Ensinar
Ensinar é mandamento e dom. A Bíblia exorta pais, líderes e mestres a transmitir a verdade divina com fidelidade, paciência e sabedoria para as próximas gerações.
Ensinar a Palavra
Toda Escritura é útil para ensinar. Quem ouve as palavras de Jesus e as pratica é como o homem sábio que construiu sobre a rocha.
Malemba onse anawalembetsa ndi Mulungu, ndipo othandiza pophunzitsa, podzudzula, pokonza cholakwika ndi polangiza za chilungamo kuti munthu wa Mulungu akonzekere bwino lomwe kugwira ntchito iliyonse yabwino.
"Nʼchifukwa chake aliyense amene amva mawu anga ndi kuwachita akufanana ndi munthu wanzeru amene anamanga nyumba yake pa thanthwe.
Mawu a Khristu akhazikike kwathunthu mʼmitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana wina ndi mnzake ndi nzeru zonse pamene mukuyimba Masalimo, nyimbo zotamanda ndi nyimbo zauzimu, kuyimbira Mulungu ndi mitima yoyamika.
Pakuti zilizonse zimene zinalembedwa kale zinalembedwa kuti zitiphunzitse ife. Malembawo amatilimbikitsa kupirira kuti tikhale ndi chiyembekezo.
Iyi ndi miyambi ya Solomoni mwana wa Davide, mfumu ya Israeli:
Ndi yothandiza kuti munthu adziwe nzeru ndi malangizo;
kuti amvetse mawu a matanthauzo ozama;
kuti alandire malangizo othandiza kuti achite zinthu mwanzeru,
akhale wangwiro, wachilungamo ndiponso wosakondera.
Ndi yothandiza munthu wamba kuti aphunzire nzeru za kuchenjera,
achinyamata kudziwa zinthu bwino ndi kulingalira.
Munthu wanzeru amvetse bwino miyamboyi kuti awonjezere kuphunzira kwake,
ndi munthu womvetsa zinthu bwino apatepo luso,
kuti azimvetsa miyambi ndi mafanizo,
mawu a anthu anzeru ndi mikuluwiko.
Kuopa Yehova ndiye chiyambi cha nzeru.
Zitsiru zimanyoza nzeru ndi malangizo.
Instruir as gerações
Ensina a criança nos caminhos de Deus. A geração que não conhece o Senhor perde a herança espiritual da fé.
Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse. Malamulo amene ndakupatsani lero ayenera kukhala mu mtima mwanu. Muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu. Muzikamba za malamulowa pamene muli mʼnyumba zanu, pamene mukuyenda mʼnjira, pamene mukugona ndi pamene mukudzuka.
Mwana wanga, mvera malangizo a abambo ako
ndipo usakane mawu okuwongolera a amayi ako.
Ali ngati sangamutu yokongola ya maluwa pamutu pako
ndiponso ali ngati mkanda mʼkhosi mwako.
Mwana wanga, usunge malamulo a abambo ako;
ndipo usataye zimene anakuphunzitsa amayi ako.
Zimenezi uzimatirire pa mtima pako masiku onse,
uzimangirire mʼkhosi mwako.
Ukamayenda, zidzakulozera njira;
ukugona, zidzakulondera;
ukudzuka, zidzakuyankhula.
Paja malamulo awa ali ngati nyale,
malangizowa ali ngati kuwunika,
ndipo chidzudzulo cha mwambo ndiwo
moyo weniweni,
Upeze nzeru, upeze nzeru zomvetsa zinthu;
usayiwale mawu anga kapena kutayana nawo.
Usasiye nzeru ndipo idzakusunga.
Uziyikonda ndipo idzakuteteza.
Fundo yayikulu pa za nzeru ndi iyi: upeze nzeru.
Kaya pali china chilichonse chimene ungapeze, koma upeze nzeru yomvetsa bwino zinthu.
Uyilemekeze nzeruyo ndipo idzakukweza;
ikumbatire nzeruyo ndipo idzakupatsa ulemu.
Ugwiritse zimene ndikukuphunzitsazi osazitaya ayi.
Uwasamale bwino pakuti moyo wako wagona pamenepa.
Usayende mʼnjira za anthu oyipa
kapena kuyenda mʼnjira ya anthu ochimwa.
Ndipotu mtima wako uziwuyangʼanira bwino ndithu
pakuti ndiwo magwero a moyo.
Usiyiretu kuyankhula zokhotakhota;
ndipo ulekeretu kuyankhula zinthu zonyansa.
Maso ako ayangʼane patsogolo;
uziyangʼana kutsogolo molunjika.
Uzilingalira bwino kumene kupita mapazi ako
ndipo njira zako zonse zidzakhala zosakayikitsa.
Usapatukire kumanja kapena kumanzere;
usapite kumene kuli zoyipa.
Malangizo a munthu wanzeru ali ngati kasupe wamoyo;
amathandiza munthu kuti asakondwe mu msampha wa imfa.
Kuopa Yehova ndiye chiyambi cha nzeru;
kudziwa Woyerayo ndiko kukhala womvetsa bwino zinthu.
Inu anthu anga imvani chiphunzitso changa;
mvetserani mawu a pakamwa panga.
Ndidzatsekula pakamwa panga mʼmafanizo,
ndidzayankhula zinthu zobisika, zinthu zakalekale
zimene tinazimva ndi kuzidziwa,
zimene makolo athu anatiwuza.
Sitidzabisira ana awo,
tidzafotokozera mʼbado wotsatira
ntchito zotamandika za Yehova,
mphamvu zake, ndi zozizwitsa zimene Iye wachita.
Mʼbado onse utapita kukakhala ndi anthu a mtundu awo, kenaka panauka mʼbado wina umene sunadziwe Yehova ngakhale ntchito zazikulu zimene Yehova anachitira Aisraeli.
Fidelidade no ensino
Quem ensina com fidelidade merece dupla honra. Cuidado com doutrinas falsas — permaneçam na doutrina de Cristo.
Akulu ampingo amene amayangʼanira bwino zochitika za mu mpingo, ndi oyenera ulemu wowirikiza, makamaka amene ntchito yawo ndi kulalikira ndi kuphunzitsa. Pakuti Mawu a Mulungu amati, "Musamange ngʼombe pakamwa pamene ikupuntha tirigu," ndi "Wantchito ngoyenera kulandira malipiro ake."
Upewe nkhani zopanda pake, zosalemekeza Mulungu, chifukwa anthu oyankhula zotere amanka napotokerapotokera. Chiphunzitso chawo chidzafalikira ngati chilonda. Mwa anthuwa muli Humenayo ndi Fileto.
Aliyense amene sasunga chiphunzitso cha Khristu, alibe Mulungu. Koma amene amasunga chiphunzitsochi, ameneyo alinso ndi Atate ndi Mwana.
Phwando lili pakatikati, Yesu anapita ku bwalo la Nyumba ya Mulungu ndi kuyamba kuphunzitsa. Ayuda anadabwa ndipo anafunsa kuti, "Kodi munthu uyu nzeru izi anazitenga kuti popanda kuphunzira?"
Yesu anayankha kuti, "Chiphunzitso changa si cha Ine ndekha. Chimachokera kwa Iye amene anandituma. Ngati munthu asankha kuchita chifuniro cha Mulungu, adzazindikira ngati chiphunzitso changa nʼchochokera kwa Mulungu kapena ngati ndi mwa Ine ndekha. Iye amene amayankhula za Iye mwini amatero kuti adzipezere ulemu, koma amene amagwira ntchito kuti amene anamutuma alandire ulemu, ameneyo ndiye munthu woona; mu mtima mwake mulibe chinyengo chilichonse.