Pular para o conteúdo
Publicidade

Estudar a Bíblia

Por Bíblia Online

Estudar a Bíblia é mergulhar na mente de Deus. A Palavra é lâmpada para os pés, espada do Espírito e alimento para a alma. O cristão que estuda cresce em sabedoria e maturidade.

A importância do estudo

Os bereanos eram mais nobres porque examinavam as Escrituras diariamente. Estudar a Bíblia é mandamento e privilégio.

Tsopano anthu a ku Bereya anali akhalidwe labwino kusiyana ndi Atesalonika, pakuti iwo analandira mawu ndi chidwi chachikulu ndipo ankasanthula Malemba tsiku ndi tsiku kuti aone ngati zimene ankanena Paulozo zinali zoona.

Uyesetse kukhala wovomerezeka pamaso pa Mulungu monga wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi amene amalalikira mawu achoonadi molondola.

Kuyambira uli wamngʼono wakhala ukudziwa Malemba Oyera, amene akhoza kukupatsa nzeru zokupulumutsa kudzera mʼchikhulupiriro cha mwa Yesu Khristu. Malemba onse anawalembetsa ndi Mulungu, ndipo othandiza pophunzitsa, podzudzula, pokonza cholakwika ndi polangiza za chilungamo kuti munthu wa Mulungu akonzekere bwino lomwe kugwira ntchito iliyonse yabwino.

Mpaka nditabwera, udzipereke powerenga mawu a Mulungu kwa anthu, kulalikira ndi kuphunzitsa.

Inu mumasanthula malemba chifukwa mumaganiza kuti mʼmalembamo muli moyo wosatha. Awa ndi malemba amene akundichitira umboni.

Meditar e guardar

Não se aparte a lei do Senhor da tua boca. Medita nela de dia e de noite para que cumpras tudo o que nela está escrito.

Uziwerenga Buku la Malamuloli, uzilingalira zolembedwa mʼmenemo usana ndi usiku, kuti uchite zonse zimene zinalembedwamo. Ukamatero udzapeza bwino ndi kupambana.

Mawu anu ndi nyale ya kumapazi kwanga

ndi kuwunika kwa pa njira yanga.

Ndithu, ine ndimakonda malamulo anu!

Ndimalingaliramo tsiku lonse.

Malamulo anu amachititsa kuti ndikhale wanzeru kuposa adani anga,

popeza malamulowo ali ndi ine nthawi zonse.

Ndimamvetsa zinthu kwambiri kuposa aphunzitsi anga onse

popeza ndimalingalira umboni wanu.

Kodi mnyamata angathe bwanji kuyeretsa mayendedwe ake?

Akawasamala potsata mawu anu.

Ndimakufunafunani ndi mtima wanga wonse;

musalole kuti ndisochere kuchoka pa malamulo anu.

Ndasunga mawu anu mu mtima mwanga

kuti ndisakuchimwireni.

Mutamandike Inu Yehova;

phunzitseni malamulo anu.

Ndi milomo yanga ndimafotokoza malamulo anu onse

amene amachokera pakamwa panu.

Ndimakondwera potsatira malamulo anu

monga momwe munthu amakondwera akakhala ndi chuma chambiri.

Ndimalingalira malangizo anu

ndipo ndimaganizira njira zanu.

Ndimakondwera ndi malamulo anu;

sindidzayiwala konse mawu anu.

Gimeli

Ndidzakutamandani ndi mtima wolungama,

pamene ndikuphunzira malamulo anu olungama.

Estudo diligente

Esdras preparou o coração para buscar e ensinar a lei. O estudo exige disciplina, constância e coração aberto.

Iye anayamba ulendo wochoka ku Babuloni pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, ndipo anafika ku Yerusalemu pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu chifukwa dzanja labwino la Mulungu wake linali pa iye. Popeza Ezara anadzipereka kuwerenga ndi kusunga malamulo a Yehova, iye anafunitsitsa kuphunzitsa Aisraeli malamulo ndi malangizo a Mulungu.

Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse. Malamulo amene ndakupatsani lero ayenera kukhala mu mtima mwanu. Muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu. Muzikamba za malamulowa pamene muli mʼnyumba zanu, pamene mukuyenda mʼnjira, pamene mukugona ndi pamene mukudzuka. Muwamange ngati zizindikiro pa manja anu ndi kuwamangirira pa zipumi zanu. Muwalembe pa mphuthu za nyumba zanu ndi pa zipata zanu.

Akakhala pa mpando waufumuwo, ayenera kulemba za iye mwini mʼbuku la malamuloli, kuchokera kwa ansembe Alevi. Asunge zimene walembazo ndipo ayenera kumaziwerenga masiku onse a moyo wake, kuti aphunzire kuopa Yehova Mulungu wake posunga mosamalitsa malamulo ndi malangizowa. Asadzione kuti iyeyo ndi wopambana kuposa abale ake, nalekeratu kutsatira malamulo. Akasamala zimenezi iye ndi ana ake adzalamulira ufumu wa Israeli kwa nthawi yayitali.

Mawu Oyamba: Cholinga ndi Mutu

Iyi ndi miyambi ya Solomoni mwana wa Davide, mfumu ya Israeli:

Ndi yothandiza kuti munthu adziwe nzeru ndi malangizo;

kuti amvetse mawu a matanthauzo ozama;

kuti alandire malangizo othandiza kuti achite zinthu mwanzeru,

akhale wangwiro, wachilungamo ndiponso wosakondera.

Ndi yothandiza munthu wamba kuti aphunzire nzeru za kuchenjera,

achinyamata kudziwa zinthu bwino ndi kulingalira.

Munthu wanzeru amvetse bwino miyamboyi kuti awonjezere kuphunzira kwake,

ndi munthu womvetsa zinthu bwino apatepo luso,

kuti azimvetsa miyambi ndi mafanizo,

mawu a anthu anzeru ndi mikuluwiko.

Phindu Lina la Nzeru

Mwana wanga, usayiwale malangizo anga,

mtima wako usunge malamulo anga.

Ukatero zaka za moyo wako zidzachuluka

ndipo udzakhala pa mtendere.

Ugwiritse zimene ndikukuphunzitsazi osazitaya ayi.

Uwasamale bwino pakuti moyo wako wagona pamenepa.

Paja malamulo awa ali ngati nyale,

malangizowa ali ngati kuwunika,

ndipo chidzudzulo cha mwambo ndiwo

moyo weniweni,

Proteção e crescimento

Quem ignora a Palavra perece. Toda Escritura é útil — crescei na graça e no conhecimento do nosso Senhor.

Anthu anga akuwonongeka chifukwa chosadziwa.

"Pakuti mwakana kudziwa,

Inenso ndidzakukanani monga ansembe anga;

chifukwa mwayiwala lamulo la Mulungu wanu,

Inenso ndidzayiwala ana anu.

kuti akalandireko mawu enieni ndi malangizo? Ngati anthuwo sayankhula monga mwa mawu awa, mwa iwo mulibe kuwala.

Yesu anawafunsa kuti, "Kodi si pamenepa nanga pomwe mumalakwira chifukwa simukudziwa malemba kapena mphamvu za Mulungu?

Pakuti zilizonse zimene zinalembedwa kale zinalembedwa kuti zitiphunzitse ife. Malembawo amatilimbikitsa kupirira kuti tikhale ndi chiyembekezo.

Nʼchifukwa chake, abale okondedwa, popeza mukuzidziwa kale zimenezi, chenjerani kuti musatengeke ndi zolakwa za anthu osaweruzika, mungagwe ndi kuchoka pamalo otetezedwa. Koma kulani mu chisomo ndi mʼchidziwitso cha Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu. Kwa Iye kukhale ulemerero tsopano mpaka muyaya. Ameni.

Kunena za chipulumutso chimenechi, aneneri amene ananeneratu za chisomo chimene chimabwera kwa inu, anafunafuna mofufuzafufuza za chipulumutsochi, kufuna kudziwa nthawi ndi momwe zidzachitikire zinthu zimene Mzimu wa Khristu amene ali mwa iwo ankanenera za kuvutika kwa Khristu, ndi ulemerero umene adzakhale nawo pambuyo pake.

Seja o primeiro