Publicidade

Fim do mundo

Por Bíblia Online

A Bíblia fala sobre o fim do mundo como evento certo e definitivo. Céus e terra passarão, mas as palavras de Jesus jamais passarão. A questão não é se, mas quando.

Os céus passarão

Os céus e a terra passarão, mas as palavras de Jesus permanecerão para sempre. O mundo presente é temporário.

Kumwamba ndi dziko lapansi zidzatha, koma mawu anga sadzatha."

"Akadzangotha mavuto a masiku amenewo,

" dzuwa lidzadetsedwa,

ndipo mwezi sudzawala;

nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba,

ndipo mphamvu za mmwamba zidzagwedezeka.

Tsiku ndi Nthawi Sizidziwika

"Palibe amene adziwa za tsikulo kapena nthawi, angakhale angelo akumwamba, angakhale Mwana, koma Atate okha.

Tsiku ndi Ora Sizikudziwika

"Palibe amene akudziwa za tsikulo kapena nthawi, ngakhale angelo akumwamba, kapena Mwana, koma Atate wokha.

O dia do Senhor

O dia do Senhor virá como ladrão. Os céus passarão com grande estrondo, e os elementos se dissolverão no fogo.

Koma tsiku la Ambuye lidzafika ngati mbala. Pa tsikuli zinthu zakumwamba zidzachoka ndi phokoso lalikulu. Zinthu zonse zidzawonongedwa ndi moto, ndipo dziko lapansi ndi zonse zili mʼmenemo zidzapsa.

Dziko la kumwamba ndi lapansi la masiku ano akulisunga ndi mawu omwewo kuti adzalitentha ndi moto. Akuzisunga mpaka tsiku limene adzaweruza ndi kuwononga anthu onse osapembedza Mulungu.

Popeza kuti zinthu zonse zidzawonongedwa motere, kodi inu muyenera kukhala anthu otani? Muyenera kukhala moyo wachiyero ndi opembedza Mulungu pamene mukuyembekezera tsiku la Mulungu ndi kufulumiza kufika kwake. Pa tsiku limeneli zinthu zakumwamba zidzawonongedwa ndi moto, ndipo zidzasungunuka ndi kutentha.

Tsiku la Ambuye

Tsono abale, za nthawi ndi nyengo yake nʼkosafunikira kuti tikulembereni, chifukwa mukudziwa bwino lomwe kuti tsiku la Ambuye lidzafika ngati mbala usiku. Pamene anthu akunena kuti, "Mtendere ndi chitetezo," chiwonongeko chidzafika pa iwo mwadzidzidzi, monga zowawa za amayi pobereka, ndipo sadzathawa.

Koma inu abale, simuli mu mdima kuti tsiku limeneli lidzakudzidzimutseni ngati mbala. Nonse ndinu ana a kuwunika ndi ana a usana. Sindife anthu a usiku kapena mdima.

Koma inu abale, simuli mu mdima kuti tsiku limeneli lidzakudzidzimutseni ngati mbala. Nonse ndinu ana a kuwunika ndi ana a usana. Sindife anthu a usiku kapena mdima. Chomwecho tsono, tisafanane ndi ena amene akugona koma tikhale maso ndi odzisunga. Pakuti amene akugona, amagona usiku, ndi amene amaledzera, amaledzera usiku. Koma popeza ndife a usana, tikhale odzisunga, titavala chikhulupiriro ndi chikondi ngati chovala pachifuwa, ndi chiyembekezo cha chipulumutso ngati chipewa. Pakuti Mulungu sanatisankhe kuti tikavutike ndi mkwiyo koma kuti tilandire chipulumutso kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu.

Destruição e renovação

O Dia do Senhor trará juízo sobre os ímpios, mas também novos céus e nova terra onde habita a justiça.

Tsiku Lalikulu la Yehova

Tsiku lalikulu la Yehova layandikira,

layandikira ndipo lifika msanga.

Tamverani! Kulira kwa pa tsiku la Yehova kudzakhala kowawa,

ngakhale munthu wolimba mtima adzalira kwambiri.

Tsiku limenelo lidzakhala la ukali,

tsiku losautsa ndi lomvetsa chisoni,

tsiku la mavuto ndi la chiwonongeko,

tsiku la mdima ndi lachisoni,

tsiku la mitambo ndi la mdima wandiweyani.

Tsiku loliza lipenga ndi la mfuwu wankhondo,

tsiku la kugwa kwa mizinda yotetezedwa

ndi nsanja za pa ngodya.

Ndidzabweretsa msautso pa anthu

ndipo adzayenda ngati anthu osaona,

chifukwa achimwira Yehova,

magazi awo adzamwazika ngati fumbi

ndi mnofu wawo ngati ndowe.

Ngakhale siliva wawo kapena golide wawo

sadzatha kuwapulumutsa

pa tsiku la ukali wa Yehova.

Dziko lonse lapansi lidzanyeka

mʼmoto wa nsanje yake

chifukwa adzakantha modzidzimutsa

onse okhala pa dziko lapansi.

Taonani, tsiku la Yehova likubwera,

tsiku lopanda chisoni, lawukali ndi lamkwiyo;

kudzasandutsa dziko kuti likhale chipululu

ndi kuwononga anthu ochimwa a mʼmenemo.

Ndinayangʼanitsitsa pamene ankatsekula chomatira chachisanu ndi chimodzi. Ndipo panachitika chivomerezi champhamvu. Dzuwa linada ngati chiguduli chopanga ndi bweya wambuzi wakuda. Mwezi wonse unafiira ngati magazi, ndipo nyenyezi zakuthambo zinagwa pa dziko lapansi ngati muja zimagwera nkhuyu zotsalira mu mtengo mphepo yamphamvu ikawomba.

Chinjoka chachikulu chija chinagwetsedwa pansi. Ichocho ndiye njoka yakalekale ija yotchedwa Mdierekezi kapena Satana, amene amasocheretsa anthu a pa dziko lonse lapansi. Chinaponyedwa pa dziko la pansi pamodzi ndi angelo ake.

"Padzakhala zizindikiro zodabwitsa pa dzuwa, mwezi ndi nyenyezi. Pa dziko lapansi, mitundu ya anthu idzakhala mʼmasautso ndipo idzathedwa nzeru pakumva mkokomo ndi mafunde a mʼnyanja. Anthu adzakomoka chifukwa cha mantha, akadzamva za zimene zikubwera pa dziko lapansi, pakuti zinthu zamlengalenga zidzagwedezeka.

Khalani tcheru nthawi zonse ndi kupemphera kuti inu mudzathe kuthawa zonse zimene zili pafupi kuchitika, ndi kuti mudzathe kuyima pamaso pa Mwana wa Munthu."

Kumwamba ndi Dziko Lapansi Zatsopano

Kenaka ndinaona kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano pakuti kumwamba koyamba ndi dziko lapansi loyamba zinapita ndipo kunalibenso nyanja ina iliyonse. Ndinaona mzinda wopatulika, Yerusalemu watsopano, ukutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu, utakonzedwa ngati mkwatibwi wovala zokongola kukonzekera mwamuna wake. Ndipo ndinamva mawu ofuwula kuchokera ku Mpando Waufumu kuti, "Taonani! Malo wokhalapo Mulungu ali pakati pa anthu, ndipo Iye adzakhala ndi anthuwo. Iwo adzakhala anthu ake ndipo Mulungu mwini adzakhala nawo nakhala Mulungu wawo. Mulungu adzapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo. Sikudzakhalanso imfa kapena kukhuza maliro kapena kulira kapena ululu popeza zakale zapita.’ "

Amene anakhala pa mpando waufumuyo anati, "Ndikulenga zinthu zonse zikhale zatsopano!" Ndipo anati, "Lemba izi, pakuti mawu awa ndi okhulupirika ndi woona."

Seja o primeiro
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-07-05_19-25-13-