Publicidade

Criação

Por Bíblia Online

A criação revela a glória de Deus. Céus, terra, mares e tudo o que existe testemunham o poder criador. No princípio Deus criou — e tudo era muito bom.

No princípio

No princípio criou Deus os céus e a terra. O Espírito de Deus pairava sobre as águas. E Deus disse: haja luz.

Chiyambi cha Chilengedwe

Pachiyambi Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi. Dziko lapansi linali losakonzedwa ndi lopanda kanthu. Mdima wandiweyani unakuta nyanja ndipo Mzimu wa Mulungu unkayendayenda pamwamba pa madziwo.

Zitatha izi Mulungu anati, "Tipange munthu mʼchifanizo chathu, mofanana ndi ife kuti alamulire nsomba za mʼnyanja, mbalame zamlengalenga, nyama zonse zoweta ndi zonse zokwawa za pa dziko lapansi ndi zamoyo zonse zakutchire."

Ndipo Mulungu analenga munthu mʼchifanizo chake.

Anawalengadi mʼchifanizo cha Mulungu;

analenga iwo, mwamuna ndi mkazi.

Ndipo Mulungu anadalitsa tsiku lachisanu ndi chiwiri nalipatula, chifukwa pa tsiku limeneli Iye anapumula ku ntchito yonse yolenga imene anayigwira.

Ndipo Yehova Mulungu anati, "Sibwino kuti munthu akhale yekha. Ndidzamupangira mnzake womuthandiza."

O poder criador

Pela palavra do Senhor foram feitos os céus. Tudo foi criado por Ele e para Ele — o visível e o invisível.

Ndi mawu a Yehova mayiko akumwamba anapangidwa,

zolengedwa zake ndi mpweya wa mʼkamwa mwake.

Mapiri asanabadwe,

musanalenge nʼkomwe dziko lapansi ndi dziko lonse,

kuyambira muyaya mpaka muyaya Inu ndinu Mulungu.

Bwerani, tiyeni tiwerame pomulambira,

tiyeni tigwade pamaso pa Yehova Mlengi wathu;

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

Ndikweza maso anga ku mapiri;

kodi thandizo langa limachokera kuti?

Thandizo langa limachokera kwa Yehova,

wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.

Thandizo lathu lili mʼdzina la Yehova

wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.

Lero ndiye tsiku limene Yehova walipanga;

tiyeni tikondwere ndi kusangalala nalo.

Pakuti Inu munalenga za mʼkati mwanga;

munandiwumba pamodzi mʼmimba mwa amayi anga.

Ndimakuyamikani chifukwa ndinapangidwa mochititsa mantha ndi modabwitsa;

ntchito zanu ndi zodabwitsa,

zimenezi ndimazidziwa bwino lomwe.

Criador e Sustentador

O Deus eterno não se cansa nem se fatiga. Dele, por Ele e para Ele são todas as coisas — a Ele seja a glória.

Kodi simukudziwa?

Kodi simunamve?

Yehova ndiye Mulungu wamuyaya,

ndiyenso Mlengi wa dziko lonse lapansi.

Iye sadzatopa kapena kufowoka

ndipo palibe amene angadziwe maganizo ake.

"Tsoka kwa wokangana ndi mlengi wake,

ngakhale kuti ali ngati phale chabe pakati pa mapale anzake.

Kodi dongo lingafunse munthu wowumba kuti,

Kodi ukuwumba chiyani?

Kodi ntchito yako inganene kuti,

Ulibe luso?

"Aa, inu Ambuye Yehova, munalenga dziko lakumwamba ndi dziko lapansi. Munazilenga ndi dzanja lanu lamphamvu ndipo palibe chokulakani.

Iye amene amamanga malo ake okhalamo kumwamba,

ndi kuyika maziko ake pa dziko lapansi,

Iye amene amayitana madzi a ku nyanja

ndikuwakhuthulira pa dziko lapansi,

dzina lake ndiye Yehova.

Pakuti zinthu zonse nʼzochokera kwa Iye, nʼzolengedwa ndi Iye ndipo zimabweretsa ulemerero kwa Iye.

Kwa Iye kukhale ulemerero mpaka muyaya! Ameni.

Pakuti kuyambira pamene dziko lapansi linalengedwa, zinthu zosaoneka za Mulungu, mphamvu zake zosatha ndi chikhalidwe cha umulungu, zakhala zikuoneka bwinobwino. Akhala akuzindikira poona zimene Mulungu analenga, kotero kuti anthu sangathe kuwiringula.

Pakuti chilengedwe chikudikira ndi chiyembekezo kuonetsedwa poyera kwa ana a Mulungu.

Nova criação

Se alguém está em Cristo, nova criatura é. O Criador faz novas todas as coisas — na natureza e na redenção.

Nʼchifukwa chake, ngati munthu aliyense ali mwa Khristu, ndi wolengedwa kwatsopano; zinthu zakale zapita taonani, zakhala zatsopano.

Pakuti ndife ntchito ya Mulungu, olengedwa mwa Khristu Yesu kuti tichite ntchito zabwino, zimene Mulungu anazikonzeratu kale kuti tizichite.

Iye anasankha kutibereka ife kudzera mʼmawu a choonadi, kuti pakati pa zolengedwa zake zonse, tikakhale ngati zipatso zoyamba.

Pakuti nyumba iliyonse imamangidwa ndi munthu wina, koma amene anapanga zonse ndi Mulungu.

Pakuti timakhala mwa Iye, kuyenda mwa Iye ndi kukhala moyo mwa Iye.Monga olemba ndakatulo anu ena akuti, Ife ndi zidzukulu zake.

Kenaka ndinamva mawu a cholengedwa chilichonse kumwamba, pa dziko lapansi, kunsi kwa dziko lapansi, pa nyanja ndi zonse zili mʼmenemo zikuyimba kuti,

"Kwa wokhala pa mpando waufumu ndi kwa Mwana Wankhosa,

kukhale mayamiko, ulemu, ulemerero ndi mphamvu

mpaka muyaya!"

Seja o primeiro
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-07-04_15-35-42-