Coração puro
Bem-aventurados os puros de coração, porque verão a Deus. A pureza de coração é alvo, privilégio e busca constante do cristão que deseja contemplar a face do Senhor.
Coração puro
Bem-aventurados os puros de coração. A pureza interior precede toda transformação externa e abre os olhos para ver a Deus.
Odala ndi amene ali oyera mtima,
chifukwa adzaona Mulungu.
Ndani angakwere phiri la Yehova?
Ndani angathe kuyima pa malo ake opatulika?
Iye amene ali ndi mʼmanja moyera ndi mtima woyera,
amene sapereka moyo wake kwa fano
kapena kulumbira mwachinyengo.
Iyeyo adzalandira madalitso kwa Yehova
ndipo Mulungu mpulumutsi wake adzagamula kuti alibe mlandu.
Mufulatire machimo anga
ndi kufafaniza zolakwa zanga zonse.
Mulenge mʼkati mwanga mtima woyera Inu Mulungu
ndi kukonzanso mzimu wokhazikika mwa ine.
Musandichotse pamaso panu
kapena kuchotsa Mzimu wanu Woyera mwa ine.
Mulungu ndi wabwino ndithu kwa Israeli,
kwa iwo amene ndi oyera mtima.
Purificar-se
Todo o que tem essa esperança em Cristo se purifica. O amor procede de coração puro, boa consciência e fé sincera.
Aliyense amene ali ndi chiyembekezo ichi mwa Iye adziyeretse yekha, monga Iye ali woyera.
Abale okondedwa, tsopano ndife ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Koma tikudziwa kuti Yesu akadzaonekera, tidzafanana naye, pakuti tidzamuona Iyeyo monga momwe alili. Aliyense amene ali ndi chiyembekezo ichi mwa Iye adziyeretse yekha, monga Iye ali woyera.
Cholinga cha lamuloli ndi chikondi, chomwe chimachokera mu mtima woyera, chikumbumtima chabwino ndi chikhulupiriro choona.
Thawa zilakolako zoyipa zachinyamata. Funafuna chilungamo, chikhulupiriro, chikondi ndi mtendere pamodzi ndi amene akuyitanira pa dzina la Ambuye ndi mtima osadetsedwa.
Ndipo pemphero langa ndi lakuti chikondi chanu chipitirire kukulirakulira pa chidziwitso ndi kuzama mʼmaganizo, kuti mukhoza kuzindikira chabwino koposa zonse ndi chiti kuti muthe kukhala wopanda chodetsa ndi wopanda chilema kufikira tsiku la Khristu. Ndipo moyo wanu udzakhala odzazidwa ndi chipatso cha chilungamo chimene chimachokera mwa Yesu Khristu. Pakuti zimenezi zidzapereka ulemerero ndi matamando kwa Mulungu.
Muzichita zonse mosawiringula kapena mosatsutsapo, kuti mukhale wopanda cholakwa ndi angwiro, ana a Mulungu wopanda cholakwika mu mʼbado uno wachinyengo ndi wosocheretsa. Mukatero mudzawala pakati pawo ngati nyenyezi zakumwamba powawuza mawu amoyo. Ndipo ine ndidzatha kunyadira pa tsiku la Khristu kuti sindinathamange kapena kugwira ntchito pachabe.
Tsopano mwayeretsa mitima yanu pomvera choonadi, kuti muzikondana ndi abale anu, kukondana kwenikweni kochokera pansi pa mtima.
Zochita zonse za munthu zimaoneka zabwino pamaso pake,
koma Yehova ndiye amasanthula zolinga zako.