Dependência
A dependência de Deus é o caminho da verdadeira liberdade. Sem Cristo, nada podemos fazer. Mas em Deus encontramos sustento, direção e força para todo desafio.
Sem Ele nada podemos
Sem mim nada podeis fazer. O cristão que se desconecta da videira seca — mas o que permanece dá muito fruto.
"Ine ndine mpesa; inu ndinu nthambi zake. Ngati munthu akhala mwa Ine ndi Ine mwa iye, adzabereka zipatso zambiri; popanda Ine simungathe kuchita kanthu.
Ndisungeni Inu Mulungu,
pakuti ine ndimathawira kwa Inu.
Ndayika Yehova patsogolo panga nthawi zonse.
Popeza Iyeyo ali kudzanja langa lamanja,
sindidzagwedezeka.
Yehova akapanda kumanga nyumba,
omanga nyumbayo agwira ntchito pachabe.
Yehova akapanda kulondera mzinda,
mlonda akanangolondera pachabe.
Sanalande dziko ndi lupanga lawo,
si mkono wawo umene unawabweretsera chigonjetso,
koma ndi dzanja lanu lamanja, mkono wanu ndi kuwala kwa nkhope yanu,
pakuti munawakonda.
Yehova adzakumenyerani nkhondo. Inu mungokhala chete."
Depender do Senhor
Confia no Senhor de todo o coração e não te estribes no teu próprio entendimento. Em todos os caminhos o reconhece.
Uzikhulupirira Yehova ndi mtima wako wonse
ndipo usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu.
Pa zochita zako zonse uvomereze kuti Mulungu alipo,
ndipo Iye adzawongola njira zako.
Mtima wa munthu umalingalira zochita,
koma Yehova ndiye amakhazikitsa njira zake.
Munthu amakonzekera zambiri mu mtima mwake,
koma cholinga cha Yehova ndiye chidzachitike.
Mdalitso wa Yehova ndiwo umabweretsa chuma,
ntchito za munthu siziwonjezerapo kanthu.
Thupi ndi mtima wanga zitha kufowoka,
koma Mulungu ndiye mphamvu ya mtima wanga
ndi cholandira changa kwamuyaya.
Tibwezereni mwakale Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse
nkhope yanu itiwalire
kuti tipulumutsidwe.
Ndikweza maso anga ku mapiri;
kodi thandizo langa limachokera kuti?
Thandizo langa limachokera kwa Yehova,
wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Sadzalola kuti phazi lako literereke;
Iye amene amakusunga sadzawodzera.
Ndikanena kuti, "Phazi langa likuterereka,"
chikondi chanu, Inu Yehova, chimandichirikiza.
Ndili mʼmasautso anga ndinalirira Yehova,
ndipo Iye anayankha pondichotsa mʼmasautsowo.
Yehova ndiye mʼbusa wanga, sindidzasowa kanthu.
Amandigoneka pa msipu wobiriwira,
amanditsogolera ku madzi akumwa abwino,
Contentamento e confiança
Aprendi a viver contente em toda situação. A dependência de Deus nos livra da ansiedade e nos firma na paz.
Sindikunena izi chifukwa choti ndikusowa thandizo, poti ine ndaphunzira kukhala wokwaniritsidwa ndi zimene ndili nazo.
Pakuti Ine Yehova, ndine Mulungu wako,
amene ndikukugwira dzanja lako lamanja
ndipo ndikuti, usaope;
ndidzakuthandiza.
Iye amalimbitsa ofowoka
ndipo otopa amawawonjezera mphamvu.
Muyanjane wina ndi mnzake. Musakhale onyada, koma lolani kuyanjana ndi anthu wamba. Musaganize kuti mumadziwa zonse.
Pakuti monga aliyense wa ife ali ndi thupi limodzi koma ziwalo zambiri, ziwalozi sizili ndi ntchito yofanana. Momwemonso mwa Khristu ife amene tili ambiri tipanga thupi limodzi ndipo chiwalo chilichonse ndi cholumikizika ku chinzake.
Ndipo anthu amene amalamulidwa ndi khalidwe lauchimo sangathe kukondweretsa Mulungu.
Chifukwa chake musadere nkhawa ndi za mawa, popeza tsiku lililonse lili ndi zovuta zake zokwanira.
"Koma ine ndine yani, ndipo anthu anga ndani, kuti tikupatsani mowolowamanja motere? Zinthu zonse zimachokera kwa Inu, ndipo ife takupatsani zomwe zimachokera mʼdzanja lanu.