Publicidade

Esperar no Senhor

Por Bíblia Online

Esperar no Senhor é ato de fé e confiança. A Bíblia promete que os que esperam em Deus renovam as forças, recebem direção e experimentam a fidelidade divina no tempo certo.

Renovar as forças

Os que esperam no Senhor renovam as forças. Sobem como águias, correm e não se cansam, caminham e não se fatigam.

koma iwo amene amakhulupirira Yehova

adzalandira mphamvu zatsopano.

Adzawuluka ngati chiwombankhanga;

adzathamanga koma sadzalefuka,

adzayenda koma sadzatopa konse.

Komatu Yehova akufunitsitsa kuti akukomereni mtima,

iye ali wokonzeka kuti akuchitireni chifundo.

Pakuti Yehova ndi Mulungu wachilungamo.

Ndi odala onse amene amakhulupirira Iye!

Dikirani pa Yehova;

khalani anyonga ndipo limbani mtima

nimudikire Yehova.

Ine ndikutsimikiza mtima za zimenezi;

ndidzaona ubwino wa Yehova

mʼdziko la anthu amoyo.

Dikirani pa Yehova;

khalani anyonga ndipo limbani mtima

nimudikire Yehova.

Yehova ndiye kuwunika kwanga ndi chipulumutso changa;

ndidzaopa yani?

Yehova ndi linga la moyo wanga;

ndidzachita mantha ndi yani?

Pamene anthu oyipa abwera kudzalimbana nane

kudzadya mnofu wanga,

pamene adani anga ndi achiwembu andithira nkhondo,

iwo adzapunthwa ndi kugwa.

Ngakhale gulu lankhondo lindizinge,

mtima wanga sudzaopa.

Ngakhale nkhondo itayambika kulimbana nane,

ngakhale nthawi imeneyo, ine ndidzalimbika mtima.

Chinthu chimodzi chokha chimene ndipempha kwa Yehova,

ichi ndi chimene ndidzachifunafuna:

kuti ndikhale mʼNyumba ya Yehova

masiku onse a moyo wanga,

ndi kuyangʼana kukongola kwa Yehova,

ndi kumufunafuna Iye mʼNyumba yake.

Pakuti pa tsiku la msautso

Iye adzanditeteza mʼmalo ake okhalamo;

adzandibisa mʼkati mwa Nyumba yake

ndi kukhazika ine pamwamba pa thanthwe.

Kotero mutu wanga udzakwezedwa

kuposa adani anga amene andizungulira;

pa Nyumba yake ndidzapereka nsembe ndi mfuwu wachimwemwe;

ndidzayimba nyimbo kwa Yehova.

Imvani mawu anga pamene ndiyitana Inu Yehova

mundichitire chifundo ndipo mundiyankhe.

Mtima wanga ukuti kwa Inu, "Funafuna nkhope yake!"

Nkhope yanu Yehova ndidzayifunafuna.

Musandibisire nkhope yanu,

musamubweze mtumiki wanu mwamkwiyo;

mwakhala muli thandizo langa.

Musandikane kapena kunditaya,

Inu Mulungu Mpulumutsi wanga.

Ngakhale abambo ndi amayi anga anditaya

Yehova adzandisamala.

Phunzitseni njira yanu Inu Yehova,

munditsogolere mʼnjira yowongoka

chifukwa cha ondizunza.

Musandipereke ku zokhumba za adani anga,

pakuti mboni zambiri zauka kutsutsana nane

ndipo zikundiopseza.

Ine ndikutsimikiza mtima za zimenezi;

ndidzaona ubwino wa Yehova

mʼdziko la anthu amoyo.

Dikirani pa Yehova;

khalani anyonga ndipo limbani mtima

nimudikire Yehova.

Espera paciente

Esperei com paciência no Senhor e Ele se inclinou para mim. Confie nele e descanse — Ele agirá no tempo certo.

Mofatsa ndinadikira Yehova

Iye anatembenukira kwa ine ndipo anamva kulira kwanga.

Ananditulutsa mʼdzenje lachitayiko,

mʼthope ndi mʼchithaphwi;

Iye anakhazikitsa mapazi anga pa thanthwe

ndipo anandipatsa malo oyimapo olimba.

Iye anayika nyimbo yatsopano mʼkamwa mwanga,

nyimbo yamatamando kwa Mulungu wanga.

Ambiri adzaona,

nadzaopa ndipo adzakhulupirira Yehova.

Ndi wodala munthu

amakhulupirira Yehova;

amene sayembekezera kwa odzikuza,

kapena kwa amene amatembenukira kwa milungu yabodza.

Zambiri, Yehova Mulungu wanga,

ndi zodabwitsa zimene Inu mwachita.

Zinthu zimene munazikonzera ife

palibe amene angathe kukuwerengerani.

Nditati ndiyankhule ndi kufotokozera,

zidzakhala zambiri kuzifotokoza.

Nsembe ndi zopereka Inu simuzifuna,

koma makutu anga mwawatsekula;

zopereka zopsereza ndi zopereka chifukwa cha tchimo

Inu simunazipemphe.

Kotero ndinati, "Ndili pano, ndabwera.

Mʼbuku mwalembedwa za ine.

Ndikufuna kuchita chifuniro chanu, Inu Mulungu wanga;

lamulo lanu lili mu mtima mwanga."

Ndikulalikira uthenga wa chilungamo chanu mu msonkhano waukulu;

sinditseka milomo yanga

monga mukudziwa Inu Yehova.

Sindibisa chilungamo chanu mu mtima mwanga;

ndinayankhula za kukhulupirika kwanu ndi chipulumutso chanu.

Ine sindiphimba chikondi chanu ndi choonadi chanu

pa msonkhano waukulu.

Musandichotsere chifundo chanu Yehova;

chikondi chanu ndi choonadi chanu zinditeteze nthawi zonse.

Pakuti mavuto osawerengeka andizungulira;

machimo anga andigonjetsa, ndipo sindingathe kuona.

Alipo ambiri kuposa tsitsi la mʼmutu mwanga,

ndipo mtima wanga ukufowoka mʼkati mwanga.

Pulumutseni Yehova;

Bwerani msanga Yehova kudzandithandiza.

Onse amene akufunafuna kuchotsa moyo wanga

achititsidwe manyazi ndi kusokonezedwa;

onse amene amakhumba chiwonongeko changa

abwezedwe mwamanyazi.

Ife timadikira kwa Yehova mwachiyembekezo;

Iye ndiye thandizo lathu ndi chishango chathu.

Mwa Iye mitima yathu imakondwera,

pakuti ife timadalira dzina lake loyera.

Chikondi chanu chosatha

chikhale pa ife Inu Yehova, pamene tikuyembekeza kwa Inu.

Ndimayembekezera Yehova, moyo wanga umayembekezera,

ndipo ndimakhulupirira mawu ake.

Moyo wanga umayembekezera Ambuye,

kupambana momwe alonda amayembekezera mmawa,

inde, kupambana momwe alonda amayembekezera mmawa,

Peza mpumulo mwa Mulungu yekhayo iwe moyo wanga;

chiyembekezo changa chichokera mwa Iye.

Khulupirira Yehova,

ndipo sunga njira yake;

Iye adzakukweza ndipo udzalandira dziko kuti likhale lako;

udzaona anthu oyipa akuwonongeka.

Confiança e perseverança

Confie no Senhor de todo o coração. Sede pacientes na tribulação — o Senhor é fiel e cumprirá todas as suas promessas.

Uzikhulupirira Yehova ndi mtima wako wonse

ndipo usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu.

Pa zochita zako zonse uvomereze kuti Mulungu alipo,

ndipo Iye adzawongola njira zako.

Koma si pokhapo ayi, koma ife tikukondweranso mʼmasautso athu chifukwa tikudziwa kuti masautso amatiphunzitsa kupirira. Ndipo kupirira kumabweretsa makhalidwe, makhalidwe amabweretsa chiyembekezo.

Timapempheranso kuti Mulungu akulimbikitseni ndi mphamvu yake yonse ya ulemerero wake, kuti muzipirira zonse ndi mitima yofatsa ndi ya chimwemwe

Kupirira Mʼmasautso

Tsono abale, pirirani mpaka kubwera kwa Ambuye. Onani mmene amachitira mlimi. Amadikirira kuti zipatso zabwino zioneke mʼmunda mwake. Amayembekezera mokhazikika mtima kuyambira nthawi ya mvula yoyamba mpaka yotsiriza. Inunso mukhale owugwira mtima ndi osasinthika chifukwa Ambuye ali pafupi kubwera.

Monga mukudziwa, tinawatenga ngati odalitsika anthu amene anapirira. Munamva za kupirira kwa Yobu ndipo mwaona zimene Ambuye anamuchitira potsiriza pake. Ambuye ndi wodzaza ndi chisoni ndi chifundo.

Tsopano mwayeretsa mitima yanu pomvera choonadi, kuti muzikondana ndi abale anu, kukondana kwenikweni kochokera pansi pa mtima. Popeza mwabadwanso, osati ndi mbewu imene imawonongeka, koma imene siwonongeka, ndiye kuti ndi Mawu a Mulungu amoyo ndi okhalitsa. Pakuti,

"Anthu onse ali ngati udzu,

ndipo ulemerero wawo uli ngati duwa la kuthengo.

Udzu umafota ndipo duwa limathothoka,

koma mawu a Ambuye adzakhala mpaka muyaya."

Ndipo awa ndi mawu amene tinalalikira kwa inu.

Ambuye sazengereza kuchita zimene analonjeza, monga ena amaganizira. Iwo akukulezerani mtima, sakufuna kuti aliyense awonongeke, koma akufuna kuti aliyense alape.

Fanizo la Anamwali Khumi

"Nthawi imeneyo ufumu wakumwamba udzafanizidwa ndi anamwali khumi amene anatenga nyale zawo napita kukakumana ndi mkwati. Asanu anali opusa ndipo asanu ena anali ochenjera. Opusawo anatenga nyale zawo koma sanatenge mafuta; koma ochenjerawo anatenga mafuta awo mʼmabotolo pamodzi ndi nyale zawo. Mkwati anachedwa ndipo onse anayamba kusinza nagona.

"Pakati pa usiku kunamveka kufuwula kuti, Onani Mkwati! Tulukani kuti mukakumane naye!

"Pamenepo anamwali onse anadzuka nayatsa nyale zawo. Opusawo anati kwa ochenjerawo, Tipatseniko mafuta anu; nyale zathu zikuzima.

"Ochenjerawo anayankha, nati, Ayi sangakwanire inu ndi ife. Pitani kwa ogulitsa mafuta ndi kukadzigulira nokha.

"Koma pamene ankapita kukagula mafutawo, mkwati anafika. Anamwali amene anali okonzeka aja analowa naye pamodzi mʼnyumba ya phwando la ukwati. Ndipo khomo linatsekedwa.

"Pambuyo pake enawo anabwera nati, Ambuye! Ambuye! Titsekulireni!

"Koma iye anayankha kuti, Zoonadi, ine ndikuwuzani kuti sindikukudziwani.

"Choncho khalani odikira, popeza simudziwa tsiku kapena nthawi."

Seja o primeiro
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-07-05_19-25-13-