Publicidade

Deus

Por Bíblia Online

Deus é a realidade suprema do universo — o criador, sustentador e redentor de tudo o que existe. Conhecê-lo é a essência da vida eterna e o maior privilégio da existência humana.

Quem é Deus

Não há santo como o Senhor. Tu és grande e fazes maravilhas — só tu és Deus. Sua majestade transcende toda compreensão.

"Palibe wina woyera ngati Yehova,

palibe wina koma inu nokha,

palibe thanthwe lofanana ndi Mulungu wathu.

Inu ndinu wamkulu, Yehova Wamphamvuzonse! Palibe wina wofanana nanu, ndipo palibe Mulungu wina koma Inu nokha, monga tamvera ndi makutu athu.

Pakuti nyumba iliyonse imamangidwa ndi munthu wina, koma amene anapanga zonse ndi Mulungu.

Nyimbo Yotamanda Yehova

Yehova ndinu Mulungu wanga;

ine ndidzakukwezani ndi kutamanda dzina lanu,

pakuti mwachita zodabwitsa

zimene munakonzekeratu kalekale

mokhulupirika kwambiri.

"Pakuti maganizo anga siwofanana ndi maganizo anu,

ngakhale njira zanu si njira zanga,"

akutero Yehova.

Deus é amor

Deus é amor. Quem permanece no amor permanece em Deus e Deus nele. Nós amamos porque Ele nos amou primeiro.

Tikudziwa ndipo timadalira chikondi chimene Mulungu ali nacho pa ife.

Mulungu ndiye chikondi. Aliyense amene amakhala moyo wachikondi, ali mwa Mulungu ndipo Mulungu amakhala mwa iye.

Ife timakonda Mulungu chifukwa ndiye anayamba kutikonda.

Ngati wina anena kuti, "Ine ndimakonda Mulungu," koma namadana ndi mʼbale wake ndi wabodza ameneyo. Pakuti aliyense amene sakonda mʼbale wake, amene akumuona, sangathenso kukonda Mulungu amene sanamuone.

Palibe amene anaonapo Mulungu, koma tikakondana wina ndi mnzake, ndiye kuti Mulungu amakhala mwa ife ndipo chikondi chake chafika pachimake penipeni mwa ife.

Yehova Mulungu wako ali pakati pako,

ali ndi mphamvu yopulumutsa.

Adzakondwera kwambiri mwa iwe,

adzakukhalitsa chete ndi chikondi chake,

adzayimba mokondwera chifukwa cha iwe."

Buscar a Deus

Buscareis o Senhor e o encontrareis quando o buscardes de todo o coração. Provai e vede que o Senhor é bom.

Mukanali komweko, ngati mudzamufunafuna Yehova Mulungu wanu mudzamupeza koma ngati mutamufunafuna ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.

Lawani ndipo onani kuti Yehova ndi wabwino;

wodala munthu amene amathawira kwa Iye.

Ndinati kwa Yehova, "Inu ndinu Ambuye anga;

popanda Inu, ine ndilibe chinthu chinanso chabwino."

Kodi kumwamba ndili ndi yani kupatula Inu?

Ndipo dziko lapansi lilibe chilichonse chimene ndimachilakalaka koposa Inuyo.

Ndikachita mantha

ndimadalira Inu.

Popeza Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa,

chifukwa cha dzina lanu tsogolereni ndi kundiwongolera.

Paja aliyense amene apeza ine wapeza moyo

ndipo Yehova amamukomera mtima.

Viver com Deus

Sê forte e corajoso, porque o Senhor teu Deus é contigo. Em Deus encontramos a razão de existir.

Paja ndinakulamula kuti ukhale wamphamvu ndi wolimba mtima. Choncho usamachite mantha kapena kutaya mtima popeza Ine Yehova Mulungu wako ndidzakhala nawe kulikonse kumene udzapite."

Ndikhoza kuchita zonse kudzera mwa Iye amene amandipatsa mphamvu.

Malangizo Otsiriza

Nthawi zonse muzikondwa mwa Ambuye. Ndikubwerezanso; muzikondwa!

Ulemerero wa Ziyoni

"Dzuka, wala, pakuti kuwala kwako kwafika,

ndipo ulemerero wa Yehova wakuwalira.

Pakuti Ine Yehova, ndine Mulungu wako,

amene ndikukugwira dzanja lako lamanja

ndipo ndikuti, usaope;

ndidzakuthandiza.

Dzichepetseni pamaso pa Ambuye ndipo Iye adzakukwezani.

Musanamizidwe: nʼkosatheka kupusitsa Mulungu. Munthu amakolola zimene wafesa.

"Lemekeza abambo ako ndi amayi ako kuti ukhale ndi moyo wautali mʼdziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa.

Seja o primeiro
Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-29_22-07-56-