Publicidade

Desejos

Por Bíblia Online

Os desejos revelam o que há no coração. A Bíblia nos ensina a purificar nossos desejos, submeter a carne ao espírito e buscar as coisas que são de cima.

Desejos da carne

A carne milita contra o espírito. O cristão é chamado a vigiar, resistir e não satisfazer os desejos da natureza pecaminosa.

Choncho ine ndikuti, mulole kuti Mzimu akutsogolereni ndipo simudzachita zofuna za thupi lanu la uchimo.

Moyo mwa Mzimu Woyera

Inu abale, Mulungu anakuyitanani kuti mukhale mfulu. Koma musagwiritse ntchito ufulu wanuwo kuchita zoyipa zachikhalidwe cha uchimo cha thupi lanu, koma mutumikirane wina ndi mnzake mwachikondi.

Kuchita Zabwino kwa Onse

Abale, ngati munthu agwa mʼtchimo lililonse, inu amene Mzimu amakutsogolerani, mumuthandize munthuyo ndi mtima wofatsa kuti akonzekenso. Koma mukhale maso kuti inu nomwe mungayesedwe.

Khalani maso ndi kupemphera kuti musagwe mʼmayesero. Mzimu ukufuna koma thupi ndi lofowoka."

Ndipo musatitengere kokatiyesa;

koma mutipulumutse kwa woyipayo.

Khalani odziretsa ndi atcheru. Mdani wanu mdierekezi amayendayenda monga mkango wobangula kufunafuna wina kuti amumeze.

Pakuti zonse za mʼdziko lapansi, zilakolako za thupi, zinthu zimene maso amakhumbira ndiponso kuyandikira zinthu za moyo uno, zonsezi sizichokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi.

Dziko lapansi likupita pamodzi ndi zilakolako zake, koma amene amachita chifuniro cha Mulungu amakhalapo mpaka muyaya.

Choncho, iphani zilakolako za dziko lapansi mwa inu, monga: dama, zodetsa, kulakalaka zosayenera, kukhumba zoyipa ndi umbombo, pakuti umbombo ndiko kupembedza mafano.

Purificar os desejos

Guarda o teu coração. Das profundezas do interior do homem saem os desejos — bons ou maus, conforme o coração.

"Ndinachita pangano ndi maso anga

kuti sindidzapenya namwali momusirira.

Kodi munthu angathe kuyenda pa makala amoto

mapazi ake osapserera?

Tsiku lonse anthu oyipa amasirira zambiri,

koma anthu olungama amapereka mowolowamanja.

Ukangoti wachipeza chumacho uwona posachedwa kuti palibepo.

Chumacho chimachita ngati chamera mapiko mwadzidzidzi

ndi kuwuluka kunka kumwamba ngati chiwombankhanga.

Pakuti kukonda ndalama ndiye muzu wa zoyipa za mitundu yonse. Anthu ena ofunitsitsa ndalama, asochera ndipo asiya njira yachikhulupiriro ndipo adzitengera zowawitsa zambiri.

Chigololo

Inu mumati, "Ine ndili ndi ufulu wochita chilichonse." Komatu si zonse zimene nʼzothandiza. "Ndili ndi ufulu wochita chilichonse." Koma sindidzagonjetsedwa ndi chilichonse.

Koma chifukwa choti chigololo chawanda, mwamuna aliyense akhale naye mkazi wakewake ndipo mkazi aliyense akhale naye mwamuna wakewake.

Palibe mayesero amene mwakumana nawo oposa amene anthu ena onse anakumana nawo. Mulungu ngokhulupirika; sadzalola kuti inu muyesedwe koposa muyeso umene mutha kupirira. Koma pamene mwayesedwa, Iyenso adzakupatsani njira yopambanira mayeserowo.

Desejos santos

Como a corça deseja as correntes de água, minha alma suspira por ti, ó Deus. Os desejos do Espírito produzem vida e paz.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya ana a Kora.

Monga mbawala ipuma wefuwefu kufunafuna mitsinje yamadzi,

kotero moyo wanga upuma wefuwefu kufunafuna Inu Mulungu.

Inde Yehova, timayenda mʼnjira zanu zolungama,

ife timayembekezera Inu;

mitima yathu imakhumba kukumbukira

ndi kulemekeza dzina lanu.

Mwa ulemerero ndi ubwino wakewo, anatipatsa malonjezo opambana kwambiri ndi a mtengowapatali. Amenewa ndi malonjezo amene amakuthandizani kulandira nawo moyo wa Mulungu, titapulumuka ku chiwonongeko chimene chili mʼdziko lapansi chifukwa cha zilakolako zoyipa.

Mumalakalaka zinthu koma simuzipeza, choncho mumapha. Mumasirira zinthu koma simutha kuzipeza zimene mukufuna, choncho mumakangana ndi kumenyana. Mulibe zinthuzo chifukwa simupempha kwa Mulungu.

Munthu akayesedwa asanene kuti, "Mulungu akundiyesa." Pakuti Mulungu sangayesedwe ndi choyipa kapena Iyeyo kuyesa munthu aliyense.

Kulimbana ndi Mphamvu za Tchimo

Nanga ife tinene chiyani? Kodi Malamulo ndi oyipa? Ayi. Nʼkosatheka! Kunena zoona, popanda Malamulo, ine sindikanazindikira tchimo. Pakuti sindikanadziwa kuti kusirira ndi tchimo ngati Malamulo sakananena kuti, "Usasirire."

Ukwati muziwulemekeza nonse, ndipo mwamuna ndi mkazi azikhala wokhulupirika, pakuti anthu adama ndi achigololo Mulungu adzawalanga.

Pakuti kumene kuli chuma chako, mtima wako udzakhala komweko.

Seja o primeiro
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-07-04_15-35-42-