Guardar o coração
Guardar o coração é o mandamento mais urgente de Provérbios. Sobre tudo o que se deve guardar, guarda o teu coração, porque dele procedem as fontes da vida.
Sobre tudo, guarda o coração
O coração é a nascente de tudo — pensamentos, desejos, decisões. Guardá-lo é proteger toda a vida espiritual e emocional.
Ndipotu mtima wako uziwuyangʼanira bwino ndithu
pakuti ndiwo magwero a moyo.
Mwana wanga, undikhulupirire
ndipo maso ako apenyetsetse njira zanga.
Mwana wanga, usayiwale malangizo anga,
mtima wako usunge malamulo anga.
Ukatero zaka za moyo wako zidzachuluka
ndipo udzakhala pa mtendere.
Munthu wabwino amatulutsa zinthu zabwino zosungidwa mu mtima mwake, koma munthu oyipa amatulutsa zinthu zoyipa zosungidwa mu mtima mwake. Pakamwa pake pamayankhula zimene zadzaza mu mtima mwake.
Coração puro e renovado
Cria em mim um coração puro, ó Deus. Os puros de coração verão a Deus — e o Espírito renova nosso interior.
Mulenge mʼkati mwanga mtima woyera Inu Mulungu
ndi kukonzanso mzimu wokhazikika mwa ine.
Odala ndi amene ali oyera mtima,
chifukwa adzaona Mulungu.
Santhuleni, Inu Mulungu ndipo mudziwe mtima wanga;
Yeseni ndipo mudziwe zolingalira zanga.
Onani ngati muli mayendedwe aliwonse oyipa mwa ine,
ndipo munditsogolere mʼnjira yanu yamuyaya.
Patseni mayeso, Inu Yehova ndipo ndiyeseni,
santhulani mtima wanga ndi maganizo anga;
pakuti chikondi chanu chili pamaso panga nthawi zonse,
ndipo ndimayenda mʼchoonadi chanu nthawi zonse.
Ngakhale Inu mutafufuza mtima wanga ndi kundisanthula usiku,
ngakhale mutandiyesa, simudzapeza kanthu;
Ine ndatsimikiza kuti pakamwa panga sipadzachimwa.
Kunena za ntchito za anthu,
monga mwa mawu a pakamwa panu,
Ine ndadzisunga ndekha
posatsata njira zachiwawa.
Mayendedwe anga akhazikika pa njira zanu;
mapazi anga sanaterereke.
Mtima wanga ndi wokhazikika, Inu Mulungu
mtima wanga ndi wokhazikika.
Ndidzayimba nyimbo, nyimbo yake yamatamando.
Guardar com a Palavra
Não vos conformeis com este mundo. A Palavra de Deus guardada no coração nos protege do pecado e nos direciona.
Musafanizidwenso ndi makhalidwe a dziko lino koma musandulike pokonzanso maganizo anu. Ndipo mudzadziwa ndi kuzindikira chifuniro chabwino cha Mulungu chomwe ndi chokondweretsa ndi changwiro.
Uziwerenga Buku la Malamuloli, uzilingalira zolembedwa mʼmenemo usana ndi usiku, kuti uchite zonse zimene zinalembedwamo. Ukamatero udzapeza bwino ndi kupambana.
Ndimakufunafunani ndi mtima wanga wonse;
musalole kuti ndisochere kuchoka pa malamulo anu.
Ndasunga mawu anu mu mtima mwanga
kuti ndisakuchimwireni.
Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse. Malamulo amene ndakupatsani lero ayenera kukhala mu mtima mwanu.
iye anawawuza kuti, "Muwasunge bwino mu mtima mwanu, mawu onse amene lero lino ndikukuwuzani kuti mudzawuze ana anu, kuti adzamvere mosamalitsa mawu onse a malamulo amenewa.
Vigilância e paz
A paz de Deus guarda nossos corações em Cristo Jesus. Chegai-vos a Deus, purificai os corações — e Ele estará convosco.
Musade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa china chilichonse, mwa pemphero ndi chidandaulo pamodzi ndi chiyamiko, perekani zopempha zanu kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu, umene upambana nzeru zonse udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Sendezani kufupi ndi Mulungu ndipo Iye adzasendeza kwa inu. Sambani mʼmanja mwanu, inu anthu ochimwa. Yeretsani mitima yanu, inu anthu okayikira.
Inunso mukhale owugwira mtima ndi osasinthika chifukwa Ambuye ali pafupi kubwera.
Tsono popeza munaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, ikani mitima yanu pa zinthu za kumwamba, kumene Khristu akukhala ku dzanja lamanja la Mulungu.