Publicidade

Jovens

Por Bíblia Online

Deus tem planos maravilhosos para os jovens. A Bíblia os convida a consagrar a juventude ao Senhor, crescer em sabedoria e ser exemplo para todos em fé, palavra, conduta e amor.

Ninguém despreze a tua mocidade

Paulo exortou Timóteo: sê exemplo dos fiéis na palavra, no procedimento, no amor, no espírito, na fé e na pureza.

Usalole kuti wina akupeputse chifukwa ndiwe wachinyamata, koma khala chitsanzo kwa okhulupirira pa mayankhulidwe, pa makhalidwe, pa chikondi, pa chikhulupiriro ndi pa kuyera mtima.

Momwemonso, uwalimbikitse amuna achichepere kuti akhale odziletsa.

Ana ndi Makolo Awo

Inu ana, mverani makolo anu mwa Ambuye, pakuti zimenezi ndi zoyenera. "Lemekeza abambo ndi amayi ako." Limeneli ndi lamulo loyamba lokhala ndi lonjezo. Ngati ulemekeza abambo ako ndi amayi ako, "zinthu zidzakuyendera bwino ndipo udzasangalala ndi moyo wautali pa dziko lapansi."

Ana ndi Makolo Awo

Inu ana, mverani makolo anu mwa Ambuye, pakuti zimenezi ndi zoyenera. "Lemekeza abambo ndi amayi ako." Limeneli ndi lamulo loyamba lokhala ndi lonjezo.

Lembrar do Criador na juventude

Lembra-te do teu Criador nos dias da tua mocidade. A sabedoria ganha cedo produz frutos duradouros na vida inteira.

Uzikumbukira mlengi wako

masiku a unyamata wako,

masiku oyipa asanafike,

nthawi isanafike pamene udzanena kuti,

"Izi sizikundikondweretsa."

Uzikumbukira mlengi wako

masiku a unyamata wako,

masiku oyipa asanafike,

nthawi isanafike pamene udzanena kuti,

"Izi sizikundikondweretsa."

Nthawi ya ukalamba wako, dzuwa ndi kuwala,

mwezi ndi nyenyezi zidzada.

Mitambo idzabweranso mvula itagwa.

Nthawi imene manja ako adzanjenjemera,

miyendo yako idzafowoka,

pamene mano ako adzalephera kutafuna chifukwa ndi owerengeka,

ndipo maso ako adzayamba kuchita chidima.

Kondwera mnyamata iwe, pamene ukanali wamngʼono,

ndipo mtima wako usangalale pa nthawi ya unyamata wako.

Tsatira zimene mtima wako ukufuna,

ndiponso zimene maso ako akuona,

koma dziwa kuti pa zinthu zonsezo

Mulungu adzakuweruza.

Choncho uchotse zokusautsa mu mtima mwako,

upewe zokupweteka mʼthupi mwako,

pakuti unyamata ndi ubwana ndi zopandapake.

Kutukuka Nʼkopandapake

Wachinyamata wosauka koma wanzeru aposa mfumu yokalamba koma yopusa imene simvanso malangizo.

Força e promessa

Os jovens renovam suas forças quando esperam no Senhor. Deus levanta jovens com visões e sonhos para transformar o mundo.

Ngakhale achinyamata amalefuka ndi kufowoka,

ndipo achinyamata amapunthwa ndi kugwa;

koma iwo amene amakhulupirira Yehova

adzalandira mphamvu zatsopano.

Adzawuluka ngati chiwombankhanga;

adzathamanga koma sadzalefuka,

adzayenda koma sadzatopa konse.

Tsiku la Yehova

"Ndipo patapita nthawi,

ndidzakhuthulira Mzimu wanga pa anthu onse.

Ana anu aamuna ndi ana anu aakazi adzanenera,

nkhalamba zanu zidzalota maloto,

anyamata anu adzaona masomphenya.

Ngakhalenso pa antchito anga aamuna ndi aakazi

ndidzakhuthulira Mzimu wanga masiku amenewo.

Kwa anyamata anayiwa Mulungu anapereka chidziwitso ndi kuzindikira bwino mitundu yonse ya zolembedwa ndi za maphunziro. Ndipo Danieli ankatanthauzira masomphenya ndi maloto a mitundu yonse.

Ndipo kumapeto kwa masiku amene mfumu inayika kuti adzaonetse anyamatawa ku nyumba yake, mkulu wa nduna za mfumu uja anawapereka iwo kwa Nebukadinezara. Mfumu inayankhula nawo, ndipo panalibe wofanana ndi Danieli; Hananiya Misaeli ndi Azariya; Choncho analowa ndi kukhala otumikira mfumu.

Ulemerero wa achinyamata uli mu mphamvu zawo,

imvi ndi ulemerero wa anthu okalamba.

Ngakhale mwana amadziwika ndi zochita zake,

ngati zochita zake zili zoyera ndi zoyenera.

Guardar o caminho

Como purificará o jovem seu caminho? Guardando-o segundo a tua Palavra. A Escritura na juventude guarda do pecado a vida inteira.

Kodi mnyamata angathe bwanji kuyeretsa mayendedwe ake?

Akawasamala potsata mawu anu.

Ndasunga mawu anu mu mtima mwanga

kuti ndisakuchimwireni.

Pakuti Inu mwakhala chiyembekezo changa, Inu Ambuye Wamphamvuzonse,

chilimbikitso changa kuyambira ndili mwana.

Inu anyamata ndi anamwali,

inu nkhalamba ndi ana omwe.

Onsewo atamande dzina la Yehova

pakuti dzina lake lokha ndi lolemekezeka;

ulemerero wake ndi woopsa pa dziko lapansi pano ndi kumwamba komwe.

Mawu Oyamba: Cholinga ndi Mutu

Iyi ndi miyambi ya Solomoni mwana wa Davide, mfumu ya Israeli:

Ndi yothandiza kuti munthu adziwe nzeru ndi malangizo;

kuti amvetse mawu a matanthauzo ozama;

kuti alandire malangizo othandiza kuti achite zinthu mwanzeru,

akhale wangwiro, wachilungamo ndiponso wosakondera.

Ndi yothandiza munthu wamba kuti aphunzire nzeru za kuchenjera,

achinyamata kudziwa zinthu bwino ndi kulingalira.

Tamvera mwana wanga, ndipo ukhale wanzeru,

mtima wako uwuyendetse mʼnjira yabwino.

Usakhale pakati pa anthu amene amaledzera

kapena pakati pa anthu amene amadya nyama mwadyera.

Paja anthu oledzera ndi adyera amadzakhala amphawi

ndipo aulesi adzavala sanza.

Mvera abambo ako amene anakubala,

usanyoze amayi ako pamene akalamba.

Coragem e vocação

Deus chamou jovens como Jeremias e Josué para grandes missões. A juventude não é desculpa — é oportunidade de servir poderosamente.

Ine ndinati, "Haa! Ambuye Yehova, ine sinditha kuyankhula; popeza ndikanali wamngʼono."

Koma Yehova anandiwuza kuti, "Usanene kuti, Ndikanali wamngʼonopopeza udzapita kwa munthu aliyense kumene ndidzakutuma ndi kunena chilichonse chimene ndidzakulamulira. Usawaope, pakuti Ine ndili nawe, ndipo ndidzakupulumutsa," akutero Yehova.

Pakuti Ine ndikudziwa zimene ndinakukonzerani," akutero Yehova, "ndimalingalira zabwino zokhazokha za inu osati zoyipa, ayi. Ndimalingalira zinthu zokupatsani chiyembekezo chenicheni pa za mʼtsogolo. Nthawi imeneyo mudzandiyitana, ndi kunditama mopemba ndipo ndidzakumverani. Mudzandifunafuna ndipo mudzandipeza. Mukadzandifuna ndi mtima wanu wonse mudzandipezadi," akutero Yehova, "ndipo ndidzakubwezerani zabwino zanu. Ndidzakusonkhanitsani kuchokera ku mayiko onse ndi kumalo konse kumene munali," akutero Yehova, "ndipo ndidzakubweretsani kumalo kumene munali ndisanakuchotseni kukupititsani ku ukapolo."

Ukhale wamphamvu ndi wolimba mtima kwambiri. Usamale ndithu kuti umvere malamulo onse amene mtumiki wanga Mose anakupatsa. Usachoke pa malamulo anga ndipo kulikonse kumene udzapite udzapambana. Uziwerenga Buku la Malamuloli, uzilingalira zolembedwa mʼmenemo usana ndi usiku, kuti uchite zonse zimene zinalembedwamo. Ukamatero udzapeza bwino ndi kupambana. Paja ndinakulamula kuti ukhale wamphamvu ndi wolimba mtima. Choncho usamachite mantha kapena kutaya mtima popeza Ine Yehova Mulungu wako ndidzakhala nawe kulikonse kumene udzapite."

Momwemonso, inu anyamata gonjerani amene ndi akulu. Inu nonse mukhale odzichepetsa kuti mutumikirane, chifukwa,

"Mulungu amatsutsana nawo odzikuza,

koma amapereka chisomo kwa odzichepetsa."

Choncho, mudzichepetse pamaso pa Mulungu wamphamvu, kuti pa nthawi yake adzakukwezeni.

Ana okondedwa, ndikukulemberani

chifukwa mumawadziwa Atate.

Abambo, ndikukulemberani

chifukwa munamudziwa Iye amene analipo kuyambira pachiyambi.

Inu anyamata, ndikukulemberani

chifukwa ndinu amphamvu.

Mawu a Mulungu amakhala mwa inu

ndipo mumamugonjetsa woyipayo.

Tiyeni tikhale moyenera monga nthawi ya masana, osati mʼmagulu amadyerero, achiwerewere ndi kuledzera, mʼmadama ndi zonyansa komanso osati mʼmagawano ndi nsanje.

Nʼkwabwino kuti munthu asenze goli

pamene ali wamngʼono.

Seja o primeiro
Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-29_22-07-56-