Publicidade

Crianças

Por Bíblia Online

As crianças ocupam lugar especial no coração de Deus. A Bíblia instrui a educá-las, protegê-las e ensiná-las nos caminhos do Senhor desde cedo — formando gerações que temem a Deus.

Herança do Senhor

Os filhos são herança do Senhor. Eles são presentes de Deus — cada criança é um milagre e uma responsabilidade sagrada.

Ana ndiye cholowa chochokera kwa Yehova,

ana ndi mphotho yochokera kwa Iye.

Ndipo ana aamuna pa chinyamata chawo

adzakhala ngati mbewu yosamalidwa bwino,

ana athu aakazi adzakhala ngati zipilala

zosemedwa bwino, zokongoletsera nyumba yaufumu.

Pakuti Inu munalenga za mʼkati mwanga;

munandiwumba pamodzi mʼmimba mwa amayi anga.

Ndimakuyamikani chifukwa ndinapangidwa mochititsa mantha ndi modabwitsa;

ntchito zanu ndi zodabwitsa,

zimenezi ndimazidziwa bwino lomwe.

Kodi mnyamata angathe bwanji kuyeretsa mayendedwe ake?

Akawasamala potsata mawu anu.

Kodi mnyamata angathe bwanji kuyeretsa mayendedwe ake?

Akawasamala potsata mawu anu.

Bwerani ana anga, mundimvere;

ndidzakuphunzitsani kuopa Yehova.

Instruir as crianças

Instrui a criança no caminho em que deve andar. A educação cristã é mandamento repetido através de toda a Escritura.

Mwana muzimuphunzitsa njira yake,

ndipo akadzakalamba sadzachokamo.

Mwana muzimuphunzitsa njira yake,

ndipo akadzakalamba sadzachokamo.

Mwana muzimuphunzitsa njira yake,

ndipo akadzakalamba sadzachokamo.

Uchitsiru umakhala mu mtima mwa mwana,

koma ndodo yomulangira mwanayo idzachotsa uchitsiruwo.

Uchitsiru umakhala mu mtima mwa mwana,

koma ndodo yomulangira mwanayo idzachotsa uchitsiruwo.

Amene sakwapula mwana wake, ndiye kuti amamuda,

koma wokonda mwana wake sazengereza kumulanga.

Mwana wanzeru amamvera malangizo a abambo ake,

koma mwana wonyoza samamvetsera chidzudzulo.

Phindu Lina la Nzeru

Mwana wanga, usayiwale malangizo anga,

mtima wako usunge malamulo anga.

Ukatero zaka za moyo wako zidzachuluka

ndipo udzakhala pa mtendere.

Phindu Lina la Nzeru

Mwana wanga, usayiwale malangizo anga,

mtima wako usunge malamulo anga.

Paja Yehova amadzudzula amene amamukonda,

monga abambo achitira mwana amene amakondwera naye.

Ndipo abambo anandiphunzitsa ndi mawu akuti,

"Ugwiritse mawu anga pa mtima pako,

usunge malamulo anga kuti ukhale ndi moyo.

Upeze nzeru, upeze nzeru zomvetsa zinthu;

usayiwale mawu anga kapena kutayana nawo.

Disciplinar com amor

A vara e a repreensão dão sabedoria. A disciplina produz o fruto pacífico da justiça nos que são exercitados por ela.

Ndodo ndi chidzudzulo zimapatsa nzeru

koma mwana womulekerera amachititsa amayi ake manyazi.

Usaleke kumulangiza mwana;

ngati umulanga ndi chikwapu sadzafa.

Mvera abambo ako amene anakubala,

usanyoze amayi ako pamene akalamba.

Gula choonadi ndipo usachigulitse;

ugulenso nzeru, mwambo ndiponso kumvetsa zinthu bwino.

Mwana wochita ndewu ndi abambo ake ndi kuthamangitsa amayi ake,

ndi mwana wochititsa manyazi ndi wonyozetsa.

Ndi wabwino munthu wosauka amene amayenda mu ungwiro,

aposa munthu wopusa woyankhula zokhota.

Munthu wolungama amakhala ndi makhalidwe abwino;

odala ndi ana ake amene amatsanzira moyo wake.

Ngakhale mwana amadziwika ndi zochita zake,

ngati zochita zake zili zoyera ndi zoyenera.

Mwana wopusa amamvetsa chisoni abambo ake

ndipo amapweteketsa mtima amayi ake.

Zidzukulu ndiye ulemu wa anthu okalamba,

ndipo makolo ndiye ulemerero wa ana.

Zidzukulu ndiye ulemu wa anthu okalamba,

ndipo makolo ndiye ulemerero wa ana.

Chitsiru chimanyoza mwambo wa abambo ake,

koma wochenjera amasamala chidzudzulo.

Mwana wanzeru amakondweretsa abambo ake,

koma mwana wopusa amanyoza amayi ake.

Amene amasunga malamulo ndi mwana wozindikira zinthu,

koma amene amayenda ndi anthu adyera amachititsa manyazi abambo ake.

Malangizo kuti Asunge Nzeru
Malangizo kwa Achinyamata

Mwana wanga, mvera malangizo a abambo ako

ndipo usakane mawu okuwongolera a amayi ako.

Ali ngati sangamutu yokongola ya maluwa pamutu pako

ndiponso ali ngati mkanda mʼkhosi mwako.

"Ndiye tsono ana inu, ndimvereni;

odala anthu amene amasunga njira zanga.

Mverani malangizo anga kuti mukhale ndi nzeru;

musanyozere mawu anga.

Obediência e promessa

Filhos, obedecei a vossos pais no Senhor. Honra a teu pai e tua mãe para que viva muito tempo sobre a terra.

Ana ndi Makolo Awo

Inu ana, mverani makolo anu mwa Ambuye, pakuti zimenezi ndi zoyenera. "Lemekeza abambo ndi amayi ako." Limeneli ndi lamulo loyamba lokhala ndi lonjezo. Ngati ulemekeza abambo ako ndi amayi ako, "zinthu zidzakuyendera bwino ndipo udzasangalala ndi moyo wautali pa dziko lapansi."

Abambo musakwiyitse ana anu; mʼmalo mwake, muwalere mʼchiphunzitso ndi mʼchilangizo cha Ambuye.

Abambo musakwiyitse ana anu; mʼmalo mwake, muwalere mʼchiphunzitso ndi mʼchilangizo cha Ambuye.

Choncho, monga ana okondedwa, tsatirani chitsanzo cha Mulungu.

Inu ana, mverani makolo anu mu zonse pakuti izi zimakondweretsa Ambuye.

Inu abambo, musakwiyitse ana anu, kuti angataye mtima.

Malamulo amene ndakupatsani lero ayenera kukhala mu mtima mwanu. Muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu. Muzikamba za malamulowa pamene muli mʼnyumba zanu, pamene mukuyenda mʼnjira, pamene mukugona ndi pamene mukudzuka.

Muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu. Muzikamba za malamulowa pamene muli mʼnyumba zanu, pamene mukuyenda mʼnjira, pamene mukugona ndi pamene mukudzuka.

Sungani malangizo ake ndi malamulo ake amene ndikukupatsani lero lino, kuti zikuyendereni bwino inu ndi ana anu kutsogoloko, ndi kuti mukhalitse mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kwa nthawi zonse.

Onetsetsani kuti muzimvera mawu onsewa amene ndikukupatsani kuti zinthu zizikuyenderani bwino nthawi zonse inu ndi ana anu chifukwa mudzakhala mukuchita zabwino ndi zoyenera pamaso pa Yehova Mulungu wanu.

iye anawawuza kuti, "Muwasunge bwino mu mtima mwanu, mawu onse amene lero lino ndikukuwuzani kuti mudzawuze ana anu, kuti adzamvere mosamalitsa mawu onse a malamulo amenewa. Mawuwa sikuti ndi mawu achabe kwa inu. Mawuwa ndi moyo wanu. Mukawamvera mudzakhala ndi moyo wautali mʼdziko limene mukukalitenga kukhala lanu mukawoloka Yorodani."

Crianças e o reino

Deixai vir a mim as crianças. Jesus honrou as crianças como modelo de fé e humildade para todo o seu povo.

Yesu anati, "Lolani ana abwere kwa Ine, ndipo musawaletse pakuti ufumu wakumwamba ndi wa iwo onga anawa."

Yesu anati, "Lolani ana abwere kwa Ine, ndipo musawaletse pakuti ufumu wakumwamba ndi wa iwo onga anawa."

Wamkulu mu Ufumu Wakumwamba

Pa nthawi imeneyo ophunzira anabwera kwa Yesu ndipo anamufunsa kuti, "Wamkulu woposa onse ndani mu ufumu wakumwamba?"

Iye anayitana kamwana kakangʼono ndi kukayimiritsa pakati pawo. Ndipo Iye anati, "Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati simusintha ndi kukhala ngati tiana tatingʼono, simudzalowa konse mu ufumu wakumwamba. Chifukwa chake, aliyense amene adzichepetsa yekha ngati kamwana aka, ameneyo ndiye wamkulu koposa onse mu ufumu wakumwamba.

Ndipo Iye anati, "Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati simusintha ndi kukhala ngati tiana tatingʼono, simudzalowa konse mu ufumu wakumwamba. Chifukwa chake, aliyense amene adzichepetsa yekha ngati kamwana aka, ameneyo ndiye wamkulu koposa onse mu ufumu wakumwamba. Ndipo aliyense amene alandira kamwana kakangʼono ngati aka mu dzina langa, alandira Ine.

Fanizo la Nkhosa Yotayika

"Onetsetsani kuti musanyoze mmodzi wa anawa. Pakuti ndikuwuzani kuti angelo awo kumwamba amakhala pamaso pa Atate anga akumwamba nthawi zonse."

Goli la Khristu

Pa nthawi imeneyo Yesu anati, "Ine ndikukuyamikani Inu Atate Ambuye akumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa Inu mwawabisira zinthu izi anzeru ndi ophunzira ndi kuziwulula kwa ana angʼonoangʼono.

Ndi odala amene amabweretsa mtendere,

chifukwa adzatchedwa ana a Mulungu.

Yesu Adalitsa Ana

Anthu anabweretsa ana kwa Yesu kuti awadalitse, koma ophunzira anawadzudzula. Pamene Yesu anaona zimenezi anayipidwa. Anati kwa iwo, "Lolani ana abwere kwa Ine, ndipo musawaletse, pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa onga awa.

Anatenga kamwana nakayimiritsa pakati pawo ndipo anawawuza kuti, "Aliyense wolandira mmodzi wa ana angʼono awa mʼdzina langa alandira Ine; ndipo aliyense wolandira Ine salandira Ine koma amene anandituma."

Ndipo Yesu anakula mu nzeru, msinkhu ndi chisomo cha Mulungu ndi anthu.

Yesu Abwezeretsa Petro

Iwo atamaliza kudya chakudya chammawa, Yesu anati kwa Simoni Petro, "Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikonda Ine kuposa mmene amandikondera awa?"

Iye anati, "Inde Ambuye, Inu mukudziwa kuti Ine ndimakukondani."

Yesu anati, "Samala ana ankhosa anga."

Identidade e crescimento

Somos filhos de Deus pelo Espírito de adoção. Crescer em Cristo é amadurecer em fé, obediência e amor ao próximo.

Koma kwa onse amene anamulandira Iye, kwa amene anakhulupirira mʼdzina lake, Iye anawapatsa mphamvu yokhala ana a Mulungu;

Onse amene amatsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu ndi ana a Mulungu.

Mzimu amene inu munalandira samakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha, koma Mzimu amakusandutsani ana. Ndipo mwa Iye ife timafuwula kuti, "Abba, Atate."

Mzimu mwini amavomerezana ndi mzimu wathu kuti ife ndife ana a Mulungu.

Pakuti chilengedwe chikudikira ndi chiyembekezo kuonetsedwa poyera kwa ana a Mulungu.

Ana a Mulungu

Nonse ndinu ana a Mulungu kudzera mʼchikhulupiriro mwa Khristu Yesu, pakuti nonse amene munalumikizana ndi Khristu mu ubatizo munavala Khristu.

Taonani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate anatikonda nacho, kuti titchedwe ana a Mulungu! Ndipo nʼchimene ife tili! Nʼchifukwa chake dziko lapansi silitidziwa chifukwa silinamudziwe Iye.

Abale okondedwa, tsopano ndife ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Koma tikudziwa kuti Yesu akadzaonekera, tidzafanana naye, pakuti tidzamuona Iyeyo monga momwe alili. Aliyense amene ali ndi chiyembekezo ichi mwa Iye adziyeretse yekha, monga Iye ali woyera.

Inu ana okondedwa, ndikukulemberani

popeza kuti machimo anu akhululukidwa chifukwa cha dzina la Yesu.

Ana okondedwa, dzisungeni bwino, osapembedza mafano.

Akhale wodziwa kusamala bwino banja lake ndi kulera ana ake bwino, kuti akhale omvera ndi aulemu weniweni.

Ngati wina sasamalira abale ake, makamaka a mʼbanja mwake mwenimweni, ameneyo wakana chikhulupiriro ndipo ndi woyipa kuposa wosakhulupirira.

Mulungu Amalanga Ana ake

Kodi mwayiwala mawu olimbitsa mtima aja, amene Mulungu anayankhula kwa inu ngati ana ake? Mawuwo ndi awa:

"Mwana wanga, usapeputse kulanga kwa Ambuye

ndipo usataye mtima pamene akukudzudzula.

Chifukwa Ambuye amadzudzula amene amawakonda

ndipo amalanga aliyense amene amamulandira."

Pamene mukupirira masautso monga chilango, Mulungu achitira inu monga ana ake. Kodi ndi mwana wotani amene abambo ake samulanga? Ngati inu simulangidwa, komatu aliyense amalangidwa, ndiye kuti sindinu ana enieni koma amʼchigololo. Komanso, tonsefe tinali ndi abambo athu otibala amene amatilanga ndipo timawapatsa ulemu. Nanga kodi sitidzagonjera Atate a mizimu yathu kuti tikhale ndi moyo?

Palibe chilango chimene chimaoneka kuti ndi chabwino pa nthawiyo, komatu chowawa. Koma pambuyo pake, chimabweretsa chipatso chachilungamo ndi mtendere kwa iwo amene aleredwa mwa njira imeneyi.

Iwo anayankha kuti, "Khulupirira Ambuye Yesu ndipo udzapulumuka, iwe ndi a mʼbanja lako."

Thawa zilakolako zoyipa zachinyamata. Funafuna chilungamo, chikhulupiriro, chikondi ndi mtendere pamodzi ndi amene akuyitanira pa dzina la Ambuye ndi mtima osadetsedwa.

Ndipo zinthu zimene unamva ine ndikuziyankhula pamaso pa mboni zambiri, uziphunzitse kwa anthu odalirika amene akaphunzitsenso ena.

Transmitir a fé

Contaremos à geração vindoura os louvores do Senhor. O legado de fé é o maior presente que damos aos nossos filhos.

Yehova adzaphunzitsa ana ako onse,

ndipo ana ako adzakhala ndi mtendere wochuluka.

Yehova adzaphunzitsa ana ako onse,

ndipo ana ako adzakhala ndi mtendere wochuluka.

Amoyo, amoyo okha ndiwo amakutamandani,

monga mmene ndikuchitira ine lero lino;

abambo amawuza ana awo za

kukhulupirika kwanu.

"Kodi amayi angathe kuyiwala mwana wawo wakubere

ndi kusachitira chifundo mwana amene anabereka iwo eni?

Ngakhale iye angathe kuyiwala,

Ine sindidzakuyiwala iwe!

Taona, ndakulemba iwe mʼzikhantho zanga;

makoma ako ndimawaona nthawi zonse.

Popeza anthu ankachita mantha, tsono ndinawawuza anthu olemekezeka, akuluakulu ndiponso anthu onse kuti, "Musawaope. Kumbukirani kuti Ambuye ndi wamkulu ndipo ndi woopsa. Choncho menyerani nkhondo abale anu, ana aamuna ndi aakazi, akazi anu ndi nyumba zanu."

Yehova Ayitana Samueli

Samueli ankatumikira Yehova moyangʼaniridwa ndi Eli. Masiku amenewo mawu a Yehova sankamveka pafupipafupi. Kuona zinthu mʼmasomphenya sikunkachitikanso kawirikawiri.

Palibe chondikondweretsa kwambiri kuposa kumva kuti ana anga akukhala mʼchoonadi.

Palibe chondikondweretsa kwambiri kuposa kumva kuti ana anga akukhala mʼchoonadi.

Sitidzabisira ana awo,

tidzafotokozera mʼbado wotsatira

ntchito zotamandika za Yehova,

mphamvu zake, ndi zozizwitsa zimene Iye wachita.

Iye anapereka mawu wodzichitira umboni kwa Yakobo

ndi kukhazikitsa lamulo mu Israeli,

zimene analamulira makolo athu

kuphunzitsa ana awo,

kotero kuti mʼbado wotsatira uthe kuzidziwa,

ngakhale ana amene sanabadwe,

ndi kuti iwo akafotokozere ana awonso.

Choncho iwo adzakhulupirira Mulungu

ndipo sadzayiwala ntchito zake

koma adzasunga malamulo ake.

Seja o primeiro
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-07-04_15-35-42-