Graça
A graça de Deus é favor imerecido. Pela graça somos salvos, pela graça vivemos, pela graça somos sustentados. É o dom mais precioso de Deus — dado a quem não merece.
Salvos pela graça
Pela graça sois salvos, mediante a fé, e isto não vem de vós — é dom de Deus. Não por obras, para que ninguém se glorie.
Pakuti mwapulumutsidwa mwachisomo, kudzera mʼchikhulupiriro ndipo izi sizochokera mwa inu eni, koma ndi mphatso ya Mulungu, osati ndi ntchito, kuti wina aliyense asadzitamandire.
Koma chifukwa cha chikondi chake chachikulu pa ife, Mulungu amene ndi olemera mʼchifundo, anatipanga kukhala amoyo ndi Khristu ngakhale pamene ife tinali akufa mu zolakwa zathu. Koma tinapulumutsidwa mwachisomo.
pakuti onse anachimwa naperewera pa ulemerero wa Mulungu ndipo onse alungamitsidwa mwaulere mwa chisomo chake chifukwa cha Khristu Yesu amene anawawombola.
Koma sitingafananitse mphatso yaulereyo ndi kuchimwa kwa anthu. Pakuti ngati anthu ambiri anafa chifukwa cha kuchimwa kwa munthu mmodziyo, kuli koposa bwanji nanga chisomo cha Mulungu ndi mphatso zomwe zinabwera ndi chisomo cha munthu mmodzi, Yesu Khristu, ndi kusefukira kwa ambiri!
Choncho monga momwe tchimo linkalamulira anthu ndi kubweretsa imfa pa iwo, chomwecho kunali koyenera kuti chisomo chilamulire pobweretsa chilungamo kwa anthu, ndi kuwafikitsa ku moyo wosatha mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
Graça que capacita
A graça me basta, pois o poder se aperfeiçoa na fraqueza. Na graça, não estamos mais sob a lei, mas sob o favor de Deus.
Tchimo silidzakhalanso ndi mphamvu pa inu, chifukwa Malamulo sakulamulira moyo wanu koma chisomo.
Nʼchiyani tsono? Kodi tidzichimwa chifukwa sitikulamulidwa ndi Malamulo koma chisomo? Ayi. Mʼnjira iliyonse ayi!
Iye anatipulumutsa ndipo anatiyitanira ku moyo oyera mtima, osati chifukwa cha chilichonse chimene tinachita, koma chifukwa cha chikonzero ndi chisomo chake. Chisomo chimenechi anatipatsa ife mwa Khristu Yesu nthawi isanayambe.
Pakuti chisomo cha Mulungu chimene chimapulumutsa chaonekera kwa anthu onse. Chisomo chimatiphunzitsa kukana moyo osalemekeza Mulungu komanso zilakolako za dziko lapansi. Ndipo chimatiphunzitsa kukhala moyo odziletsa, olungama ndi opembedza Mulungu nthawi ino,
Choncho konzani mtima wanu, khalani odziretsa; khazikitsani chiyembekezo chanu kotheratu pa chisomo chimene mudzapatsidwe pamene Yesu Khristu adzaonekera.
Ndipo Mulungu wachisomo chonse, amene anakuyitanani ku ulemerero wake wamuyaya mwa Khristu, mutamva zowawa pa kanthawi, adzakukonzaninso ndi kukulimbitsani pa maziko olimba.
A graça de Deus
O Senhor é compassivo e gracioso, tardio em irar-se e grande em amor. Sua graça é nova a cada manhã.
Yehova ndi wachifundo ndi wokoma mtima,
wosakwiya msanga ndi wachikondi chochuluka.
Zoonadi, zokoma ndi chikondi chosasinthika zidzanditsata
masiku onse a moyo wanga,
ndipo ndidzakhala mʼNyumba ya Yehova
kwamuyaya.
Kukoma mtima kwa Ambuye Mulungu wathu kukhale pa ife;
tikhazikitsireni ntchito ya manja athu;
inde, khazikitsani ntchito ya manja athu.
Ndikulirira kwa Inu Yehova ndili mʼdzenje lozama;
Ambuye imvani mawu anga.
Makutu anu akhale tcheru kumva
kupempha chifundo kwanga.
" ‘Yehova akudalitse
ndi kukusunga;
Yehova awalitse nkhope yake pa iwe,
nakuchitira chisomo;
Yehova akweze nkhope yake pa iwe,
nakupatse mtendere.’ "
Komatu Yehova akufunitsitsa kuti akukomereni mtima,
iye ali wokonzeka kuti akuchitireni chifundo.
Pakuti Yehova ndi Mulungu wachilungamo.
Ndi odala onse amene amakhulupirira Iye!
Viver pela graça
A graça de nosso Senhor Jesus Cristo esteja convosco. Perdoando e confessando, experimentamos a graça restauradora.
Chisomo cha Ambuye Yesu chikhale ndi anthu onse. Ameni.
Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu chikhale ndi mzimu wako.
Tiyeni tsono tiyandikire ku mpando waufumu, wachisomo mopanda mantha, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo chotithandiza pa nthawi yeniyeni.
Koma sindilabadira konse za moyo wanga ngati kuti ndi wa mtengo wapatali kwa ine, malingana ndikatsirize ntchito yanga ndi utumiki umene Ambuye Yesu anandipatsa, ntchito yochitira umboni Uthenga Wabwino wachisomo cha Mulungu.
"Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi, kotero anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira Iye asatayike koma akhale ndi moyo wosatha.
Ngati inu mukhululukira anthu pamene akuchimwirani, Atate anu akumwamba adzakukhululukirani.
Wobisa machimo ake sadzaona mwayi,
koma aliyense amene awulula ndi kuleka machimowo, adzalandira chifundo.
Hezekiya anatumiza uthenga mʼdziko lonse la Israeli ndi ku Yuda ndiponso analemba makalata ku Efereimu ndi Manase, oyitana anthu kuti abwere ku Nyumba ya Yehova ku Yerusalemu kudzakondwerera Paska wa Yehova, Mulungu wa Israeli. Mfumu ndi akuluakulu ake pamodzi ndi anthu onse a mu Yerusalemu anagwirizana kuti akondwerere Paska pa mwezi wachiwiri. Iwo sanathe kukondwerera pa nthawi yake chifukwa si ansembe ambiri amene anadziyeretsa ndiponso anthu anali asanasonkhane mu Yerusalemu. Chikonzerochi chinaoneka kuti chinali chabwino kwa mfumu pamodzi ndi anthu onse. Iwo anagwirizana zoti alengeze mu Israeli monse kuyambira ku Beeriseba mpaka ku Dani, kuyitana anthu kuti abwere ku Yerusalemu ndi kudzakondwerera Paska wa Yehova, Mulungu wa Israeli. Si ambiri amene ankachita chikondwererochi monga momwe kunalembedwera.
Molamulidwa ndi mfumu, amithenga anapita mu Israeli yense ndi Yuda ndi makalata ochokera kwa mfumu ndi kwa akuluakulu ake, olembedwa kuti,
"Aisraeli bwererani kwa Yehova, Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Israeli, kuti abwerere kwa inu amene mwatsala, amene mwapulumuka mʼdzanja la mafumu a ku Asiriya. Musakhale ngati makolo anu ndi abale anu, amene anali osakhulupirika kwa Yehova Mulungu wa makolo awo kotero kuti anawachititsa kuti akhale chinthu chochititsa mantha, monga mukuoneramu. Musawumitse khosi monga anachitira makolo anu, Gonjerani Yehova. Bwerani ku malo opatulika, amene anawapatula kwamuyaya. Tumikirani Yehova Mulungu wanu kuti mkwiyo wake ukuchokereni. Ngati inu mubwerera kwa Yehova, pamenepo abale anu ndi ana anu adzachitiridwa chifundo ndi amene anawagwira ukapolo ndipo adzabwereranso ku dziko lino pakuti Yehova, Mulungu wanu ndi wokoma mtima ndi wachifundo. Iye sadzakufulatirani ngati inuyo mubwerera kwa Iye."
Amithenga aja anapita mzinda ndi mzinda wa ku Efereimu ndi Manase mpaka ku Zebuloni, koma anthu anawanyoza ndi kuwachita chipongwe. Komabe anthu ena a ku Aseri, Manase ndi Zebuloni anadzichepetsa ndipo anapita ku Yerusalemu. Dzanja la Mulungu linalinso pa anthu a ku Yuda, kuwapatsa mtima umodzi wochita zimene mfumu ndi akuluakulu ake analamula potsata mawu a Yehova.
Gulu lalikulu la anthu linasonkhana mu Yerusalemu kudzachita chikondwerero cha Buledi Wopanda Yisiti pa mwezi wachiwiri. Anachotsa mu Yerusalemu maguwa ofukizira lubani ndipo anakawaponya mʼchigwa cha Kidroni.
Iwo anapha mwana wankhosa wa Paska pa tsiku la 14 la mwezi wachiwiri. Ansembe ndi Alevi anachita manyazi ndipo anadziyeretsa ndi kubweretsa nsembe zopsereza ku Nyumba ya Yehova. Ndipo anakhala mʼmalo awo a nthawi zonse potsatira zolembedwa mʼmalamulo a Mose munthu wa Mulungu. Ansembe anawaza magazi amene anawapatsa Alevi. Popeza ambiri mʼgululo anali asanadziyeretse, Alevi anapha ana ankhosa a Paska a iwo amene, mwa mwambo, anali osayeretsedwa ndipo sakanatha kupereka ana ankhosa awo kwa Yehova. Ngakhale kuti ambiri mwa anthu ochokera ku Efereimu, Manase, Isakara ndi Zebuloni sanadziyeretse okha, komabe anadya Paska motsutsana ndi zimene zinalembedwa. Koma Hezekiya anawapempherera, kunena kuti, "Yehova wabwino, khululukirani aliyense amene wayika mtima wake kufunafuna Yehova, Mulungu wa makolo ake, ngakhale ali wosayeretsedwa molingana ndi malamulo a malo opatulika." Ndipo Yehova anamvera Hezekiya ndipo anachiritsa anthuwo.
Aisraeli amene anali mu Yerusalemu anachita chikondwerero cha Buledi Wopanda Yisiti kwa masiku asanu ndi awiri akusangalala kwambiri, pamene Alevi ndi ansembe amayimbira Yehova tsiku lililonse, akuyimbira zida zamatamando za Yehova.
Hezekiya anayankhula molimbikitsa Alevi onse amene anaonetsa kumvetsa bwino za kutumikira Yehova. Kwa masiku asanu ndi awiri anadya gawo lawo ndi kupereka nsembe zachiyanjano ndi kutamanda Yehova, Mulungu wa makolo awo.
Ndipo msonkhano wonse unagwirizana zopitiriza chikondwerero kwa masiku ena asanu ndi awiri. Kotero kwa masiku ena asanu ndi awiri anachita chikondwererocho mosangalala. Hezekiya mfumu ya Yuda anapereka ngʼombe zamphongo 1,000 ndi nkhosa ndi mbuzi 7,000 ku msonkhanoko ndipo akuluakulu ake anapereka ngʼombe zamphongo 1,000, nkhosa ndi mbuzi 10,000. Ansembe ambiri anadziyeretsa. Gulu lonse la ku Yuda linasangalala, pamodzi ndi ansembe ndi Alevi ndi onse amene anasonkhana ochokera ku Israeli, kuphatikizanso alendo amene anachokera ku Israeli ndi amene amakhala ku Yuda. Munali chikondwerero chachikulu mu Yerusalemu, pakuti kuyambira masiku a Solomoni mwana wa Davide mfumu ya Israeli sizinachitikepo zotere mu Yerusalemu. Ansembe ndi Alevi anayimirira kudalitsa anthu, ndipo Mulungu anawamvera pakuti pemphero lawo linafika kumwamba, malo ake oyera.