Publicidade

Cura

Por Bíblia Online

A cura é promessa e poder de Deus. Jesus curou toda enfermidade e todo mal. As Escrituras declaram que pelas suas pisaduras fomos sarados — cura do corpo, da alma e do espírito.

Pelas suas pisaduras

Ele foi ferido pelas nossas transgressões e moído pelas nossas iniquidades. Pelas suas pisaduras fomos sarados.

Koma iye analasidwa chifukwa cha zolakwa zathu,

ndipo anamuzunza chifukwa cha zoyipa zathu;

iye analangidwa kuti ife tikhale ndi mtendere,

ndipo ndi mabala ake ife tinachiritsidwa.

Koma iye analasidwa chifukwa cha zolakwa zathu,

ndipo anamuzunza chifukwa cha zoyipa zathu;

iye analangidwa kuti ife tikhale ndi mtendere,

ndipo ndi mabala ake ife tinachiritsidwa.

Ndithudi, iye anamva zowawa mʼmalo mwa ife;

ndipo anasautsidwa mʼmalo mwathu.

Koma ife tinkaganiza kuti ndi Mulungu amene akumulanga,

kumukantha ndi kumusautsa.

Koma iye analasidwa chifukwa cha zolakwa zathu,

ndipo anamuzunza chifukwa cha zoyipa zathu;

iye analangidwa kuti ife tikhale ndi mtendere,

ndipo ndi mabala ake ife tinachiritsidwa.

Iye mwini anasenza machimo athu mʼthupi lake pa mtanda, kuti ife tife kutchimo ndi kukhala ndi moyo potsata chilungamo, ndipo ndi mabala ake munachiritsidwa.

Iye mwini anasenza machimo athu mʼthupi lake pa mtanda, kuti ife tife kutchimo ndi kukhala ndi moyo potsata chilungamo, ndipo ndi mabala ake munachiritsidwa.

Jesus, o curador

Jesus percorreu cidades e aldeias curando toda doença. Ele deu autoridade aos discípulos para curar enfermos.

Antchito ndi Ochepa

Yesu anayendayenda mʼmizinda yonse ndi mʼmidzi, kuphunzitsa mʼmasunagoge awo, nalalikira Uthenga Wabwino wa ufumu ndi kuchiritsa nthenda zawo zonse ndi zofowoka za mʼmatupi mwawo.

Chiritsani odwala, ukitsani akufa, chiritsani akhate, tulutsani ziwanda. Munalandira kwaulere, perekani kwaulere.

Chiritsani odwala, ukitsani akufa, chiritsani akhate, tulutsani ziwanda. Munalandira kwaulere, perekani kwaulere.

Yesu Atuma Ophunzira Ake

Yesu anayitana ophunzira ake khumi ndi awiri ndipo anawapatsa ulamuliro otulutsa mizimu yoyipa ndi kuchiritsa nthenda iliyonse ndi zofowoka zilizonse.

Yesu atamva, anati, "Munthu wamoyo safuna singʼanga ayi, koma wodwala.

Yesu Achiritsa Odwala

Yesu anayendayenda mu Galileya kuphunzitsa mʼmasunagoge awo, nalalikira Uthenga Wabwino wa ufumu ndi kuchiritsa matenda onse pakati pa anthu.

Chiritsani odwala amene ali kumeneko ndipo muwawuze kuti, Ufumu wa Mulungu wayandikira.

"Mzimu wa Ambuye ali pa Ine;

chifukwa wandidzoza

kuti ndilalikire Uthenga Wabwino kwa osauka.

Wandituma kuti ndilalikire kwa a mʼndende kuti amasulidwe

ndi kwa osaona kuti apenyenso,

kumasulidwa kwa osautsidwa,

Iye atawaona, anati, "Pitani kadzionetseni nokha kwa ansembe." Ndipo pamene iwo ankapita, anachiritsidwa.

Mayi Wokhota Msana Achiritsidwa pa Sabata

Pa Sabata Yesu ankaphunzitsa mʼsunagoge ina, ndipo momwemo munali mayi amene anali ndi mzimu woyipa umene unamudwalitsa zaka 18. Iye anali wokhota msana ndipo samatha kuweramuka ndi pangʼono pomwe. Yesu atamuona anamuyitana kutsogolo ndipo anati kwa iye, "Amayi, mwamasulidwa ku mavuto." Kenaka anasanjika manja ake pa iye, ndipo nthawi yomweyo anawongoka nayamika Mulungu.

Chifukwa cha kuyipidwa kuti Yesu anachiritsa pa Sabata, wolamulira sunagoge anati kwa anthu, "Pali masiku asanu ndi limodzi ogwira ntchito. Choncho bwerani kuti mudzachiritsidwe masiku amenewo osati pa Sabata."

Ambuye anamuyankha kuti, "Iwe wachiphamaso! Kodi nonsenu simumasula pa Sabata ngʼombe zanu kapena bulu kumuchotsa mʼkhola ndi kupita naye kukamupatsa madzi? Nanga mayiyu, amene ndi mwana wa Abrahamu, ndipo anamangidwa ndi Satana zaka 18, kodi siwoyenera kuti amasulidwe msinga imeneyi pa tsiku la Sabata?"

Atanena izi, onse omutsutsa anachititsidwa manyazi, koma anthu anakondwera ndi zodabwitsa zonse zimene Iye anazichita.

Atamva zimenezi, Yesu anati kwa Yairo, "Usachite mantha, ingokhulupirira basi ndipo adzachiritsidwa."

Anati kwa iye, "Mwana wamkazi, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Pita mu mtendere ndipo khala womasulidwa ku mavuto ako."

Yesu anati, " Ngati mungathe!Zinthu zonse ndi zotheka kwa iye amene akhulupirira."

Yesu anati, "Pita, chikhulupiriro chako chakuchiritsa!" Nthawi yomweyo anapenya, nʼkumatsatira Yesu pa ulendowo.

Tsono zizindikiro izi zidzawatsata amene adzakhulupirira: Mʼdzina langa adzatulutsa ziwanda; adzayankhula malilime atsopano; adzanyamula njoka ndi manja awo; ndipo pamene adzamwa mankhwala akupha, sadzawapweteka nʼpangʼonongʼono pomwe; adzasanjika manja awo pa anthu odwala ndipo odwalawo adzachira."

Petro anati kwa iye, "Eneya, Yesu Khristu akukuchiritsa iwe, dzuka ndipo yalula mphasa yako." Nthawi yomweyo Eneya anayimirira.

Eu sou o Senhor que te sara

Eu sou o Senhor que te sara. Ele perdoa todas as iniquidades e sara todas as enfermidades — com bondade e misericórdia.

Yehova anati, "Ngati inu mudzamvetsa bwino mawu anga, kuchita zolungama, kumvera malamulo anga ndi kusamalitsa zimene ndikukuwuzani ndiye kuti Ine sindidzayika pa inu matenda amene ndinayika pa anthu a ku Igupto popeza ndine Yehova amene ndimakuchiritsani."

Muzipembedza Yehova Mulungu wanu ndipo adzakudalitsani ndi chakudya ndi madzi ndiponso ndidzachotsa nthenda pakati panu.

Amene amakhululuka machimo ako onse

ndi kuchiritsa nthenda zako zonse,

Amene amakhululuka machimo ako onse

ndi kuchiritsa nthenda zako zonse,

Akutsogolera anthu osweka mtima

ndi kumanga mabala awo.

Akutsogolera anthu osweka mtima

ndi kumanga mabala awo.

Iye anatumiza mawu ake ndi kuwachiritsa;

anawalanditsa ku manda.

Iye anatumiza mawu ake ndi kuwachiritsa;

anawalanditsa ku manda.

Inu Yehova Mulungu wanga ndinapempha kwa Inu thandizo

ndipo Inu munandichiritsa.

Yehova amatsekula maso anthu osaona,

Yehova amadzutsa onse amene awerama pansi,

Yehova amakonda anthu olungama.

Yehova adzamuthandiza pamene akudwala

ndipo adzamuchiritsa pa bedi lake la matenda.

Munthu wolungama atha kukhala ndi mavuto ambiri,

Koma Yehova amamulanditsa ku mavuto onsewo,

Cura e restauração

Eu te restaurarei e sararei as tuas feridas, diz o Senhor. A oração da fé salvará o enfermo e o Senhor o levantará.

Ndidzachiza matenda anu

ndi kupoletsa zilonda zanu,

akutero Yehova,

chifukwa mukutchedwa anthu otayika.

Amati, ndi anthu a ku Ziyoni awa amene alibe wowasamala.’ "

" Pambuyo pake mzindawu ndidzawupatsanso moyo ndi kuwuchiritsa; ndidzachiritsa anthu anga ndi kuwapatsa chitetezo ndi mtendere weniweni.

Inu Yehova, chiritseni, ndipo ndidzachira;

pulumutseni ndipo ndidzapulumuka,

chifukwa ndinu amene ndimakutamandani.

Kodi alipo wina mwa inu akudwala? Ayitane akulu ampingo kuti adzamupempherere ndi kumudzoza mafuta mʼdzina la Ambuye. Ndipo pemphero lachikhulupiriro lidzachiritsa munthu wodwalayo ndipo Ambuye adzamuutsa. Ngati wachimwa adzakhululukidwa.

Kodi alipo wina mwa inu akudwala? Ayitane akulu ampingo kuti adzamupempherere ndi kumudzoza mafuta mʼdzina la Ambuye. Ndipo pemphero lachikhulupiriro lidzachiritsa munthu wodwalayo ndipo Ambuye adzamuutsa. Ngati wachimwa adzakhululukidwa. Choncho, ululiranani machimo anu ndi kupemphererana wina ndi mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama ndi lamphamvu ndipo limagwira ntchito.

Choncho, ululiranani machimo anu ndi kupemphererana wina ndi mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama ndi lamphamvu ndipo limagwira ntchito.

kapena chifukwa cha mavumbulutso aakulu kuposa awa. Choncho, kuti ndisadzitukumule, ndinayikidwa minga mʼthupi langa, wamthenga wa Satana, kuti adzindizunza. Katatu konse ndinapempha Ambuye kuti andichotsere. Koma anandiwuza kuti, "Chisomo changa ndi chokukwanira, pakuti mphamvu zanga zimaoneka kwathunthu mwa munthu wofowoka." Choncho ndidzadzitamandira mokondwera chifukwa cha zofowoka zanga, kuti mʼkutero mphamvu ya Khristu ikhale pa ine.

ngati anthu anga, amene amatchedwa ndi dzina langa adzichepetsa ndi kupemphera ndi kufunafuna nkhope yanga, nasiya njira zawo zoyipa, pamenepo Ine ndidzamva kumwamba ndipo ndidzakhululuka tchimo lawo ndi kuchiritsa dziko lawo.

"Bwerera, kamuwuze Hezekiya mtsogoleri wa anthu anga kuti, Yehova Mulungu wa Davide kholo lako akuti: Ndamva pemphero lako ndipo misozi yako ndayiona ndipo ndidzakuchiritsa. Tsiku lachitatu kuchokera lero udzapita ku Nyumba ya Yehova.

Promessas e esperança

O Senhor dá forças aos cansados. O sol da justiça se levantará com salvação nas suas asas.

Iye amalimbitsa ofowoka

ndipo otopa amawawonjezera mphamvu.

Koma inu amene mumaopa dzina langa, dzuwa lachilungamo lidzakutulukirani lili ndi kuwala kokuchiritsani. Ndipo inu mudzatuluka ndi kulumphalumpha ngati ana angʼombe amene atulutsidwa mʼkhola.

Koma inu amene mumaopa dzina langa, dzuwa lachilungamo lidzakutulukirani lili ndi kuwala kokuchiritsani. Ndipo inu mudzatuluka ndi kulumphalumpha ngati ana angʼombe amene atulutsidwa mʼkhola.

Mtima wosangalala uli ngati mankhwala abwino,

koma mtima wokhumudwa umafowoketsa mafupa.

Muziyenda mʼnjira zowongoka, kuti iwo amene akukutsatirani ngakhale ndi olumala ndi ofowoka asapunthwe ndi kugwa koma adzilimbikitsidwa.

Seja o primeiro
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-07-04_15-35-42-