Publicidade

Juízo

Por Bíblia Online

O juízo de Deus é manifestação de sua justiça e soberania. Ele julga o mundo, julga as nações e julga cada coração com perfeita equidade e misericórdia.

O juízo de Deus

Deus é juiz justo que prova os corações. Seu juízo é verdadeiro e alcança toda obra, secreta ou pública.

Pakuti Mulungu adzaweruza zochita zonse,

kuphatikizanso zinthu zonse zobisika,

kaya zabwino kapena zoyipa.

Pakuti monga Atate amaukitsa akufa nawapatsa moyo, momwemonso Mwana amapereka moyo kwa amene Iye akufuna. Komanso, Atate saweruza aliyense koma wapereka kwa Mwana ulamuliro woweruzawo, kuti aliyense alemekeze Mwanayo monga momwe amalemekezera Atate. Munthu amene salemekeza Mwana salemekezanso Atate amene anamutuma Mwanayo.

"Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene amamva mawu anga ndi kukhulupirira Iye amene ananditumiza Ine, ali ndi moyo wosatha ndipo sadzaweruzidwa. Iye wachoka mu imfa ndipo walowa mʼmoyo. Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti nthawi ikubwera ndipo yafika kale tsopano, pamene akufa adzamva mawu a Mwana wa Mulungu ndipo iwo amene amva adzakhala ndi moyo. Pakuti monga Atate ali gwero la moyo, momwemonso anapereka mphamvu zopereka moyo mwa Mwana. Ndipo wamupatsa Iye ulamuliro woweruza chifukwa ndi Mwana wa Munthu.

"Musadabwe ndi zimenezi. Pakuti nthawi ikubwera pamene onse amene ali mʼmanda adzamva mawu ake ndi kutuluka. Iwo amene anachita zabwino adzauka ndi kupita ku moyo wosatha ndipo amene anachita zoyipa adzauka ndi kupita ku chilango chamuyaya. Pakuti sindingathe kuchita kena kalikonse pa ndekha. Ine ndimaweruza molingana ndi zomwe Mulungu wandiwuza ndipo kuweruza kwanga ndi kolungama. Ine sindifuna kudzikondweretsa ndekha koma Iye amene anandituma.

Maumboni Onena za Yesu

"Ngati ndidzichitira umboni ndekha, umboni wanga si woona.

Komatu ndakuwuzani zoona. Ine ndikuti kuli bwino kwa inu kuti ndichoke. Ngati sindichoka, Nkhosweyo sidzabwera kwa inu, koma ngati Ine ndipita, ndidzamutumiza kwa inu. Iye akabwera, adzatsutsa dziko lapansi za uchimo, zachilungamo ndi zachiweruzo. Za uchimo, chifukwa anthu sakhulupirira Ine.

Yesu anati, "Mawu awa abwera chifukwa cha inu osati chifukwa cha Ine. Ino tsopano ndi nthawi yachiweruzo pa dziko lapansi; tsopano olamulira wa dziko lapansi adzathamangitsidwa. Koma Ine, akadzandipachika pa dziko lapansi, ndidzakokera anthu onse kwa Ine."

Pamenepo munthuyo anati, "Ambuye, ndikukhulupirira," ndipo anamulambira Iye.

Yesu anati, "Ndinabwera pansi pano kudzaweruza kuti osaona aone ndi openya asaone."

Prestando contas

Cada um prestará contas de si mesmo a Deus. O juízo começa pela casa de Deus e depois alcança os que não obedecem ao evangelho.

Ofowoka ndi Amphamvu

Mulandire amene ndi ofowoka mʼchikhulupiriro, osatsutsana naye pa maganizo ake. Chikhulupiriro cha munthu wina chimamulola kudya china chilichonse koma munthu wina, amene chikhulupiriro chake ndi chofowoka, amangodya zamasamba zokha. Munthu amene amadya chilichonse sayenera kunyoza amene satero, ndipo munthu amene samadya chilichonse asaweruze munthu amene amatero, pakuti Mulungu anamulandira. Kodi ndiwe ndani kuti uweruze wantchito wamwini? Mbuye wake yekha ndiye aweruze ngati iye wakhoza kapena walephera pa ntchito yake. Ndipo adzakhoza popeza kuti Mbuye wake angathe kumukhozetsa.

Choncho tsopano, aliyense wa ife adzafotokoza yekha kwa Mulungu.

Motero, tiyeni tisiye kuweruzana wina ndi mnzake. Mʼmalo mwake, tsimikizani mʼmaganizo anu kuti musayike chokhumudwitsa kapena chotchinga mʼnjira ya mʼbale wanu. Monga mmodzi amene ndili mwa Ambuye Yesu, ndine wotsimikiza mtima kuti palibe chakudya chimene pachokha ndi chodetsedwa. Koma ngati wina atenga china chake kukhala chodetsedwa, kwa iyeyo ndi chodetsedwa.

Pakuti nthawi yafika kuti chiweruzo chiyambe mʼnyumba ya Mulungu, ndipo ngati chiyamba ndi ife nanga podzafika kwa osamvera Uthenga Wabwino wa Mulungu, chidzakhala chotani?

Chomwecho musaweruze nthawi yoweruza isanakwane. Dikirani mpaka Ambuye atabwera. Iye adzaonetsa poyera zimene zabisika mu mdima ndipo adzaonetsa maganizo a mʼmitima ya anthu. Pa nthawi imeneyo aliyense adzalandira kwa Mulungu chiyamiko.

Pakuti momwe inu muweruzira ena, inunso mudzaweruzidwa chimodzimodzi, muyeso umene muyesera ena inunso mudzayesedwa ndi womwewo.

"Chifukwa chiyani iwe uyangʼana kachitsotso ka mʼdiso la mʼbale wako koma susamalira chimtengo chili mʼdiso mwako? Kodi unganene bwanji kwa mʼbale wako kuti, Ndikuchotse kachitsotso mʼdiso mwako,pamene nthawi zonse chimtengo uli nacho mʼdiso mwako?

Justiça e redenção

O juízo de Deus é também redenção. Ele livrou Israel do Egito com juízos e salva os arrependidos pela cruz de Cristo.

"Nʼchifukwa chake nena kwa Aisraeli kuti, Ine ndine Yehova, ndipo ndidzakutulutsani mʼgoli la Aigupto. Ndidzakumasulani mu ukapolo, ndidzakuwombolani ndi dzanja langa lotambasuka ndi kuchita ntchito zachiweruzo.

"Usiku umenewo Ine ndidzadutsa mʼdziko la Igupto ndipo ndidzapha chilichonse choyamba kubadwa kuyambira mwana wa munthu aliyense mpaka ana aziweto. Ndidzalanganso milungu yonse ya Igupto. Ine ndine Yehova.

Motsutsana ndi Inu, Inu nokha, ndachimwa

ndipo ndachita zoyipa pamaso panu,

Kotero kuti inu mwapezeka kuti ndinu wolungama

pamene muyankhula ndi pamene muweruza.

Ziyoni akumva ndipo akukondwera,

midzi ya Yuda ikusangalala

chifukwa cha maweruzo anu Yehova.

Kenaka anaphwanya ndi nkhwangwa ndi akasemasema awo

zonse zimene tinapachika.

Iwo anatentha malo anu opatulika mpaka kuwagwetsa pansi;

anadetsa malo okhalamo dzina lanu.

Babuloni Wagwa, Haleluya!

Zitatha izi, ndinamva chimene chinamveka ngati phokoso la gulu lalikulu mmwamba likufuwula kuti,

"Haleluya!

Chipulumutso ndi ulemerero ndi mphamvu ndi za Mulungu wathu,

pakuti chiweruzo chake ndi choona ndi cha chilungamo.

Iye waweruza mkazi wadama wotchuka uja

amene anayipitsa dziko lonse lapansi ndi zigololo zake.

Iye wabwezera pa mkaziyo magazi a atumiki ake."

Ndipo anafuwulanso kuti,

"Haleluya!

Utsi wochokera kwa mkazi wadamayo udzakwera kumwamba mpaka muyaya."

Seja o primeiro
Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-29_22-07-56-