Publicidade

O Deus do impossível

Por Bíblia Online

Deus é o Deus do impossível. Para Ele não há nada difícil demais. O que parece impossível aos olhos humanos é perfeitamente possível para o Criador do universo.

Nada é impossível

Para Deus nada é impossível. Ele faz infinitamente mais do que podemos pedir ou imaginar — esse é o nosso Deus.

Yesu anawayangʼana iwo nati, "Ndi anthu, izi nʼzosatheka, koma ndi Mulungu zinthu zonse zimatheka."

Yesu anawayangʼana ndipo anati, "Kwa munthu zimenezi nʼzosatheka, koma osati ndi Mulungu; zinthu zonse zimatheka ndi Mulungu."

Yesu anayankha kuti, "Zinthu zosatheka ndi anthu zimatheka ndi Mulungu."

Mariya anafunsa mngeloyo kuti, "Izi zingatheke bwanji popeza ine sindidziwa mwamuna?"

Mngelo anayankha kuti, "Mzimu Woyera adzabwera pa iwe ndipo mphamvu ya Wammwambamwamba idzakuphimba, ndipo Woyerayo amene adzabadwe adzatchedwa Mwana wa Mulungu. Ngakhale Elizabeti mʼbale wako adzakhala ndi mwana mu ukalamba wake ndipo iye amene amati ndi wosabereka, uno mwezi wake wachisanu ndi chimodzi. Pakuti palibe chinthu chosatheka ndi Mulungu."

Mariya anayankha kuti, "Ine ndine mtumiki wa Ambuye. Zikhale kwa ine monga mwanenera."

Ndipo Yehova anati kwa Abrahamu, "Nʼchifukwa chiyani Sara anaseka nʼkumati, Moti ine nʼkudzakhaladi ndi mwana mmene ndakalambiramu?Kodi pali chimene chikhoza kumukanika Yehova? Pa nthawi yake, ngati yomwe ino chaka chamawa ndidzabweranso, ndipo Sara adzabala mwana wamwamuna."

"Ndikudziwa kuti Inu mungathe kuchita zinthu zonse;

chimene mufuna kuchita wina sangaletse konse.

"Aa, inu Ambuye Yehova, munalenga dziko lakumwamba ndi dziko lapansi. Munazilenga ndi dzanja lanu lamphamvu ndipo palibe chokulakani.

Fé no impossível

Se tiverdes fé como um grão de mostarda... Os impossíveis de Deus são convites ao exercício da fé audaciosa.

Iye anayankha kuti, "Chifukwa inu muli ndi chikhulupiriro chachingʼono. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati muli ndi chikhulupiriro monga kambewu ka mpiru, mukhoza kunena ndi phiri ili kuti, Choka apa nupite apo,ndipo lidzachoka. Palibe kanthu kamene kadzakukanikani.

Yesu anati, " Ngati mungathe!Zinthu zonse ndi zotheka kwa iye amene akhulupirira."

Nʼchifukwa chake ndikukuwuzani kuti chilichonse chimene mupempha mʼpemphero, khulupirirani kuti mwalandira, ndipo chidzakhala chanu.

Yehova Wamphamvuzonse akuti, "Ngati zikuoneka kuti nʼzosatheka kwa anthu otsala pa nthawi ino, kodi zidzakhala zosathekanso kwa Ine?" akutero Yehova Wamphamvuzonse.

Yehova ndi wamkulu ndi wamphamvu kwambiri;

nzeru zake zilibe malire.

Yesu ameneyu anaperekedwa kwa inu mwa kufuna ndi kudziwiratu kwa Mulungu; ndipo inu mothandizidwa ndi anthu oyipa, munamupha Iye pomupachika pa mtanda. Koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa, kumumasula Iye ku zowawa za imfa, chifukwa kunali kosatheka kuti agwiridwe ndi imfa.

Seja o primeiro
Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-29_22-07-56-