Pular para o conteúdo
Publicidade

Dia dos pais

Por Bíblia Online

O Dia dos Pais celebra o amor e o sacrifício paterno. A Bíblia honra os pais como provedores, protetores e guias espirituais que moldam as próximas gerações.

O pai que educa

Instrui a criança no caminho em que deve andar. O pai justo educa com amor, firmeza e o exemplo de uma vida íntegra.

Mwana muzimuphunzitsa njira yake,

ndipo akadzakalamba sadzachokamo.

Amene sakwapula mwana wake, ndiye kuti amamuda,

koma wokonda mwana wake sazengereza kumulanga.

Munthu wolungama amakhala ndi makhalidwe abwino;

odala ndi ana ake amene amatsanzira moyo wake.

Abambo a munthu wolungama ali ndi chimwemwe chachikulu;

Wobala mwana wanzeru adzakondwera naye.

Amene amaopa Yehova ali ndi chitetezo chokwanira

ndipo iye adzakhala pothawira pa ana ake.

Honra e alegria

Honra a teu pai e tua mãe. Os filhos são herança do Senhor, e a família que serve a Deus junta é inabalável.

"Lemekeza abambo ako ndi amayi ako kuti ukhale ndi moyo wautali mʼdziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa.

Ana ndiye cholowa chochokera kwa Yehova,

ana ndi mphotho yochokera kwa Iye.

Ana a pa unyamata ali ngati mivi mʼmanja

mwa munthu wankhondo.

Wodala munthu

amene motengera mivi mwake mwadzaza.

Iwo sadzachititsidwa manyazi

pamene alimbana ndi adani awo pa zipata.

Koma ngati kutumikira Yehova kukuyipirani, sankhani lero amene mudzamutumikire, kapena milungu imene makolo anu ankayitumikira kutsidya kwa mtsinje wa Yufurate, kapena milungu ya Aamori, amene mukukhala mʼdziko lawo. Koma ine ndi banja langa, tidzatumikira Yehova."

Khalani tcheru; khazikikani mʼchikhulupiriro chanu; limbani mtima; khalani amphamvu.

Ndipo iye ananyamuka ndi kupita kwa abambo ake.

"Koma iye akanali patali, abambo ake anamuona ndipo anamvera chisoni; anathamangira mwanayo, namukumbatira ndi kupsompsona.

"Mwanayo anati, Abambo, ine ndachimwira kumwamba ndi inunso. Ine sindiyenera konse kutchedwa mwana wanu.

"Koma abambowo anati kwa antchito ake, Fulumirani! Bweretsani mkanjo wabwino kwambiri ndipo mumuveke. Muvekeni mphete ndi nsapato. Bweretsani mwana wangʼombe wonenepa ndipo iphani. Tiyeni tikhale ndi phwando ndi kukondwerera.

Seja o primeiro