Deus é amor
Deus é amor — esta é a declaração mais profunda da Bíblia sobre a natureza divina. Tudo que Deus faz nasce do amor. Quem permanece no amor permanece em Deus.
A natureza de Deus
Deus é amor. Quem permanece no amor, permanece em Deus e Deus nele. Ele nos amou primeiro com amor eterno.
Mulungu ndiye Chikondi
Anzanga okondedwa, tiyeni tikondane wina ndi mnzake, pakuti chikondi chimachokera kwa Mulungu. Aliyense amene ali ndi chikondi ndi mwana wa Mulungu ndipo amadziwa Mulungu. Aliyense amene alibe chikondi sadziwa Mulungu, chifukwa Mulungu ndiye chikondi.
Chikondi ndi ichi: osati kuti ife ndife amene tinamukonda Mulungu, koma kuti Iyeyo ndiye amene anatikonda ndipo anatumiza Mwana wake kuti akhale nsembe yopepesera machimo athu.
Ngati aliyense avomereza kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu, Mulungu amakhala mwa iye ndipo iyeyo amakhala mwa Mulungu. Tikudziwa ndipo timadalira chikondi chimene Mulungu ali nacho pa ife.
Mulungu ndiye chikondi. Aliyense amene amakhala moyo wachikondi, ali mwa Mulungu ndipo Mulungu amakhala mwa iye.
Ife timakonda Mulungu chifukwa ndiye anayamba kutikonda.
"Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi, kotero anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira Iye asatayike koma akhale ndi moyo wosatha.
O amor de Deus revelado
Deus prova o seu amor em que Cristo morreu por nós quando ainda éramos pecadores. Seu amor é compassivo e eterno.
Koma Mulungu anaonetsa chikondi chake kwa ife chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu anatifera.
Koma chifukwa cha chikondi chake chachikulu pa ife, Mulungu amene ndi olemera mʼchifundo, anatipanga kukhala amoyo ndi Khristu ngakhale pamene ife tinali akufa mu zolakwa zathu. Koma tinapulumutsidwa mwachisomo.
Koma Ambuye ndinu Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima,
wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi ndi wokhulupirika.
Chikondi chanu chosatha ndi chamtengowapatali!
Otchuka pamodzi ndi anthu wamba pakati pa anthu
amapeza pothawirapo mu mthunzi wa mapiko anu.
Chifukwa chikondi chanu
ndi choposa moyo, milomo yanga idzakulemekezani.
Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino.
Pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
Kodi alipo Mulungu wofanana nanu,
amene amakhululukira tchimo ndi kuyiwala zolakwa
za anthu otsala amene ndi cholowa chake?
Inu simusunga mkwiyo mpaka muyaya
koma kwanu nʼkuonetsa chikondi chosasinthika.
Malonje Otsiriza
Potsiriza abale, ndikuti tsalani bwino. Yesetsani kukhala angwiro, mvetsetsani pempho langa, khalani a mtima umodzi, khalani mwamtendere. Ndipo Mulungu wachikondi ndi mtendere adzakhala nanu.