Publicidade

Coração quebrantado

Por Bíblia Online

Deus está perto dos que têm o coração quebrantado. A Bíblia consola os aflitos: o sacrifício que Deus aceita é o espírito quebrantado e um coração contrito — jamais desprezará.

Yehova ali pafupi kwa osweka mtima

ndipo amapulumutsa iwo amene asweka mu mzimu.

Nsembe za Mulungu ndi mzimu wosweka;

mtima wosweka ndi wachisoni

Inu Mulungu simudzawunyoza.

Akutsogolera anthu osweka mtima

ndi kumanga mabala awo.

Thupi ndi mtima wanga zitha kufowoka,

koma Mulungu ndiye mphamvu ya mtima wanga

ndi cholandira changa kwamuyaya.

Pakuti Iye amene ali Wamkulu ndi Wopambanazonse,

amene alipo nthawi zonse, amene dzina lake ndi Woyerayo,

akunena kuti, "Ndimakhala pamalo aulemu ndi opatulika,

koma ndimakhalanso ndi munthu wodzichepetsa ndi wosweka mtima

kuti odzichepetsawo ndiwalimbitse

ndi kuwachotsa mantha osweka mtima.

Kodi si manja anga amene anapanga zinthu zonsezi,

motero zonsezi ndi zanga?"

Akutero Yehova.

"Koma munthu amene ndimakondwera naye ndi uyu:

amene ali wodzichepetsa ndi wosweka mtima,

ndipo amamvera mawu anga.

Uthenga Wabwino wa Yehova

Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine,

chifukwa Yehova wandidzoza

kuti ndilalikire uthenga wabwino kwa anthu osauka.

Wandituma kuti ndikatonthoze anthu osweka mtima,

ndikalengeze kwa akapolo kuti alandire ufulu

ndiponso kuti ndikamasule a mʼndende.

Wandituma kuti ndikalengeze nthawi imene Yehova adzapulumutsa anthu ake;

za tsiku limene Yehova adzalanga adani a anthu ake.

Wandituma kuti ndikatonthoze olira.

Wandituma kuti ndiwakonzere olira a ku Ziyoni,

nkhata ya maluwa yokongola

mʼmalo mwa phulusa,

ndiwapatse mafuta achikondwerero

mʼmalo mwa kulira.

Ndiwapatse chovala cha matamando

mʼmalo mwa mtima wopsinjika.

Ndipo iwo adzatchedwa mitengo ya thundu yamphamvu yachilungamo,

yoyidzala Yehova

kuti Iye mwini apezemo ulemerero wake.

"Odala ndi amene ali osauka mu mzimu,

chifukwa ufumu wakumwamba ndi wawo.

Odala ndi amene ali achisoni,

chifukwa adzatonthozedwa.

Odala ndi amene ali ofatsa,

chifukwa adzalandira dziko lapansi.

Chisoni chimene Mulungu amafuna chimabweretsa kutembenuka mtima komwe kumabweretsa chipulumutso, ndipo sichikhumudwitsa. Koma chisoni cha dziko lapansi chimabweretsa imfa. Taonani zimene chisoni chimene Mulungu amafuna chatulutsa mwa inu. Chatulutsa khama lalikulu, chakuthandizani kuti mudzikonze nokha, chakukwiyitsani kwambiri, komanso chakupatsani mantha aakulu. Chakuchititsani kuti mufune kundiona ine, mwakhudzidwa kwambiri ndipo mukufuna kuonetsetsa kuti chilungamo chachitikadi. Pa nkhani yonseyi, mwaonetsadi kuti ndinu osalakwa.

Koma anandiwuza kuti, "Chisomo changa ndi chokukwanira, pakuti mphamvu zanga zimaoneka kwathunthu mwa munthu wofowoka." Choncho ndidzadzitamandira mokondwera chifukwa cha zofowoka zanga, kuti mʼkutero mphamvu ya Khristu ikhale pa ine.

Seja o primeiro
Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-28_14-13-17-