Ler a Bíblia
Ler a Bíblia é essencial para a vida cristã. A Escritura é lâmpada para os pés, alimento para a alma e espada do Espírito. O cristão que lê a Bíblia é transformado pela Palavra.
A importância de ler
Meditar na Palavra dia e noite traz prosperidade e bom sucesso. Ler a Bíblia ilumina o entendimento e fortalece a fé.
Uziwerenga Buku la Malamuloli, uzilingalira zolembedwa mʼmenemo usana ndi usiku, kuti uchite zonse zimene zinalembedwamo. Ukamatero udzapeza bwino ndi kupambana.
Mawu anu ndi nyale ya kumapazi kwanga
ndi kuwunika kwa pa njira yanga.
Mawu anu akamaphunzitsidwa amapereka kuwunika;
ngakhale anthu wamba amamvetsetsa.
Ndithu, ine ndimakonda malamulo anu!
Ndimalingaliramo tsiku lonse.
Malamulo anu amachititsa kuti ndikhale wanzeru kuposa adani anga,
popeza malamulowo ali ndi ine nthawi zonse.
Ndimamvetsa zinthu kwambiri kuposa aphunzitsi anga onse
popeza ndimalingalira umboni wanu.
Kodi mnyamata angathe bwanji kuyeretsa mayendedwe ake?
Akawasamala potsata mawu anu.
Ndimakufunafunani ndi mtima wanga wonse;
musalole kuti ndisochere kuchoka pa malamulo anu.
Ndasunga mawu anu mu mtima mwanga
kuti ndisakuchimwireni.
A Escritura é inspirada
Toda a Escritura é útil para ensinar, corrigir e instruir em justiça. Examine as Escrituras — nelas encontramos a vida eterna.
Malemba onse anawalembetsa ndi Mulungu, ndipo othandiza pophunzitsa, podzudzula, pokonza cholakwika ndi polangiza za chilungamo kuti munthu wa Mulungu akonzekere bwino lomwe kugwira ntchito iliyonse yabwino.
Inu mumasanthula malemba chifukwa mumaganiza kuti mʼmalembamo muli moyo wosatha. Awa ndi malemba amene akundichitira umboni.
Pakuti zilizonse zimene zinalembedwa kale zinalembedwa kuti zitiphunzitse ife. Malembawo amatilimbikitsa kupirira kuti tikhale ndi chiyembekezo.
Ngodala munthu amene awerenga mawu oneneratu zamʼtsogolo ndi iwo amene amamva ndi kusunga zolembedwa mʼbukuli pakuti nthawi yayandikira.
Mpaka nditabwera, udzipereke powerenga mawu a Mulungu kwa anthu, kulalikira ndi kuphunzitsa.
Estudar com diligência
Os bereanos eram mais nobres porque examinavam as Escrituras diariamente. O estudo dedicado da Bíblia produz maturidade espiritual.
Tsopano anthu a ku Bereya anali akhalidwe labwino kusiyana ndi Atesalonika, pakuti iwo analandira mawu ndi chidwi chachikulu ndipo ankasanthula Malemba tsiku ndi tsiku kuti aone ngati zimene ankanena Paulozo zinali zoona.
Popeza Ezara anadzipereka kuwerenga ndi kusunga malamulo a Yehova, iye anafunitsitsa kuphunzitsa Aisraeli malamulo ndi malangizo a Mulungu.
Iwo anawerenga buku la malamulo a Mulungu momveka bwino ndi kutanthauzira mawuwo kuti anthu amvetse bwino zowerengedwazo.
Yesu anawafunsa kuti, "Kodi si pamenepa nanga pomwe mumalakwira chifukwa simukudziwa malemba kapena mphamvu za Mulungu?
Malamulo amene ndakupatsani lero ayenera kukhala mu mtima mwanu. Muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu. Muzikamba za malamulowa pamene muli mʼnyumba zanu, pamene mukuyenda mʼnjira, pamene mukugona ndi pamene mukudzuka. Muwamange ngati zizindikiro pa manja anu ndi kuwamangirira pa zipumi zanu.
Ubwino Wanzeru
Mwana wanga, ngati ulandira mawu anga
ndi kusunga malamulo anga mu mtima mwako,
ndiponso kutchera khutu lako ku nzeru
ndi kuyikapo mtima pa kumvetsa zinthu;
ngati upempha kuti uzindikire zinthu
inde kupempha ndi mtima wonse kuti ukhale womvetsa zinthu,
ngati ufunafuna nzeruyo ngati siliva
ndi kuyisakasaka ngati chuma chobisika,
ndiye udzamvetsa bwino tanthauzo la kuopa Yehova;
ndipo udzapezanso tanthauzo la kumudziwa Yehova.
Pakuti Yehova ndiye amapereka nzeru,
ndipo mʼkamwa mwake mumachokera chidziwitso ndi kumvetsa zinthu.