Pular para o conteúdo
Publicidade

Livramento

Por Bíblia Online

Deus é o grande Libertador. Através da Bíblia, vemos Deus livrando seu povo de inimigos, de perigos e da morte. Quem clama ao Senhor, Ele ouve e liberta.

Deus ouve e livra

Clamaram ao Senhor na sua tribulação, e Ele os livrou das suas angústias. O Senhor é refúgio e a salvação dos que nele confiam.

Olungama amafuwula, ndipo Yehova amawamva;

Iye amawalanditsa ku mavuto awo onse.

Adzandiyitana, ndipo ndidzamuyankha;

ndidzakhala naye pa mavuto,

ndidzamupulumutsa ndi kumulemekeza.

Ndidzanena za Yehova, "Iye ndiye pothawira panga ndi linga langa,

Mulungu wanga amene ndimadalira."

Ndithu, Iye adzakupulumutsa ku msampha wa mlenje

ndi ku mliri woopsa;

Mulungu wathu ndi Mulungu amene amapulumutsa;

Ambuye Wamphamvuzonse ndiye amene amatipulumutsa ku imfa.

Pakuti mwawombola moyo wanga ku imfa

ndi mapazi anga kuti ndingagwe,

kuti ndiyende pamaso pa Mulungu

mʼkuwala kwa moyo.

Landitsani anthu ofowoka ndi osowa;

apulumutseni mʼdzanja la anthu oyipa.

Pulumutseni Yehova;

Bwerani msanga Yehova kudzandithandiza.

Choncho aliyense okhulupirika apemphere kwa Inuyo

pomwe mukupezeka;

ndithu pamene madzi amphamvu auka,

sadzamupeza.

Livramento poderoso

Deus livrou Daniel dos leões, os jovens hebreus do fogo e Israel do Egito. Seu braço não é curto para salvar.

Ngati tiponyedwa mʼngʼanjo ya moto, Mulungu amene timamutumikira akhoza kutipulumutsa ku ngʼanjo yamotoyo, ndipo adzatilanditsa mʼdzanja lanu mfumu. Koma ngakhale Mulungu wathu atapanda kutipulumutsa, tikufuna mudziwe inu mfumu, kuti sitidzatumikira milungu yanu kapena kupembedza fano la golide limene munaliyimika."

Anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu,

adani anga amene anali amphamvu kuposa ine.

Koma awiriwo anayima pakati pa mundawo. Iwo anawuteteza, nakantha Afilistiwo ndipo Yehova anawapambanitsa koposa.

Ngati muwazunza ndipo iwo nʼkulirira kwa Ine, ndidzamva kulira kwawo.

"Ine ndine Mulungu kuyambira nthawi yamakedzana, ndipo ndidzakhalabe Mulungu ku nthawi zonse.

Palibe amene angathe kuthawa mʼmanja mwanga,

ndipo chimene ndachita palibe angathe kuchisintha."

Redenção e restauração

Todo aquele que invocar o nome do Senhor será salvo. Deus livra do pecado, da morte e de todo mal aqueles que se humilham diante dele.

pakuti, "Aliyense amene adzayitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka."

Ndipo tsopano ukudikira chiyani? Dzuka ndi kutama dzina la Ambuye mopemba, ubatizidwe ndi kuchotsa machimo ako.

Ndipo mukudikira Mwana wake kuchokera kumwamba, Yesu, amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa. Iyeyo amatipulumutsa ku mkwiyo umene ukubwera.

ngati anthu anga, amene amatchedwa ndi dzina langa adzichepetsa ndi kupemphera ndi kufunafuna nkhope yanga, nasiya njira zawo zoyipa, pamenepo Ine ndidzamva kumwamba ndipo ndidzakhululuka tchimo lawo ndi kuchiritsa dziko lawo.

Ndipo Ine ndidzachita chilichonse chimene inu mudzapempha mʼdzina langa kuti Atate alemekezedwe mwa Mwana. Ngati mudzapempha kanthu kalikonse mʼdzina langa, Ine ndidzachita.

Lonjezo la Mzimu Woyera

"Ngati mundikonda Ine, sungani malamulo anga. Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani Nkhoswe ina kuti izikhala nanu nthawi zonse.

Ife tikudziwa kuti Mulungu samvera wochimwa. Iye amamvera munthu woopa Mulungu amene amachita chifuniro chake.

Sendezani kufupi ndi Mulungu ndipo Iye adzasendeza kwa inu. Sambani mʼmanja mwanu, inu anthu ochimwa. Yeretsani mitima yanu, inu anthu okayikira.

Tsono ngati inu woyipitsitsa mumadziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanga Atate anu akumwamba sadzapereka mphatso zabwino kwa iwo amene amupempha?

Akapemphera kwa Mulungu, iyeyo adzalandiridwa.

Mulungu adzamulandira mwa chimwemwe

ndipo adzamubwezeretsa pamalo ake oyamba.

Seja o primeiro

Este artigo te tocou? Faça uma oração!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.