: inu Aisraeli, Ine ndidzakuweruzani aliyense wa inu molingana ndi ntchito zake. Lapani! Lekani zoyipa zanu kuti musawonongeke nazo. Tayani zolakwa zanu zonse zimene munandichimwira nazo ndipo khalani ndi mtima watsopano ndi mzimu watsopano. Kodi muferanji inu Aisraeli? Ine sindikondwera ndi imfa ya munthu aliyense, akutero Ambuye Yehova. Chifukwa chake, lapani kuti mukhale ndi moyo."

Ambuye sazengereza kuchita zimene analonjeza, monga ena amaganizira. Iwo akukulezerani mtima, sakufuna kuti aliyense awonongeke, koma akufuna kuti aliyense alape.

Transformação

Voltai-vos para mim e sereis salvos! Rasgai o coração e não as vestes. A verdadeira conversão transforma o interior.

Woyipa asiye makhalidwe ake oyipa,

ndipo wosalungama asinthe maganizo ake oyipa.

Abwerere kwa Yehova, ndipo adzamuchitira chifundo,

ndi kwa Mulungu wathu, pakuti adzamukhululukira koposa.

Ndachotsa zolakwa zako ngati mitambo,

ndi machimo ako ngati nkhungu ya mmawa.

Bwerera kwa Ine,

popeza ndakupulumutsa."

Ngʼambani Mtima Wanu

"Ngakhale tsopano,

bwererani kwa Ine ndi mtima wanu wonse

posala zakudya ndi kukhetsa misozi," akutero Yehova.

Ngʼambani mtima wanu

osati zovala zanu.

Bwererani kwa Yehova Mulungu wanu,

pakuti Iye ndi wokoma mtima ndi wachifundo,

wosakwiya msanga ndi wachikondi chochuluka,

ndipo amaleka kubweretsa mavuto.

ngati anthu anga, amene amatchedwa ndi dzina langa adzichepetsa ndi kupemphera ndi kufunafuna nkhope yanga, nasiya njira zawo zoyipa, pamenepo Ine ndidzamva kumwamba ndipo ndidzakhululuka tchimo lawo ndi kuchiritsa dziko lawo.

Hezekiya Achita Chikondwerero cha Paska

Hezekiya anatumiza uthenga mʼdziko lonse la Israeli ndi ku Yuda ndiponso analemba makalata ku Efereimu ndi Manase, oyitana anthu kuti abwere ku Nyumba ya Yehova ku Yerusalemu kudzakondwerera Paska wa Yehova, Mulungu wa Israeli. Mfumu ndi akuluakulu ake pamodzi ndi anthu onse a mu Yerusalemu anagwirizana kuti akondwerere Paska pa mwezi wachiwiri. Iwo sanathe kukondwerera pa nthawi yake chifukwa si ansembe ambiri amene anadziyeretsa ndiponso anthu anali asanasonkhane mu Yerusalemu. Chikonzerochi chinaoneka kuti chinali chabwino kwa mfumu pamodzi ndi anthu onse. Iwo anagwirizana zoti alengeze mu Israeli monse kuyambira ku Beeriseba mpaka ku Dani, kuyitana anthu kuti abwere ku Yerusalemu ndi kudzakondwerera Paska wa Yehova, Mulungu wa Israeli. Si ambiri amene ankachita chikondwererochi monga momwe kunalembedwera.

Molamulidwa ndi mfumu, amithenga anapita mu Israeli yense ndi Yuda ndi makalata ochokera kwa mfumu ndi kwa akuluakulu ake, olembedwa kuti,

"Aisraeli bwererani kwa Yehova, Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Israeli, kuti abwerere kwa inu amene mwatsala, amene mwapulumuka mʼdzanja la mafumu a ku Asiriya. Musakhale ngati makolo anu ndi abale anu, amene anali osakhulupirika kwa Yehova Mulungu wa makolo awo kotero kuti anawachititsa kuti akhale chinthu chochititsa mantha, monga mukuoneramu. Musawumitse khosi monga anachitira makolo anu, Gonjerani Yehova. Bwerani ku malo opatulika, amene anawapatula kwamuyaya. Tumikirani Yehova Mulungu wanu kuti mkwiyo wake ukuchokereni. Ngati inu mubwerera kwa Yehova, pamenepo abale anu ndi ana anu adzachitiridwa chifundo ndi amene anawagwira ukapolo ndipo adzabwereranso ku dziko lino pakuti Yehova, Mulungu wanu ndi wokoma mtima ndi wachifundo. Iye sadzakufulatirani ngati inuyo mubwerera kwa Iye."

Amithenga aja anapita mzinda ndi mzinda wa ku Efereimu ndi Manase mpaka ku Zebuloni, koma anthu anawanyoza ndi kuwachita chipongwe. Komabe anthu ena a ku Aseri, Manase ndi Zebuloni anadzichepetsa ndipo anapita ku Yerusalemu. Dzanja la Mulungu linalinso pa anthu a ku Yuda, kuwapatsa mtima umodzi wochita zimene mfumu ndi akuluakulu ake analamula potsata mawu a Yehova.

Gulu lalikulu la anthu linasonkhana mu Yerusalemu kudzachita chikondwerero cha Buledi Wopanda Yisiti pa mwezi wachiwiri. Anachotsa mu Yerusalemu maguwa ofukizira lubani ndipo anakawaponya mʼchigwa cha Kidroni.

Iwo anapha mwana wankhosa wa Paska pa tsiku la 14 la mwezi wachiwiri. Ansembe ndi Alevi anachita manyazi ndipo anadziyeretsa ndi kubweretsa nsembe zopsereza ku Nyumba ya Yehova. Ndipo anakhala mʼmalo awo a nthawi zonse potsatira zolembedwa mʼmalamulo a Mose munthu wa Mulungu. Ansembe anawaza magazi amene anawapatsa Alevi. Popeza ambiri mʼgululo anali asanadziyeretse, Alevi anapha ana ankhosa a Paska a iwo amene, mwa mwambo, anali osayeretsedwa ndipo sakanatha kupereka ana ankhosa awo kwa Yehova. Ngakhale kuti ambiri mwa anthu ochokera ku Efereimu, Manase, Isakara ndi Zebuloni sanadziyeretse okha, komabe anadya Paska motsutsana ndi zimene zinalembedwa. Koma Hezekiya anawapempherera, kunena kuti, "Yehova wabwino, khululukirani aliyense amene wayika mtima wake kufunafuna Yehova, Mulungu wa makolo ake, ngakhale ali wosayeretsedwa molingana ndi malamulo a malo opatulika." Ndipo Yehova anamvera Hezekiya ndipo anachiritsa anthuwo.

Aisraeli amene anali mu Yerusalemu anachita chikondwerero cha Buledi Wopanda Yisiti kwa masiku asanu ndi awiri akusangalala kwambiri, pamene Alevi ndi ansembe amayimbira Yehova tsiku lililonse, akuyimbira zida zamatamando za Yehova.

Hezekiya anayankhula molimbikitsa Alevi onse amene anaonetsa kumvetsa bwino za kutumikira Yehova. Kwa masiku asanu ndi awiri anadya gawo lawo ndi kupereka nsembe zachiyanjano ndi kutamanda Yehova, Mulungu wa makolo awo.

Ndipo msonkhano wonse unagwirizana zopitiriza chikondwerero kwa masiku ena asanu ndi awiri. Kotero kwa masiku ena asanu ndi awiri anachita chikondwererocho mosangalala. Hezekiya mfumu ya Yuda anapereka ngʼombe zamphongo 1,000 ndi nkhosa ndi mbuzi 7,000 ku msonkhanoko ndipo akuluakulu ake anapereka ngʼombe zamphongo 1,000, nkhosa ndi mbuzi 10,000. Ansembe ambiri anadziyeretsa. Gulu lonse la ku Yuda linasangalala, pamodzi ndi ansembe ndi Alevi ndi onse amene anasonkhana ochokera ku Israeli, kuphatikizanso alendo amene anachokera ku Israeli ndi amene amakhala ku Yuda. Munali chikondwerero chachikulu mu Yerusalemu, pakuti kuyambira masiku a Solomoni mwana wa Davide mfumu ya Israeli sizinachitikepo zotere mu Yerusalemu. Ansembe ndi Alevi anayimirira kudalitsa anthu, ndipo Mulungu anawamvera pakuti pemphero lawo linafika kumwamba, malo ake oyera.

Yuda Abwerera kwa Yehova

Mwezi wachisanu ndi chitatu, mʼchaka chachiwiri cha ulamuliro wa Dariyo, Yehova anayankhula ndi mneneri Zekariya mwana wa Berekiya, mwana wa Ido, kuti:

"Yehova anakwiya kwambiri ndi makolo anu. Choncho awuze anthuwa kuti, Yehova Wamphamvuzonse akuti, Bwererani kwa Ine,akutero Yehova Wamphamvuzonse. Ndipo Ine ndidzabwerera kwa inu,akutero Yehova Wamphamvuzonse. Musakhale ngati makolo anu, amene aneneri akale anawalalikira kuti: Yehova Wamphamvuzonse akuti, Tsopano lekani njira zanu zoyipa ndi machitidwe anu oyipawo.Koma iwo sanamvere kapena kulabadira za Ine, akutero Yehova. Kodi makolo anuwo ali kuti tsopano? Nanga aneneri, kodi amakhalapo mpaka muyaya? Kodi mawu anga ndi malangizo anga, amene ndinawawuza atumiki anga aneneri, suja anawachitira makolo anu?

"Tsono iwo analapa ndi kunena kuti, Yehova Wamphamvuzonse watichitira zomwe zikuyenera njira zathu ndi machitidwe athu, monga anatsimikiza kuti adzachita.’ "

Munthu Pakati pa Mitengo ya Mchisu

Tsiku la 24 la mwezi wa 11, mwezi wa Sebati, chaka chachiwiri cha ulamuliro wa Dariyo, Yehova anayankhula ndi Zekariya mwana wa Berekiya, mwana wa Ido.

Nthawi ya usiku ndinaona masomphenya. Ndinaona munthu atakwera pa kavalo wofiira. Iye anayima pakati pa mitengo ya mchisu mʼchigwa. Kumbuyo kwake kunali akavalo ofiira, akhofi ndi oyera.

Ine ndinafunsa kuti, "Mbuye wanga, kodi zimenezi ndi chiyani?"

Mngelo amene amayankhula nane anayankha kuti, "Ndidzakuonetsa kuti zimenezi ndi chiyani."

Pamenepo munthu amene anayima pakati pa mitengo ya mchisu anafotokoza kuti, "Amenewa ndiwo amene Yehova wawatuma kuti ayendere dziko lonse lapansi."

Ndipo okwera pa akavalo enawo anafotokoza kwa mngelo wa Yehova, amene anayima pakati pa mitengo ya mchisu kuti, "Ife tayendera dziko lonse lapansi ndipo tapeza kuti dziko lonselo lili pa bata ndi mtendere."

Tsono mngelo wa Yehova anati, "Yehova Wamphamvuzonse, kodi mpaka liti mudzakhala osaonetsa chifundo chanu kwa Yerusalemu ndi mizinda ya Yuda, amene mwawakwiyira kwa zaka izi 70?" Choncho Yehova anayankhula mawu abwino ndi achitonthozo kwa mngelo amene ankayankhula nane.

Pamenepo mngelo amene ankayankhula nane anati, "Lengeza mawu awa: Yehova Wamphamvuzonse akuti, Ine ndikuchitira nsanje Yerusalemu ndi Ziyoni, koma ndakwiya kwambiri ndi anthu a mitundu ina amene akuganiza kuti ali pa mtendere. Ndinakwiyira anthu anga pangʼono pokha, koma iwo anawonjeza kuzunza anthu angawo.

"Choncho, Yehova akuti, Ndidzabwerera ku Yerusalemu ndi mtima wachifundo, nyumba yanga adzayimanganso kumeneko. Ndipo adzatenganso chingwe choyezera kuti amange Yerusalemu,akutero Yehova Wamphamvuzonse.

"Lengezanso kuti, Yehova Wamphamvuzonse akuti, Mizinda yanga idzakhalanso ndi zokoma zosefukira ndipo Yehova adzatonthoza Ziyoni ndi kusankhanso Yerusalemu.’ "

Nyanga Zinayi ndi Amisiri Azitsulo Anayi

Kenaka ndinayangʼananso, ndipo patsogolo panga panali nyanga zinayi. Ndinamufunsa mngelo amene amayankhula nane kuti, "Kodi zimenezi ndi chiyani?"

Iye anandiyankha kuti, "Izi ndi nyanga zimene zinabalalitsa Yuda, Israeli ndi Yerusalemu."

Kenaka Yehova anandionetsa amisiri azitsulo anayi. Ndinafunsa kuti, "Amisiri a zitsulowa akudzachita chiyani?"

Iye anayankha kuti, "Izi ndi nyanga zimene zinabalalitsa Yuda kotero kuti panalibe wina amene akanalimbana nazo, koma amisiri a zitsulowa abwera kudzaziopseza ndi kugwetsa nyanga zimenezi za mitundu ya anthu amene analimbana ndi dziko la Yuda ndi kubalalitsa anthu ake."

Amene ndimawakonda ndimawadzudzula ndi kuwalanga. Choncho chita changu ndipo lapa.

Choncho, iphani zilakolako za dziko lapansi mwa inu, monga: dama, zodetsa, kulakalaka zosayenera, kukhumba zoyipa ndi umbombo, pakuti umbombo ndiko kupembedza mafano.

Musapereke ziwalo zathupi lanu ku tchimo, ngati zipangizo zamakhalidwe oyipa. Mʼmalo mwake, mudzipereke kwa Mulungu, ngati amene achoka ku imfa kupita ku moyo. Ndipo mupereke ziwalo zathupi lanu ngati zipangizo zachilungamo.

Kuchita Zabwino kwa Onse

Abale, ngati munthu agwa mʼtchimo lililonse, inu amene Mzimu amakutsogolerani, mumuthandize munthuyo ndi mtima wofatsa kuti akonzekenso. Koma mukhale maso kuti inu nomwe mungayesedwe.

Choncho chotsani chizolowezi choyipa ndi khalidwe loyipa pakati panu, ndipo modzichepetsa landirani mawu amene anadzalidwa mwa inu, amene akhoza kukupulumutsani.

Seja o primeiro
Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-28_14-13-17-