Filhos
Os filhos são herança do Senhor — bênção e responsabilidade sagrada. A Bíblia orienta sobre a criação dos filhos com amor, disciplina e instrução nos caminhos de Deus.
Herança do Senhor
Os filhos são herança do Senhor e o fruto do ventre é seu galardão. Bem-aventurado o homem que enche deles a sua aljava.
Ana ndiye cholowa chochokera kwa Yehova,
ana ndi mphotho yochokera kwa Iye.
Ana a pa unyamata ali ngati mivi mʼmanja
mwa munthu wankhondo.
Wodala munthu
amene motengera mivi mwake mwadzaza.
Iwo sadzachititsidwa manyazi
pamene alimbana ndi adani awo pa zipata.
Odala ndi onse amene amaopa Yehova,
amene amayenda mʼnjira zake.
Udzadya chipatso cha ntchito yako;
madalitso ndi chuma zidzakhala zako.
Mkazi wako adzakhala ngati mpesa wobereka
mʼkati mwa nyumba yako;
ana ako adzakhala ngati mphukira za mitengo ya olivi
kuzungulira tebulo lako.
Ameneyu ndiye munthu wodalitsidwa
amene amaopa Yehova.
Odala ndi onse amene amaopa Yehova,
amene amayenda mʼnjira zake.
Udzadya chipatso cha ntchito yako;
madalitso ndi chuma zidzakhala zako.
Mkazi wako adzakhala ngati mpesa wobereka
mʼkati mwa nyumba yako;
ana ako adzakhala ngati mphukira za mitengo ya olivi
kuzungulira tebulo lako.
Ndipo ana aamuna pa chinyamata chawo
adzakhala ngati mbewu yosamalidwa bwino,
ana athu aakazi adzakhala ngati zipilala
zosemedwa bwino, zokongoletsera nyumba yaufumu.
Ana ake adzakhala amphamvu mʼdziko;
mʼbado wa olungama mtima udzadalitsidwa.
Mulungu anawadalitsa nati kwa iwo, "Muberekane, muchulukane, mudzaze dziko lapansi ndipo muligonjetse. Mulamulire nsomba zamʼnyanja, mbalame zamlengalenga ndi cholengedwa chamoyo chilichonse chimene chimayenda mokwawa pa dziko lapansi."
Yehova adzadalitsa ana anu, zokolola za mʼdziko lanu, ngʼombe zanu pamodzi ndi ziweto zanu zonse.
Inu mudzadalitsika kuposa mtundu wina uliwonse wa anthu ndipo palibe mwamuna kapena mkazi aliyense pakati panu amene adzakhale wosabereka. Ziweto zanu nazonso, sipadzapezeka zosabereka.
Instruir e disciplinar
Instrui a criança no caminho em que deve andar, e quando envelhecer não se desviará dele. Disciplina é amor em ação.
Mwana muzimuphunzitsa njira yake,
ndipo akadzakalamba sadzachokamo.
Uchitsiru umakhala mu mtima mwa mwana,
koma ndodo yomulangira mwanayo idzachotsa uchitsiruwo.
Amene sakwapula mwana wake, ndiye kuti amamuda,
koma wokonda mwana wake sazengereza kumulanga.
Ndodo ndi chidzudzulo zimapatsa nzeru
koma mwana womulekerera amachititsa amayi ake manyazi.
Usaleke kumulangiza mwana;
ngati umulanga ndi chikwapu sadzafa.
Ananu, mverani malangizo a abambo anu;
tcherani khutu kuti mupeze nzeru zodziwira zinthu.
Miyambo ya Solomoni:
Mwana wanzeru amakondweretsa abambo ake,
koma mwana wopusa amamvetsa amayi ake chisoni.
Malamulo amene ndakupatsani lero ayenera kukhala mu mtima mwanu. Muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu. Muzikamba za malamulowa pamene muli mʼnyumba zanu, pamene mukuyenda mʼnjira, pamene mukugona ndi pamene mukudzuka.
O amor de Deus por crianças
Deixai vir a mim as crianças. Jesus acolheu, abençoou e honrou as crianças como modelo de fé e humildade.
Pamene Yesu anaona zimenezi anayipidwa. Anati kwa iwo, "Lolani ana abwere kwa Ine, ndipo musawaletse, pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa onga awa.
Tsono ngati inu woyipitsitsa mumadziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanga Atate anu akumwamba sadzapereka mphatso zabwino kwa iwo amene amupempha?
Ndipo Yesu anakula mu nzeru, msinkhu ndi chisomo cha Mulungu ndi anthu.
Monga bambo amachitira chifundo ana ake,
choncho Yehova ali ndi chifundo ndi iwo amene amamuopa;
Taonani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate anatikonda nacho, kuti titchedwe ana a Mulungu! Ndipo nʼchimene ife tili! Nʼchifukwa chake dziko lapansi silitidziwa chifukwa silinamudziwe Iye.
Bênção e promessa
O Senhor te abençoe e te guarde. Os filhos dos justos serão abençoados e suas gerações caminharão na retidão.
" ‘Yehova akudalitse
ndi kukusunga;
Yehova awalitse nkhope yake pa iwe,
nakuchitira chisomo;
Yehova akweze nkhope yake pa iwe,
nakupatse mtendere.’ "
Mulungu akugwetsere mame akumwamba
ndipo minda yako ibale tirigu wambiri
ndi vinyo watsopano.
Mitundu ya anthu ikutumikire iwe
ndipo anthu akugwadire iwe.
Ukhale wolamula abale ako,
ndipo ana aamuna a amayi ako akugwadire.
Amene akutemberera iwe atembereredwe
ndipo amene adalitsa iwe adalitsike."
Pakuti ndidzathira madzi pa nthaka yowuma,
ndi kuyendetsa mitsinje mʼdziko lowuma;
ndidzatumiza Mzimu wanga pa ana anu,
ndi kutsitsa madalitso anga pa zidzukulu zanu.
Iwo adzakula ngati udzu wothirira bwino
ndi ngati bango lomera mʼmbali mwa mitsinje ya madzi oyenda.
Yehova adzaphunzitsa ana ako onse,
ndipo ana ako adzakhala ndi mtendere wochuluka.
"Ndisanakuwumbe mʼmimba mwa amayi ako ndinali nditakudziwa kale,
iwe usanabadwe ndinali nditakupatula kale;
ndinakuyika kuti ukhale mneneri kwa anthu a mitundu yonse."
Iwo adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wawo. Ndidzawapatsa mtima umodzi ndi khalidwe limodzi kotero kuti azidzandiopa nthawi zonse ndipo iwo pamodzi ndi zidzukulu zawo zinthu zidzawayendera bwino.
Pakuti Inu munalenga za mʼkati mwanga;
munandiwumba pamodzi mʼmimba mwa amayi anga.
Ndimakuyamikani chifukwa ndinapangidwa mochititsa mantha ndi modabwitsa;
ntchito zanu ndi zodabwitsa,
zimenezi ndimazidziwa bwino lomwe.
Mapangidwe anga sanabisike pamaso panu
pamene ndimapangidwa mʼmalo achinsinsi,
pamene ndinkawumbidwa mwaluso mʼmimba ya amayi anga.
Maso anu anaona thupi langa lisanawumbidwe.
Masiku onse amene anapatsidwa kwa ine, analembedwa mʼbuku lanu
asanayambe nʼkuwerengedwa komwe.
Chibadwire ine ndinaperekedwa kwa Inu;
kuchokera mʼmimba mwa amayi anga Inu mwakhala muli Mulungu wanga.
Ine ndinali wamngʼono ndipo tsopano ndakalamba
koma sindinaonepo olungama akusiyidwa
kapena ana awo akupempha chakudya.
Iwo ndi owolowamanja nthawi zonse ndipo amabwereketsa mwaufulu;
ana awo adzadalitsika.
Sitidzabisira ana awo,
tidzafotokozera mʼbado wotsatira
ntchito zotamandika za Yehova,
mphamvu zake, ndi zozizwitsa zimene Iye wachita.
Zidzukulu ndiye ulemu wa anthu okalamba,
ndipo makolo ndiye ulemerero wa ana.
Munthu wolungama amakhala ndi makhalidwe abwino;
odala ndi ana ake amene amatsanzira moyo wake.
Criação e obediência
Pais, criai vossos filhos na disciplina e instrução do Senhor. Filhos, obedecei a vossos pais — isto é justo e agradável a Deus.
Inu ana, mverani makolo anu mwa Ambuye, pakuti zimenezi ndi zoyenera. "Lemekeza abambo ndi amayi ako." Limeneli ndi lamulo loyamba lokhala ndi lonjezo. Ngati ulemekeza abambo ako ndi amayi ako, "zinthu zidzakuyendera bwino ndipo udzasangalala ndi moyo wautali pa dziko lapansi."
Abambo musakwiyitse ana anu; mʼmalo mwake, muwalere mʼchiphunzitso ndi mʼchilangizo cha Ambuye.
Inu ana, mverani makolo anu mu zonse pakuti izi zimakondweretsa Ambuye.
Inu abambo, musakwiyitse ana anu, kuti angataye mtima.
"Lemekeza abambo ako ndi amayi ako kuti ukhale ndi moyo wautali mʼdziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa.
Pamene mukupirira masautso monga chilango, Mulungu achitira inu monga ana ake. Kodi ndi mwana wotani amene abambo ake samulanga? Ngati inu simulangidwa, komatu aliyense amalangidwa, ndiye kuti sindinu ana enieni koma amʼchigololo.
Koma ngati mkazi wamasiye ali ndi ana ndi zidzukulu, anawo ayambe aphunzira kukwaniritsa udindo wawo pa banja lawo moopa Mulungu, potero akubweza zabwino kwa makolo awo ndi agogo awo. Pakuti zimenezi ndiye zimakondweretsa Mulungu.
Mayi akamabereka mwana amamva ululu chifukwa nthawi yake yafika; koma mwana wake akabadwa amayiwala ululu wake chifukwa cha chimwemwe chake chakuti mwana wabadwa mʼdziko lapansi.
Ndipo angʼonoangʼono amene munati adzagwidwa ukapolo, ana anu amene sanadziwe kusiyanitsa chabwino ndi choyipa, amenewo adzalowa mʼdzikolo. Ndidzalipereka kwa iwo ndipo lidzakhala lawo.