Pular para o conteúdo
Publicidade

Dia das crianças

Por Bíblia Online

As crianças são preciosas aos olhos de Deus. Jesus as acolheu, abençoou e ensinou que delas é o Reino dos Céus — modelos de fé, pureza e humildade.

Jesus e as crianças

Deixai vir a mim as crianças. Jesus abraçou, abençoou e honrou as crianças como modelo de fé para os adultos.

Yesu anati, "Lolani ana abwere kwa Ine, ndipo musawaletse pakuti ufumu wakumwamba ndi wa iwo onga anawa."

Wamkulu mu Ufumu Wakumwamba

Pa nthawi imeneyo ophunzira anabwera kwa Yesu ndipo anamufunsa kuti, "Wamkulu woposa onse ndani mu ufumu wakumwamba?"

Iye anayitana kamwana kakangʼono ndi kukayimiritsa pakati pawo. Ndipo Iye anati, "Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati simusintha ndi kukhala ngati tiana tatingʼono, simudzalowa konse mu ufumu wakumwamba. Chifukwa chake, aliyense amene adzichepetsa yekha ngati kamwana aka, ameneyo ndiye wamkulu koposa onse mu ufumu wakumwamba.

Fanizo la Nkhosa Yotayika

"Onetsetsani kuti musanyoze mmodzi wa anawa. Pakuti ndikuwuzani kuti angelo awo kumwamba amakhala pamaso pa Atate anga akumwamba nthawi zonse."

Koma akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo ataona zodabwitsa zimene anachita, komanso ana akufuwula mʼNyumbayo kuti, "Hosana kwa Mwana wa Davide," anapsa mtima.

Anamufunsa kuti, "Kodi mukumva zimene anawa akunena?"

Yesu anayankha nati, "Inde. Kodi simunawerenge kuti,

"Kuchokera mʼkamwa mwa ana ndi makanda

mwatuluka mayamiko?"

Ndikukuwuzani choonadi, aliyense amene sadzalandira Ufumu wa Mulungu ngati kamwana sadzalowamo." Ndipo ananyamula ana mʼmanja ake, ndi kuyika manja ake pa iwo nawadalitsa.

Anatenga kamwana nakayimiritsa pakati pawo ndipo anawawuza kuti, "Aliyense wolandira mmodzi wa ana angʼono awa mʼdzina langa alandira Ine; ndipo aliyense wolandira Ine salandira Ine koma amene anandituma."

Instruir e proteger

Instrui a criança no caminho de Deus. Elas são herança do Senhor — presentes sagrados que devemos educar com amor.

Mwana muzimuphunzitsa njira yake,

ndipo akadzakalamba sadzachokamo.

Yehova adzaphunzitsa ana ako onse,

ndipo ana ako adzakhala ndi mtendere wochuluka.

Ana ndiye cholowa chochokera kwa Yehova,

ana ndi mphotho yochokera kwa Iye.

Inu ana, mverani makolo anu mu zonse pakuti izi zimakondweretsa Ambuye.

Inu abambo, musakwiyitse ana anu, kuti angataye mtima.

Ana ndi Makolo Awo

Inu ana, mverani makolo anu mwa Ambuye, pakuti zimenezi ndi zoyenera. "Lemekeza abambo ndi amayi ako." Limeneli ndi lamulo loyamba lokhala ndi lonjezo. Ngati ulemekeza abambo ako ndi amayi ako, "zinthu zidzakuyendera bwino ndipo udzasangalala ndi moyo wautali pa dziko lapansi." Abambo musakwiyitse ana anu; mʼmalo mwake, muwalere mʼchiphunzitso ndi mʼchilangizo cha Ambuye.

" Yehova akudalitse

ndi kukusunga;

Yehova awalitse nkhope yake pa iwe,

nakuchitira chisomo;

Yehova akweze nkhope yake pa iwe,

nakupatse mtendere.’ "

Seja o primeiro