Despedida
As despedidas na Bíblia são momentos sagrados de bênção, oração e confiança em Deus. Mesmo na separação, os filhos de Deus se despedem com fé, carinho e esperança de reencontro.
Despedidas bíblicas
Paulo se despediu dos anciãos de Éfeso com oração e lágrimas. As despedidas entre irmãos são marcadas por afeto e fé.
Atanena zimenezi, anagwada pansi pamodzi ndi ena onse, napemphera. Onse analira pamene amamukumbatira ndi kupsompsona. Chimene chinamvetsa chisoni kwambiri ndi mawu ake akuti sadzaonanso nkhope yake. Kenaka iwo anamuperekeza ku sitima yapamadzi.
Paulo Apita ku Makedoniya ndi ku Grisi
Litatha phokoso, Paulo anayitanitsa ophunzira ndipo atawalimbikitsa anawatsanzika ndipo ananyamuka kupita ku Makedoniya.
Atakhala kumeneko kwa kanthawi, abale aja anatsanzikana nawo mwamtendere kuti abwerere kwa amene anawatuma.
Paulo Afunitsitsa Kuonanso Atesalonika
Koma abale, titasiyana kwa nthawi pangʼono (mʼthupi osati mʼmaganizo), tinayesetsa koposa kuti tikuoneni.
Mulungu angandichitire umboni kuti ndimakulakalakani ndi chikondi cha Khristu Yesu.
Amizades profundas
Davi e Jônatas se despediram com lágrimas e pacto de amizade. Rute se apegou a Noemi com lealdade inabalável.
Mnyamatayo anapita. Kenaka Davide anatuluka ku mbali ina ya mulu wa miyala uja, nadzigwetsa pansi ndi kugunditsa nkhope yake pansi katatu. Anapsompsona nayamba kulira onse awiri, koma Davide analira kwambiri.
Yonatani anawuza Davide kuti, "Pita mu mtendere pakuti ife awiri tinalumbira mʼdzina la Yehova kuti, ‘Yehova ndiye akhale mboni pakati pa iwe ndi ine ndiponso pakati pa zidzukulu zako ndi zidzukulu zanga kwa nthawi yonse.’ " Kenaka Davide anachoka, ndipo Yonatani anabwerera ku mzinda kuja.
Mnyamatayo anapita. Kenaka Davide anatuluka ku mbali ina ya mulu wa miyala uja, nadzigwetsa pansi ndi kugunditsa nkhope yake pansi katatu. Anapsompsona nayamba kulira onse awiri, koma Davide analira kwambiri.
Kenaka Naomi anati kwa apongozi ake awiri aja, "Bwererani, aliyense kwa amayi ake. Yehova akukomereni mtima, monga munachita ndi malemu aja ndi ine ndemwe.
"Yehova akuthandizeni kuti aliyense wa inu apeze pokhala pabwino komanso mwamuna." Kenaka anawapsompsona koma awiriwo analira mokweza.
Ndipo anati kwa Naomi, "Ife tipita nawo kwa anthu akwanu."
Koma Naomi anati, "Bwererani kwanu ana anga. Chifukwa chiyani mukufuna kupita ndi ine? Kodi ine ndingaberekenso ana ena kuti akhale amuna anu? Bwererani kwanu ana anga muzipita kwanu. Ine ndakalamba kwambiri kotero kuti sindingakwatiwenso. Ngakhale ndikananena kuti ndili nacho chikhulupiriro, ngakhale ndikanakhala ndi mwamuna usiku uno, ndipo nʼkubala ana aamuna, kodi inu mukanadikira kuti akule? Kodi mukanakhalabe osakwatiwa kudikira iwowo? Ayi ana anga. Zimenezi zikundiwawa kwambiri kuposa inu, chifukwa ndi ineyo amene Yehova wafuna kuti ndizunzike."
Atamva zimenezi analiranso kwambiri, ndipo Oripa anapsompsona apongozi ake nawatsanzika, koma Rute anakakamirabe.
Atamva zimenezi analiranso kwambiri, ndipo Oripa anapsompsona apongozi ake nawatsanzika, koma Rute anakakamirabe.
Kenaka Mose analola kuti mpongozi wake, Yetero anyamuke kubwerera ku dziko la kwawo.
Bênçãos de despedida
O Senhor te abençoe e te guarde. O Senhor faça resplandecer o seu rosto sobre ti e te dê a paz.
" ‘Yehova akudalitse
ndi kukusunga;
Yehova awalitse nkhope yake pa iwe,
nakuchitira chisomo;
Yehova akweze nkhope yake pa iwe,
nakupatse mtendere.’ "
Yehova adzakuteteza ku zoyipa zonse;
adzasunga moyo wako.
Yehova adzayangʼanira kutuluka kwako ndi kulowa kwako;
kuyambira tsopano mpaka muyaya.
Chisomo chikhale ndi inu nonse.
Malonje Otsiriza
Potsiriza abale, ndikuti tsalani bwino. Yesetsani kukhala angwiro, mvetsetsani pempho langa, khalani a mtima umodzi, khalani mwamtendere. Ndipo Mulungu wachikondi ndi mtendere adzakhala nanu.
Malonje Otsiriza
Potsiriza abale, ndikuti tsalani bwino. Yesetsani kukhala angwiro, mvetsetsani pempho langa, khalani a mtima umodzi, khalani mwamtendere. Ndipo Mulungu wachikondi ndi mtendere adzakhala nanu.
Lonjeranani ndi mpsopsono wachiyero. Anthu onse a Mulungu akupereka moni.
Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu, ndi chikondi cha Mulungu, ndi chiyanjano cha Mzimu Woyera zikhale ndi inu nonse.
Zida Zankhondo za Mulungu
Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye ndi mwa mphamvu zake zazikulu.
Ndipo Yoswa anawadalitsa ndi kuwalola kuti apite ndipo anapitadi ku nyumba zawo.
Koma winanso anati, "Ine ndidzakutsatani Ambuye; koma choyamba ndiloleni ndibwerere kuti ndikatsanzikane nalo banja langa."
Yesu anayankha kuti, "Munthu amene akulima ndi khasu lokokedwa nʼkumayangʼana mʼmbuyo, si woyenera kugwira ntchito mu ufumu wa Mulungu."
Pomwepo Elisa anasiya ngʼombe zake nathamangira Eliya. Iye anati, "Mundilole kuti ndikatsanzike abambo ndi amayi anga, ndipo kenaka ndidzakutsatani."
Eliya anayankha kuti, "Bwerera. Ine ndachita chiyani kwa iwe?"
Choncho Elisa anamusiya Eliyayo nabwerera kwawo. Anatenga ngʼombe zake ziwiri zapagoli nazipha. Anatenga magoli a mapulawo ake nasonkhera moto kuphikira nyamayo ndipo anayipereka kwa anthu kuti adye. Ndipo ananyamuka natsatira Eliya ndi kukhala mtumiki wake.