Publicidade

Sinais do fim dos tempos

Por Bíblia Online

A Bíblia descreve sinais que precederão a volta de Jesus. Guerras, falsos mestres, sinais cósmicos e a pregação do evangelho a todas as nações — tudo aponta para o fim dos tempos.

Sinais proféticos

Este evangelho do Reino será pregado em todo o mundo e então virá o fim. Os sinais dos últimos tempos já se manifestam.

Ndipo uthenga wa ufumu udzalalikidwa ku dziko lonse lapansi ngati umboni kwa mitundu yonse, ndipo pomwepo chimaliziro chidzafika."

"Akadzangotha mavuto a masiku amenewo,

" dzuwa lidzadetsedwa,

ndipo mwezi sudzawala;

nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba,

ndipo mphamvu za mmwamba zidzagwedezeka.

"Pa nthawi imeneyo chizindikiro cha Mwana wa Munthu chidzaoneka mlengalenga, ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzalira. Idzaona Mwana wa Munthu akubwera ndi mitambo, mphamvu ndi ulemerero waukulu. Ndipo adzatuma angelo ake, ndi kulira kwa lipenga kwakukulu, nadzasonkhanitsa osankhidwa ake kuchokera ku mphepo zinayi, ndi kuchokera kumathero a thambo kufika mbali ina.

"Chifukwa chake yangʼanirani, popeza simudziwa tsiku lanji limene Ambuye anu adzabwera. Koma zindikirani ichi: Ngati mwini nyumba akanadziwa nthawi yanji ya usiku imene mbala imabwera, sakanagona ndipo sakanalola kuti nyumba yake ithyoledwe. Inunso tsono muyenera kukhala okonzeka, chifukwa Mwana wa Munthu adzabwera pa nthawi imene inu simukumuyembekezera.

ndi kuwaphunzitsa amvere zonse zimene ndinakulamulirani. Ndipo onani, Ine ndidzakhala pamodzi ndi inu kufikira kutha kwa dziko lapansi pano."

Tsiku ndi Ora Sizikudziwika

"Palibe amene akudziwa za tsikulo kapena nthawi, ngakhale angelo akumwamba, kapena Mwana, koma Atate wokha.

Os últimos dias

Nos últimos dias virão tempos difíceis, homens amantes de si mesmos. Mas derramarei o meu Espírito sobre toda a carne.

Zoopsa za Mʼmasiku Otsiriza

Koma dziwa izi: Mʼmasiku otsiriza kudzafika nthawi zoopsa kwambiri. Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzitama, onyada, achipongwe, osamvera makolo awo, osayamika, wopanda chiyero. Adzakhala wopanda chikondi, osakhululuka, osinjirira, osadziletsa, ankhanza, osakonda zabwino, opereka anzawo kwa adani awo, osaopa zoyipa, odzitukumula, okonda zowasangalatsa mʼmalo mokonda Mulungu. Adzakhala ndi maonekedwe achipembedzo koma mphamvu yake ndi kumayikana. Anthu amenewa uziwapewa.

" Mulungu akuti, mʼmasiku otsiriza

ndidzakhuthulira Mzimu wanga pa anthu onse.

Ana anu aamuna ndi aakazi adzanenera,

anyamata anu adzaona masomphenya,

nkhalamba zanu zidzalota maloto.

Ngakhalenso pa antchito anga aamuna ndi aakazi,

ndidzakhuthulira Mzimu wanga masiku amenewo,

ndipo iwo adzanenera.

Ndipo ndidzaonetsa zodabwitsa mlengalenga

ndi zizindikiro pa dziko lapansi pano,

ndizo magazi, moto ndi utsi watolotolo.

Dzuwa lidzadetsedwa

ndipo mwezi udzaoneka ngati magazi

lisanafike tsiku lalikulu ndi laulemerero la Ambuye.

Ndipo aliyense amene adzayitana

pa dzina la Ambuye adzapulumuka.

Tsiku la Yehova

"Ndipo patapita nthawi,

ndidzakhuthulira Mzimu wanga pa anthu onse.

Ana anu aamuna ndi ana anu aakazi adzanenera,

nkhalamba zanu zidzalota maloto,

anyamata anu adzaona masomphenya.

Ngakhalenso pa antchito anga aamuna ndi aakazi

ndidzakhuthulira Mzimu wanga masiku amenewo.

Nthawi Yotsiriza

"Pa nthawi imeneyo Mikayeli, mngelo wamkulu amene amateteza anthu a mtundu wako, adzabwera. Imeneyi idzakhala nthawi ya mavuto aakulu omwe sanaonekepo kuyambira pachiyambi cha mitundu ya anthu mpaka nthawi ikudzayo. Komatu pa nthawiyi anthu a mtundu wako, aliyense amene dzina lake lidzapezeke lolembedwa mʼbuku adzapulumutsidwa. Ambiri mwa amene akugona mʼnthaka adzadzuka: ena adzapita ku moyo wosatha, ena ku malo amanyazi ndi chilango chosatha. Amene ali anzeru mʼnjira ya chilungamo adzawala ngati kuwala kwa mlengalenga, ndipo amene alondolera ambiri ku njira yolungama, adzawala ngati nyenyezi ku nthawi zosatha.

Esperança e prontidão

O dia do Senhor virá como ladrão. Mas nós não somos das trevas — estejamos sóbrios, vigiliando e esperando.

Molingana ndi mawu a Ambuye mwini, tikukuwuzani kuti, ife amene tikanali ndi moyo, otsala mpaka kubwera kwa Ambuye, sitidzawasiya kumbuyo amene anagona kale. Pakuti Ambuye mwini adzatsika kuchokera kumwamba, ndi mfuwu waulamuliro, ndi liwu la mngelo wamkulu, ndi kulira kwa lipenga la Mulungu, ndipo akufa amene ali mwa Yesu adzauka poyamba. Kenaka, ife amene tili ndi moyo, otsalafe, tidzakwatulidwa pamodzi ndi iwo mʼmitambo kukakumana ndi Ambuye mlengalenga. Tsono ife tidzakhala ndi Ambuye mpaka muyaya. Nʼchifukwa chake tsono muzilimbikitsana ndi mawu amenewa.

Chomwecho tsono, tisafanane ndi ena amene akugona koma tikhale maso ndi odzisunga. Pakuti amene akugona, amagona usiku, ndi amene amaledzera, amaledzera usiku. Koma popeza ndife a usana, tikhale odzisunga, titavala chikhulupiriro ndi chikondi ngati chovala pachifuwa, ndi chiyembekezo cha chipulumutso ngati chipewa. Pakuti Mulungu sanatisankhe kuti tikavutike ndi mkwiyo koma kuti tilandire chipulumutso kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu.

Za Kukhala Tcheru

"Samalani, kuti mitima yanu ingalemetsedwe ndi maphwando, kuledzera ndi kudera nkhawa za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingadzakupezeni modzidzimutsa ngati msampha. Pakuti lidzafika pa onse okhala pa dziko lonse lapansi. Khalani tcheru nthawi zonse ndi kupemphera kuti inu mudzathe kuthawa zonse zimene zili pafupi kuchitika, ndi kuti mudzathe kuyima pamaso pa Mwana wa Munthu."

Koma abale okondedwa, musayiwale chinthu chimodzi ichi: Kuti pamaso pa Ambuye tsiku limodzi lili ngati zaka 1,000, ndipo zaka 1,000 zili ngati tsiku limodzi! Ambuye sazengereza kuchita zimene analonjeza, monga ena amaganizira. Iwo akukulezerani mtima, sakufuna kuti aliyense awonongeke, koma akufuna kuti aliyense alape.

Koma tsiku la Ambuye lidzafika ngati mbala. Pa tsikuli zinthu zakumwamba zidzachoka ndi phokoso lalikulu. Zinthu zonse zidzawonongedwa ndi moto, ndipo dziko lapansi ndi zonse zili mʼmenemo zidzapsa.

Popeza kuti zinthu zonse zidzawonongedwa motere, kodi inu muyenera kukhala anthu otani? Muyenera kukhala moyo wachiyero ndi opembedza Mulungu pamene mukuyembekezera tsiku la Mulungu ndi kufulumiza kufika kwake. Pa tsiku limeneli zinthu zakumwamba zidzawonongedwa ndi moto, ndipo zidzasungunuka ndi kutentha. Koma ife tikudikira kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano, zimene Mulungu analonjeza, mʼmene chilungamo chidzakhalamo.

Tamverani, ndikuwuzeni chinsinsi. Tonse sitidzagona tulo, koma tonse tidzasandulika. Zidzachitika mwadzidzidzi, mʼkamphindi kochepa, monga ngati kuphethira kwa diso, pa lipenga lotsiriza. Pakuti lipenga lidzalira, akufa adzaukitsidwa opanda chovunda, ndipo ife tidzasandulika.

Chilengedwe Chatsopano

"Taonani, ndikulenga

mlengalenga mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano.

Zinthu zakale sizidzakumbukika,

zidzayiwalika kotheratu.

Koma inu mukhale osangalala ndi okondwa mpaka muyaya

chifukwa cha zimene ndikulenga,

pakuti ndikulenga Yerusalemu kukhala malo wosangalatsa

ndipo anthu ake adzakhala achimwemwe.

Ine ndidzakondwa chifuwa cha Yerusalemu

ndipo ndidzasangalala chifukwa cha anthu anga.

Kumeneko sikudzamvekanso kulira

ndi mfuwu wodandaula.

Tsiku la Yehova

Yehova Wamphamvuzonse akuti, "Ndithu tsiku likubwera; lidzayaka ngati ngʼanjo. Anthu onse odzikuza, ndi aliyense ochita zoyipa adzapsa ngati chiputu, ndipo pa tsiku limene likubweralo adzapserera ndi moto. Sipadzatsalira muzu kapena nthambi. Koma inu amene mumaopa dzina langa, dzuwa lachilungamo lidzakutulukirani lili ndi kuwala kokuchiritsani. Ndipo inu mudzatuluka ndi kulumphalumpha ngati ana angʼombe amene atulutsidwa mʼkhola.

Kumwamba ndi Dziko Lapansi Zatsopano

Kenaka ndinaona kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano pakuti kumwamba koyamba ndi dziko lapansi loyamba zinapita ndipo kunalibenso nyanja ina iliyonse. Ndinaona mzinda wopatulika, Yerusalemu watsopano, ukutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu, utakonzedwa ngati mkwatibwi wovala zokongola kukonzekera mwamuna wake. Ndipo ndinamva mawu ofuwula kuchokera ku Mpando Waufumu kuti, "Taonani! Malo wokhalapo Mulungu ali pakati pa anthu, ndipo Iye adzakhala ndi anthuwo. Iwo adzakhala anthu ake ndipo Mulungu mwini adzakhala nawo nakhala Mulungu wawo. Mulungu adzapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo. Sikudzakhalanso imfa kapena kukhuza maliro kapena kulira kapena ululu popeza zakale zapita.’ "

Seja o primeiro
Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-29_22-07-56-