Publicidade

Doença

Por Bíblia Online

A doença é realidade humana que a Bíblia confronta com compaixão e poder. Jesus curou toda enfermidade e prometeu ouvir a oração da fé pelos enfermos.

Jesus, o curador

Jesus percorreu toda a Galileia curando toda enfermidade e doença entre o povo. Pelo seu nome, curas continuam acontecendo.

Antchito ndi Ochepa

Yesu anayendayenda mʼmizinda yonse ndi mʼmidzi, kuphunzitsa mʼmasunagoge awo, nalalikira Uthenga Wabwino wa ufumu ndi kuchiritsa nthenda zawo zonse ndi zofowoka za mʼmatupi mwawo.

Chiritsani odwala, ukitsani akufa, chiritsani akhate, tulutsani ziwanda. Munalandira kwaulere, perekani kwaulere.

Chiritsani odwala, ukitsani akufa, chiritsani akhate, tulutsani ziwanda. Munalandira kwaulere, perekani kwaulere.

Itafika nthawi yamadzulo, anthu anabweretsa kwa Iye anthu ambiri ogwidwa ndi ziwanda ndipo anatulutsa ziwandazo ndi mawu okha, nachiritsa odwala onse. Uku kunali kukwaniritsa zimene ananena mneneri Yesaya kuti,

"Iye anatenga zofowoka zathu,

nanyamula nthenda zathu."

ndinali wausiwa ndipo munandiveka, ndinali wodwala ndipo munandisamalira, ndinali ku ndende ndipo inu munandiyendera.

"Ndipo olungamawo adzamuyankha kuti, Ambuye ndi liti tinakuonani muli ndi njala ndipo tinakudyetsani, kapena ludzu ndipo tinakupatsani madzi akumwa? Ndi liti tinakuonani muli mlendo ndipo tinakulandirani, kapena wa usiwa ndipo tinakuvekani? Ndi liti tinakuonani mutadwala kapena ku ndende ndipo tinakuyenderani?

"Mfumu idzayankha kuti, Zoonadi, ndikuwuzani kuti chilichonse chimene munachitira mmodzi wa abale anga onyozekawa munandichitira Ine.

Yesu atamva zimenezi, anawawuza kuti, "Anthu amene ali bwino safuna singʼanga koma odwala. Ine sindinabwere kudzayitana olungama, koma ochimwa."

Chiritsani odwala amene ali kumeneko ndipo muwawuze kuti, Ufumu wa Mulungu wayandikira.

Yesu Atuma Ophunzira ake Khumi ndi Awiri

Yesu atawayitana khumi ndi awiriwo pamodzi, Iye anawapatsa mphamvu ndi ulamuliro wotulutsa ziwanda zonse ndi kuchiritsa matenda. Ndipo Iye anawatumiza kukalalikira za ufumu wa Mulungu ndi kukachiritsa odwala.

Promessas de cura

Eu sou o Senhor que te sara. As Escrituras prometem cura para o corpo e para a alma aos que confiam em Deus.

Yehova anati, "Ngati inu mudzamvetsa bwino mawu anga, kuchita zolungama, kumvera malamulo anga ndi kusamalitsa zimene ndikukuwuzani ndiye kuti Ine sindidzayika pa inu matenda amene ndinayika pa anthu a ku Igupto popeza ndine Yehova amene ndimakuchiritsani."

Muzipembedza Yehova Mulungu wanu ndipo adzakudalitsani ndi chakudya ndi madzi ndiponso ndidzachotsa nthenda pakati panu.

Muzipembedza Yehova Mulungu wanu ndipo adzakudalitsani ndi chakudya ndi madzi ndiponso ndidzachotsa nthenda pakati panu.

Inu Yehova, chiritseni, ndipo ndidzachira;

pulumutseni ndipo ndidzapulumuka,

chifukwa ndinu amene ndimakutamandani.

Amene amakhululuka machimo ako onse

ndi kuchiritsa nthenda zako zonse,

Akutsogolera anthu osweka mtima

ndi kumanga mabala awo.

Yehova amatsekula maso anthu osaona,

Yehova amadzutsa onse amene awerama pansi,

Yehova amakonda anthu olungama.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

Wodala ndi munthu amene amaganizira anthu osauka;

Yehova amamuwombola pa nthawi yamsautso.

Yehova adzamuteteza ndi kusunga moyo wake;

Yehova adzamudalitsa iye mʼdziko

ndipo sadzamupereka ku zofuna za adani ake.

Yehova adzamuthandiza pamene akudwala

ndipo adzamuchiritsa pa bedi lake la matenda.

Wokondedwa, ndimakupempherera kuti zako zonse zikuyendere bwino, ndikuti ukhale bwino mʼthupi mwako, monga momwe ulili moyo wako wauzimu.

Oração pelos doentes

A oração da fé salvará o enfermo. Confessai as ofensas uns aos outros e orai uns pelos outros para serdes curados.

Kodi alipo wina mwa inu akudwala? Ayitane akulu ampingo kuti adzamupempherere ndi kumudzoza mafuta mʼdzina la Ambuye. Ndipo pemphero lachikhulupiriro lidzachiritsa munthu wodwalayo ndipo Ambuye adzamuutsa. Ngati wachimwa adzakhululukidwa.

Kodi alipo wina mwa inu akudwala? Ayitane akulu ampingo kuti adzamupempherere ndi kumudzoza mafuta mʼdzina la Ambuye. Ndipo pemphero lachikhulupiriro lidzachiritsa munthu wodwalayo ndipo Ambuye adzamuutsa. Ngati wachimwa adzakhululukidwa.

Choncho, ululiranani machimo anu ndi kupemphererana wina ndi mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama ndi lamphamvu ndipo limagwira ntchito.

kapena chifukwa cha mavumbulutso aakulu kuposa awa. Choncho, kuti ndisadzitukumule, ndinayikidwa minga mʼthupi langa, wamthenga wa Satana, kuti adzindizunza. Katatu konse ndinapempha Ambuye kuti andichotsere. Koma anandiwuza kuti, "Chisomo changa ndi chokukwanira, pakuti mphamvu zanga zimaoneka kwathunthu mwa munthu wofowoka." Choncho ndidzadzitamandira mokondwera chifukwa cha zofowoka zanga, kuti mʼkutero mphamvu ya Khristu ikhale pa ine. Tsono, chifukwa cha Khristu, ndimakondwera pamene ndili wofowoka, pamene akundinyoza, pamene ndikumva zowawa, ndi pamene akundizunza ndi kundisautsa. Pakuti pamene ndili wofowoka ndiye kuti ndili wamphamvu.

Esperança na aflição

Ele tomou sobre si as nossas enfermidades. Mesmo na doença, o coração alegre serve de bom remédio e Deus dá esperança.

Ndithudi, iye anamva zowawa mʼmalo mwa ife;

ndipo anasautsidwa mʼmalo mwathu.

Koma ife tinkaganiza kuti ndi Mulungu amene akumulanga,

kumukantha ndi kumusautsa.

Ndithudi, iye anamva zowawa mʼmalo mwa ife;

ndipo anasautsidwa mʼmalo mwathu.

Koma ife tinkaganiza kuti ndi Mulungu amene akumulanga,

kumukantha ndi kumusautsa.

Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu,

munthu amene moyo wake unali wamasautso, wozolowera zowawa,

ndipo anali ngati munthu amene anzake amaphimba nkhope zawo akamuona.

Iye ananyozedwa, ndipo ife sitinamuyese kanthu.

Mtima wosangalala uli ngati mankhwala abwino,

koma mtima wokhumudwa umafowoketsa mafupa.

Mtima wa munthu utha kupirira pa matenda,

koma munthu akataya mtima ndani angathe kumulimbitsanso.

Chinthu chochiyembekezera chikalephereka chimalefula mtima,

koma chinthu chochilakalaka chikachitikadi chimakhala ngati mtengo wamoyo.

Pamene ndinali chete,

mafupa anga anakalamba

chifukwa cha kubuwula kwanga tsiku lonse.

Monga inu mukudziwa ndinkakulalikirani Uthenga Wabwino ndili wofowoka. Ngakhale kuti matendawo anali ngati mayesero kwa inu, simunandinyoze kapena kunyansidwa nane. Komatu inu munandilandira ngati kuti ndinali mngelo wa Mulungu, ngati kuti ndinali Khristu Yesu mwini.

Uleke kumangomwa madzi okha, koma uzimwako vinyo pangʼono chifukwa cha vuto lako la mʼmimba ndi kudwala kwako kwa pafupipafupi.

Mulungu adzapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo. Sikudzakhalanso imfa kapena kukhuza maliro kapena kulira kapena ululu popeza zakale zapita.’ "

Seja o primeiro
Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-29_22-07-56-