Publicidade

Tomar uma decisão

Por Bíblia Online

Tomar decisões com sabedoria é um dos maiores desafios da vida. A Bíblia nos ensina a buscar a Deus em oração, na Palavra e no conselho, confiando que Ele dirige os nossos passos.

Buscar a Deus

Se algum de vós tem falta de sabedoria, peça a Deus. Ele dá generosamente e sem repreensão a todos os que pedem.

Ngati wina pakati panu akusowa nzeru, apemphe kwa Mulungu amene amapereka kwa onse mwaulere ndi mosatonzera, ndipo adzapatsidwa.

Ife timalimba mtima tikamafika pamaso pa Mulungu, popeza kuti ngati tipempha kanthu kalikonse monga mwa chifuniro chake, amatimvera.

Koma tikavomereza machimo athu, Iye ndi wokhulupirika ndi wolungama ndipo adzatikhululukira machimo athu, nadzatiyeretsa ndi kutichotsera chosalungama chilichonse.

Uzikhulupirira Yehova ndi mtima wako wonse

ndipo usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu.

Pa zochita zako zonse uvomereze kuti Mulungu alipo,

ndipo Iye adzawongola njira zako.

Pa zochita zako zonse uvomereze kuti Mulungu alipo,

ndipo Iye adzawongola njira zako.

Pakuti Ine ndikudziwa zimene ndinakukonzerani," akutero Yehova, "ndimalingalira zabwino zokhazokha za inu osati zoyipa, ayi. Ndimalingalira zinthu zokupatsani chiyembekezo chenicheni pa za mʼtsogolo.

Conselho e direção

Onde não há conselho os planos se frustam. Toda Escritura é útil para nos guiar nas decisões da vida.

Pakasoweka uphungu mtundu wa anthu umagwa;

koma pakakhala aphungu ambiri pamakhalanso chipulumutso.

Maere amaponyedwa pa mfunga,

koma ndiye Yehova amene amalongosola zonse.

Munthu wokonda kukhala yekha amafunafuna zomukomera yekha;

iye amatsutsana ndi malangizo onse anzeru.

Chitsiru chilibe chidwi chomvetsa zinthu,

koma chimakondwera ndi kuyankhula maganizo ake okha.

Kuyipa mtima kukabwera, manyozonso amabwera.

Manyazi amabwera pamodzi ndi kunyozeka.

Mawu a munthu ali ngati madzi akuya,

kasupe wa nzeru ndiye mtsinje wotumphuka.

Si kwabwino kukondera munthu woyipa pa milandu;

kapena kupondereza munthu wosalakwa.

Mawu a chitsiru amautsa mkangano;

pakamwa pake pamayitana mkwapulo.

Pakamwa pa chitsiru ndipo pamabweretsa chiwonongeko chake,

ndipo milomo yake ili ngati msampha wa moyo wake.

Mawu a miseche ali ngati chakudya chokoma;

amalowa mʼmimba mwa munthu.

Munthu waulesi pa ntchito yake

ali pachibale ndi munthu amene amawononga zinthu.

Dzina la Yehova lili ngati nsanja yolimba;

wolungama amathawiramo napulumuka.

Chuma cha anthu olemera chili ngati mzinda wake wolimba;

chili ngati khoma lalitali limene amaganiza kuti limutchinjiriza.

Chiwonongeko chisanafike, mtima wa munthu umakhala wonyada,

koma ulemu umatsatira kudzichepetsa.

Ukayankha usanamvetse bwino nkhani,

umenewo ndi uchitsiru ndipo umachita manyazi.

Mtima wa munthu utha kupirira pa matenda,

koma munthu akataya mtima ndani angathe kumulimbitsanso.

Malemba onse anawalembetsa ndi Mulungu, ndipo othandiza pophunzitsa, podzudzula, pokonza cholakwika ndi polangiza za chilungamo

kuti munthu wa Mulungu akonzekere bwino lomwe kugwira ntchito iliyonse yabwino.

Atafika ku malire a Musiya, anayesa kulowa ku Bituniya, koma Mzimu wa Yesu sunawalole kutero.

Barnaba ndi Saulo Atumidwa ndi Mpingo

Mu mpingo wa ku Antiokeya munali aneneri ndi aphunzitsi awa: Barnaba, Simeoni, Lukia wa ku Kurene, Manayeni (amene analeredwa pamodzi ndi mfumu Herode), ndiponso Saulo. Iwo pamene ankapembedza Ambuye ndi kusala kudya, Mzimu Woyera anati, "Mundipatulire Barnaba ndi Saulo kuti akagwire ntchito imene ndinawayitanira." Ndipo atasala kudya ndi kupemphera anasanjika manja awo pa iwo nawatumiza.

Confiar e seguir

Seja o que for que façais, fazei tudo para a glória de Deus. O sábio ouve a Deus antes de agir.

Nʼchifukwa chake chilichonse mungadye kapena kumwa, kapena chimene mungachite, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.

Yesu Chitsanzo Chathu

Tsono popeza ifenso tazunguliridwa ndi gulu lalikulu la mboni, tiyeni titaye chilichonse chimene chimatitchinga, makamaka tchimo limene limatikola mosavuta, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu.

Ku Gibiyoniko Yehova anaonekera kwa Solomoni mʼmaloto usiku, ndipo Mulungu anati, "Pempha chilichonse chimene ukufuna ndipo ndidzakupatsa."

Solomoni anayankha kuti, "Inu munaonetsa kukoma mtima kwanu kwakukulu kwa kapolo wanu, abambo anga Davide, chifukwa anali wokhulupirika pamaso panu, wolungama mtima ndiponso wa mtima wangwiro. Inu mukupitirizabe kukoma mtima kwanu kwakukulu kwa iye ndipo mwamupatsa mwana kuti akhale pa mpando wake waufumu lero lino.

"Tsopano Inu Yehova Mulungu wanga, mtumiki wanune mwandiyika kukhala mfumu mʼmalo mwa abambo anga Davide. Komatu ndine mwana wamngʼono ndipo sindidziwa kagwiridwe kake ka ntchito yangayi. Mtumiki wanu ali pakati pa anthu amene munawasankha, mtundu waukulu, anthu ochuluka kwambiri osatheka kuwawerenga. Choncho mupatseni mtumiki wanu nzeru zolamulira anthu anu ndi kuti azitha kusiyanitsa pakati pa chabwino ndi choyipa. Pakuti ndani amene angathe kulamulira anthu anu ochulukawa?"

Ambuye anakondwera kuti Solomoni anapempha zimenezi. Tsono Mulungu anati kwa Solomoni, "Popeza wapempha zinthu zimenezi osati moyo wautali kapena chuma chako kapena imfa ya adani ako koma nzeru zolamulira anthu mwachilungamo, Ine ndidzakuchitira zimene wapempha. Ndidzakupatsa mtima wanzeru ndi wozindikira zinthu, kotero kuti sipanakhalepo wina wofanana nawe ndipo sipadzapezekanso wina wonga iwe pambuyo pako.

Mkazi wake anati kwa iye, "Kodi ukuwumirirabe kukhala wangwiro? Tukwana Mulungu kuti ufe!"

Yobu anayankha kuti, "Ukuyankhula ngati mkazi wopusa. Kodi tidzalandira zokoma zokhazokha kwa Mulungu, osalandiranso zowawa?"

Mu zonsezi, Yobu sanachimwe pa zimene anayankhula.

Seja o primeiro
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-07-04_15-35-42-