Pular para o conteúdo
Publicidade

Língua

Por Bíblia Online

A língua tem poder de vida e de morte. A Bíblia compara a língua ao leme de um navio e à faísca que incendeia uma floresta. Dominar a língua é prova de maturidade espiritual.

O poder da língua

A morte e a vida estão no poder da língua. Quem a domina é varão perfeito, capaz de controlar todo o corpo.

Mawu ako angathe kukuphetsa kapena kukukhalitsa moyo.

Wokonda kuyankhulayankhula adzadya zipatso zake.

Tonsefe timapunthwa mʼnjira zambiri. Ngati wina salakwa poyankhula, ameneyo ndi munthu wangwiro, wodziwa kuyangʼanira bwino thupi lake lonse.

Tikayika tizitsulo mʼkamwa mwa akavalo kuti atimvere, timatha kuwongolera thupi lake lonse. Taonani sitima zapamadzi. Ngakhale ndi zazikulu kwambiri ndipo zimakankhidwa ndi mphepo yamphamvu, zimawongoleredwa ndi tsigiro lalingʼono kulikonse kumene woyendetsayo akufuna kupita. Momwemonso, lilime ndi kachiwalo kakangʼono ka thupi koma limadzitama kuti nʼkuchita zikuluzikulu. Tangoganizirani za nkhalango yayikulu imene ingapse ndi kalawi kamoto koyamba mochepa. Lilime nalonso ndi moto, dziko la zoyipa pakati pa ziwalo za thupi. Limawononga munthu yense wathunthu. Limayika zonse za moyo wake pa moto, ndipo moto wake ndi wochokera ku gehena.

Mitundu yonse ya nyama, ya mbalame, ya zokwawa ndi ya zolengedwa za mʼnyanja, zikuwetedwa ndipo munthu wakhala akuziweta, koma palibe munthu amene angaweta lilime. Lilime ndipo silitha kupuma, ndi lodzaza ndi ululu wakupha.

Ndi lilime lomwelo timatamanda Ambuye ndi Atate athu, komanso ndi lilime lomwelo timalalatira anthu, amene anapangidwa mʼchifanizo cha Mulungu. Mʼkamwa momwemo mutuluka matamando ndi kulalata. Abale anga, zisamatero ayi. Kodi madzi abwino ndi a mchere angatuluke pa kasupe mmodzi? Abale anga, kodi mtengo wa mkuyu nʼkubala mphesa, kapena mtengo wampesa nʼkubala nkhuyu? Kasupe wa madzi a mchere sangatulutsenso madzi abwino.

Palavras sábias

A língua branda quebra até ossos. A palavra certa no tempo certo é como maçãs de ouro em salvas de prata.

Kupirira ndiye kumagonjetsa mfumu,

ndipo kufewa mʼkamwa kutha kumafatsitsa munthu wowuma mtima.

Munthu woyankhula mosasamala mawu ake amalasa ngati lupanga,

koma mawu a munthu wanzeru amachiritsa.

Mawu woona amakhala mpaka muyaya

koma mawu abodza sakhalitsa.

Mawu akachuluka zolakwa sizisowa,

koma amene amasunga pakamwa pake ndi wanzeru.

Ngakhale chitsiru chimakhala ngati chanzeru chikakhala chete;

ndipo chikatseka pakamwa chimakhala ngati munthu wochenjera.

Disciplinar a fala

Quem guarda a boca e a língua guarda a sua alma de angústias. A religião sem controle da língua é vã.

Ngati wina amadziyesa ngati ndi wachipembedzo, koma chonsecho saletsa lilime lake, amadzinyenga yekha ndipo chipembedzo chakecho ndi cha chabechabe.

Ndinati, "Ndidzasamalira njira zanga

ndipo ndidzasunga lilime langa kuti ndisachimwe;

ndidzatseka pakamwa panga ndi chitsekerero

nthawi yonse imene woyipa ali pamaso panga."

Aliyense wa inu amene amakonda moyo wake

ndi kukhumba kuti aone masiku abwino ambiri,

asunge lilime lake ku zoyipa

ndi milomo yake kuti isayankhule zonama.

Pakamwa pa munthu wolungama pamayankhula za nzeru,

ndipo lilime lake limayankhula zolungama.

Lamulo la Mulungu wake lili mu mtima mwake;

mapazi ake saterereka.

Pakamwa panga padzayankhula za chilungamo chanu

ndi za matamando anu tsiku lonse.

Mawu asanatuluke pa lilime langa

mumawadziwa bwinobwino, Inu Yehova.

Pulumutseni Yehova ku milomo yabodza,

ndi kwa anthu achinyengo.

Inu Yehova tsekani milomo yonse yachinyengo

ndi pakamwa paliponse podzikuza.

Pakamwa pamene pamati, "Ife tidzapambana ndi kuyankhula kwathu;

pakamwapa ndi pathupathu, tsono mbuye wathu ndani?"

Sokonezani maganizo a oyipa, Inu Ambuye, tsutsani mawu awo;

pakuti ine ndikuona chiwawa ndi mkangano mu mzinda.

Toda língua confessará

Ao nome de Jesus todo joelho se dobrará e toda língua confessará que Jesus Cristo é Senhor, para glória de Deus Pai.

Choncho Mulungu anamukweza Iye kukhala wapamwamba kwambiri,

ndipo anamupatsa dzina loposa dzina lina lililonse

kuti pakumva dzina la Yesu, bondo lililonse limugwadire,

kumwamba ndi pa dziko lapansi ndi pansi pa dziko,

ndipo lilime lililonse livomereze kuti Yesu Khristu ndi Ambuye

kuchitira ulemu Mulungu Atate.

Kupambana kwa Chikondi

Ngakhale nditamayankhula mʼmalilime a anthu ndi a angelo, koma ngati ndilibe chikondi, ndili ngati chinganga chaphokoso kapena ngati chitsulo chosokosera.

Ine ndikukuwuzani kuti pa tsiku la chiweruziro munthu adzazengedwa mlandu chifukwa cha mawu aliwonse wopanda pake amene anayankhula. Pakuti ndi mawu anu mudzapezeka osalakwa ndiponso ndi mawu anu mudzapezeka olakwa."

Koma Yehova anatsika kudzaona mzindawo ndi nsanja imene anthu aja ankayimanga. Yehova anati, "Anthuwa ndi amodzi, ndipo ali ndi chiyankhulo chimodzi. Izi akuchitazi nʼchiyambi chabe cha zomwe akufuna kukwaniritsa kuchita. Tiyeni titsikireko tikasokoneze chiyankhulo chawo kuti asamamvetsetsane."

Choncho Yehova anabalalitsa anthu aja pa dziko lonse lapansi ndipo analeka kumanga mzindawo. Nʼchifukwa chake mzindawo unatchedwa Babeli, popeza Yehova anasokoneza chiyankhulo cha anthu onse. Powachotsa kumeneko, Yehova anawabalalitsira pa dziko lonse lapansi.

Seja o primeiro

Este artigo te tocou? Faça uma oração!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.