Publicidade

Homem

Por Bíblia Online

A Bíblia fala sobre o homem como criação de Deus — feito à sua imagem e semelhança, mas também frágil, mortal e necessitado de redenção.

Criado à imagem de Deus

Deus criou o homem à sua imagem. Mas pelo pecado, o homem caiu e passou a depender da graça para ser restaurado.

Zitatha izi Mulungu anati, "Tipange munthu mʼchifanizo chathu, mofanana ndi ife kuti alamulire nsomba za mʼnyanja, mbalame zamlengalenga, nyama zonse zoweta ndi zonse zokwawa za pa dziko lapansi ndi zamoyo zonse zakutchire."

Ndipo Mulungu analenga munthu mʼchifanizo chake.

Anawalengadi mʼchifanizo cha Mulungu;

analenga iwo, mwamuna ndi mkazi.

Kenaka munthu uja ndi mkazi wake anamva mtswatswa wa Yehova Mulungu akuyendayenda mʼmundamo madzulo a tsikulo, ndipo iwo anabisala pamaso pa Yehova Mulungu pakati pa mitengo ya mʼmundamo.

Imfa Kudzera mwa Adamu, Moyo Kudzera mwa Yesu

Choncho monga momwe tchimo linalowa mʼdziko lapansi kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzera mu tchimo, mʼnjirayi imfa inafika kwa anthu onse pakuti onse anachimwa.

Kwalembedwa kuti, "Munthu woyamba Adamu anakhala wamoyo," Adamu wotsiriza anakhala wopatsa moyo. Zauzimu sizinabwere koyambirira, koma zachilengedwe, pambuyo pake zauzimu. Munthu woyamba anali wa dziko lapansi, wochokera mʼnthaka koma munthu wachiwiri anali wochokera kumwamba. Monga analili munthu wa dziko lapansi, momwemonso anthu onse amene ndi a dziko lapansi. Ndipo monga alili munthu wakumwamba, momwemonso anthu onse amene ndi akumwamba. Ndipo monga momwe tinabadwa ofanana ndi munthu wa dziko lapansi uja, momwemonso tidzakhala ofanana ndi munthu wakumwamba.

Fragilidade humana

O homem nascido de mulher é de poucos dias e cheio de inquietação. Deus conhece nossa fragilidade e cuida de nós.

"Munthu wobadwa mwa amayi

amakhala masiku owerengeka ndipo ndi odzaza ndi mavuto okhaokha.

Kodi munthu angathe kukhala wolungama kupambana Mulungu?

Kodi munthu angathe kukhala wangwiro kupambana Mlengi wake?

"Kodi munthu nʼchiyani kuti muzimuganizira chotere,

kuti muzisamala zochita zake,

Koma palipo pena pamene wina anachitira umboni kuti,

"Kodi munthu ndani kuti muzimukumbukira,

kapena mwana wa munthu kuti muzimusamalira?

Mayendedwe a munthu amawalamulira ndi Yehova,

tsono munthu angadziwe bwanji njira yake?

Renovação e chamado

Despojados do velho homem e revestidos do novo, somos chamados a buscar a justiça, a piedade e o amor.

Inu munaphunzitsidwa molingana ndi moyo wanu wakale, kuchotsa umunthu wakale, umene ukupitirira kuwonongeka ndi zilakolako zachinyengo; kuti mukonzedwe mwatsopano mʼmitima mwanu; ndi kuti muvale umunthu watsopano, wolengedwa kuti ufanane ndi Mulungu mu chilungamo chenicheni ndi chiyero.

pothetsa mʼthupi lake lamulo pamodzi ndi zolamulira zake ndi malangizo. Cholinga chake chinali chakuti alenge mwa Iye mwini, munthu mmodzi watsopano kuchokera kwa abwino, motero nʼkupanga mtendere,

Malangizo Otsiriza kwa Timoteyo

Koma iwe, munthu wa Mulungu, thawa zinthu zonsezi. Tsatira chilungamo, moyo wolemekeza Mulungu, chikhulupiriro, chikondi, kupirira ndi kufatsa.

Pamene ndinali mwana ndinkayankhula ngati mwana, ndinkaganiza ngati mwana, ndinkalingalira ngati mwana. Koma nditakula, zonse zachibwana ndinazisiya.

Pakuti mayendedwe onse a munthu Yehova amawaona,

ndipo Iye amapenyetsetsa njira zake zonse.

Zolinga za mu mtima ndi za munthu,

koma kwa Yehova ndiye kumachokera yankho.

A confiança errada

Maldito o homem que confia no homem. O homem de duplo ânimo é instável em todos os seus caminhos.

Yehova akuti,

"Ndi wotembereredwa munthu amene amadalira munthu mnzake,

amene amatsamira pa munthu mnzake kuti amuthandize

pamene mtima wake wafulatira Yehova.

Munthu wotere asayembekezere kulandira kalikonse kuchokera kwa Ambuye. Iyeyu ndi munthu wa mitima iwiri, wosakhazikika pa zimene akuchita.

Malangizo kwa Amayi Amasiye, Akulu Ampingo ndi Akapolo

Usadzudzule munthu wachikulire mokalipa, koma umuchenjeze ngati abambo ako. Achinyamata uwatenge ngati abale ako.

Seja o primeiro
Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-29_22-07-56-